Gawoli mwachidule

Transcription

Gawoli mwachidule
Bukuli linalembedwa ndi chithandizo chochokera kwa anthu a ku America kudzera m’mabungwe
a President’s Emergency Plan for AIDS Relief (PEPFAR) ndi a U.S. Agency for International
Development (USAID) kupyolera mu Contract nambala GHH-I-00-07-00032-00, USAID | Project
SEARCH, Task Order 01. Zolembedwa mkatimu ndi za Go Girls! Initiative ndipo sikuti zikuonetsera
kwenikweni maganizo a PEPFAR kapena boma la United States.
3
4
Zamkatimu
Zothokoza.......................................................................................................................................................................7
Mau Otsogolera............................................................................................................................................................9
Gawo 1: Tiyeni Ophunzira! - Tiyembekezere zotani?............................................................................... 11
Gawo 2: Mphamvu ndi Zolinga Zanga ........................................................................................................... 23
Gawo 3: Mubokosi langa, kutuluka m’bokosi langa ............................................................................... 26
Gawo 4: Maubwenzi abwino .............................................................................................................................. 28
Gawo 5: Yankhulani! Kulumikizana ndi ena................................................................................................. 32
Zowerenga Aphunzitsi 1: Kuyankhula zomwe tikufuna ndi momwe tikumvera ................................ 36
Gawo 6:Akulu monga othandiza ...................................................................................................................... 37
Gawo 7: Thupi langa likusintha- Ndiri bwinobwino? Mbali yoyamba............................................ 41
Zowerenga Aphunzitsi 2: Mmene tingayankhulirane
ndi achinyamata nkhani zokhuza kugonana.................................................................................................... 43
Gawo 8: Thupi langa likusintha-Ndiri bwinobwino? Mbali yachiwiri ............................................. 48
Zowerenga Zowonjezera 1: Njira za momwe tingathandizilane kuti tikhale ozidalira ..................... 51
Gawo 9: Kodi mimba?............................................................................................................................................. 52
Zowerenga Zowonjezera 2: Ziwalo zoberekera , Msambo ndi Mimba.................................................... 55
Gawo10: Thumba la katengedwe ka HIV....................................................................................................... 63
Zowerenga Aphunzitsi 3: Mgwiriza omwe ulipo pakati pa HIV ndi
ndi Matenda opatsirana pogonana ndi zinthu za m’thumba la katengedwe ka HIV......................... 65
Gawo11:Kupanga zisankho zabwino.............................................................................................................. 68
Gawo12: Ndipange chiyani ndi zilakolakozi?............................................................................................. 65
Gawo13: Ndine wokonzeka kuchita zogonana?........................................................................................ 72
Gawo14: Kunena kuti “ayi” ku zogonana..................................................................................................... 75
Gawo15: Sindinkafuna kuchita zogonana................................................................................................... 78
Zowerenga Aphunzitsi 4: Mmene tingachitile ndi achinyamata omwe
anachitilidwapo nkhaza zogwirilidwa kapena kukamizidwa kuchita zogonana................................. 82
5
Gawo16: Kukambirana ndi akuluakulu za kugonana............................................................................. 89
Gawo17: Kugonana ndi akuluakulu................................................................................................................ 93
Gawo18: Mfundo zanga, ndalama zanga...................................................................................................... 98
Gawo19: Kugonana inu nokha .......................................................................................................................101
Gawo20: Zotsatira za mowa...............................................................................................................................104
Gawo21: Kugwira ntchito kulumikizana kuti tidziteteze tokha......................................................108
Zowerenga Aphunzitsi 5: Zitsanzo zowonjezera za kulumikizana..........................................................112
Gawo22: kulemekeza mbiri yathu, kuteteza tsogolo lathu ..............................................................114
Gawo23: Ndiri pachiopsezo?............................................................................................................................116
Gawo24: Kukonzekera za cholinga changa...............................................................................................120
Ndandanda wa matanthauzo...........................................................................................................................122
Mafomu owunika mmene ntchito yayendera ..........................................................................................127
6
Zothokoza
Bukuli linalembedwa ndi Maryce Ramsey komanso Judy Palmore. Maluso ena anaperekedwa ndi
Joanna Skinner, Patricia Poppe, Jane Brown, Carol Underwood, Jessica Fehringer, Tinaye Mmusi,
Maipelo Madibelo, Assana Magombo, Dorothy Nyasulu, Enni Panizzo ndi mamembala ena a gulu
la PEPFAR Gender Technical Working Group komanso ndi magulu PEPFAR am’maiko a Botswana,
Malawi ndi Mozambique.
Tikufuna tithokoze mabungwe angapo omwe ntchito ya zolemba zawo yagwiritsidwa ntchito
bukuli. Mabungwe ake ndi monga:
International HIV/AIDS Alliance, www.aidsalliance.org
• “Sexuality and Life-Skills: Participatory Activities on Sexual and Reproductive Health with
Young People”
• “Our Future Sexuality and Life Skills Education for Young People, Grades 4-5”
• “Our Future: Sexuality and Life Skills Education for Young People, Grades 6-7”
• “Our Future: sexuality and life skills education for young people Grades 8-9”
United States Agency for International Development, www.usaid.gov
• “Doorways I: Student Life Skills Manual on School-Related Gender-Based Violence (SRGBV),”
unadapted version, February 2006.
• “Doorways II: Counsellor Training Manual on School-Related Gender-Based Violence (SRGBV),”
unadapted version, November, 2006.
Family Care International, Inc., www.familycareintl.org
• Pictures on male and female reproductive systems, menstrual process and pregnancy from
“Healthy Women, Healthy Mothers, An Information Guide.” 1995, 2nd Ed., Arkutu, A.
EngenderHealth, www.engenderhealth.org
• Male reproductive system text adapted from Introduction to Men’s Reproductive Health
Services—Revised Edition: Participant Handbook. 2008. New York.
PATH. www.path.org, Population Council, www.popcouncil.org and Kenya Adolescent
Reproductive Health Project (KARHP)
• Female reproductive system, pregnancy, and menstruation text adapted from “Tuko Pamoja:
Adolescent Reproductive Health and Life Skills Curriculum.” 2006.
Campaign for our Children, Inc. www.cfoc.org
• “Talking to Your Parents about Sex,” in “Teen Guide” Found at: http://www.cfoc.org/index.php/
teen-guide/talking-to-your-parents-about-sex/
Namibian German Reproductive Health Project, [email protected]
• Pictures of puberty development from pages 7 and 9 of their booklet “The questions adolescents
ask most frequently about Growing Up and their answers”, Vol. 1
Cover photo by Patrick Coleman/CCP, Courtesy of Photoshare.
7
8
Mau Otsogolera
Mwalandiridwa ku Tiyeni Ophunzira! Buku la aphunzitsi la Maluso okhudzana ndi umoyo wa
Atsikana ndi Anyamata m’sukulu. Bukuli lalembedwa kuti lithandize aphunzitsi pophunzitsa
ophunzira maluso osiyanasiyana omwe angawathandize iwo kudziteteza ku mliri wa HIV/Edzi.
Mbiri yokhudzana ndi Tiyeni Atsikana!
Tiyeni Atsikana! Buku la Aphunzitsi la Maluso okhudzana ndi umoyo wa Atsikana ndi
Anyamata m’sukulu linalembedwa ndi gulu la Tiyeni Atsikana lomwe limadziwikanso ngati
Go Girls! Initiative (GGI). Gulu la GGI lomwe limathandizidwa ndi bungwe la U.S. Agency for
International Development kudzera ku bungwe la U.S. President’s Emergency Plan for AIDS
Relief, inali pulojekiti ya zaka zitatu (2007-2010) yomwe cholinga chake kunali kufuna kuchepetsa
kufalikira kwa kachilombo ka HIV pakati pa atsikana omwe ali pachiopsezo kwambiri a msinkhu
wa pakati pa zaka 10 mpaka 17 m’maiko a Botswana, Malawi, ndi Mozambique.
Ntchito yomwe inagwiridwa ndi a Johns Hopkins Bloomberg School of Public Health/Center for
Communication Programs (CCP), Tiyeni Atsikana! Inayesetsa kulimbikitsa ma pulogalamu okhudza
amuna komanso akazi dziko lonse pokhazikitsa njira zatsopano komanso kukweza njira zomwe
zinalipo kale zochepetsera chiopsezo cha atsikana ku mliri wa HIV. Pofuna kugawana ndi dziko
lonse zotsatira za ntchito ya Tiyeni Atsikana! Mabuku othandizira kuphatikizapo buku lothandiza
kupima chiopsezo cha atsikana ndi zipangizo zothandizira ma pulogalamu, kuphatikizapo bukulizilipo zaulere kuti zithandize anthu omwe amakhazikitsa mfundo komanso mapulogalamu
osiyanasiyana kuti the kulimbikitsa atsikana ndi Madera kukhala amphamvu padziko lonse.
Kuti muthe kupeza zipangizo zones za Tiyeni Atsikana, funsani a U.S. Agency for International
Development pa adiresi ya intaneti ya [email protected] kapena pezani a CCP
pa www.jhuccp.org.
Tanthauzo la atsikana osatetezedwa
Atsikana omwe ndi “osatetezedwa” ku kachilombo ka HIV ndi amene amakhala pa
chiopsezo chachikulu chotenga kachilomboka kusiyana ndi anzawo. Atsikana ali
pachiopsezo chachikuluwa ndi monga ana amasiye, osiyira sukulu panjira, opanda
maubwenzi abwino, nzika za maiko ena zomwe zangofika kumene kapena zopanda
chilolezo ndi omwe amakhala m’moyo wa umphawi.Zinthu zimenezi kuphatikizapo
zina monga kuzindikira, kudzikhulupirira, kumwa mowa, mphamvu ya maubwenzi,
ndi ubwenzi ndi makolo nthawi zambiri zimalowana powaika atsikana kukhala
pachiopsezo chachikulu chotenga kachilombo ka HIV.
9
Buku la aphunzitsi la Tiyeni Ophunzira! Maluso okhudzana ndi umoyo wa Atsikana ndi
anyamata m’sukulu limazindikira kuti anyamata ndi atsikana, abambo ndi amayi onse ali
chiopsezo ku mliri wa HIV/EDZI. Komabe, kafukufuku amaonetsa kuti atsikana ali pa chiopsezo
kwambiri ku mliri wa HIV/EDZI. Mwachitsanzo:
99 Atsikana ali ndi mwayi wochepa wopita ku sukulu komanso kumaliza maphunziro awo;
99 Atsikana ali ndi mwayi wochepa wodziwa zambiri zokhudza za HIV/EDZI;
99 Atsikana ali ndi mwayi wochepa wopezera chuma kusiyana ndi anyamata zomwe
zimawapangitsa kuti azisinthanitsa matupi awo ndi ndalama;
99 Maudindo omwe atsikana ali nawo pachikhalidwe amawalepheretsa iwo kukhala
ochangamuka;
99 Atsikana amakwatiwa ndikuyamba mchitidwe wogonana akadali achichepere kusiyana ndi
anyamata; ndi,
99 Atsikana ndi omwe amakhala opalamulidwa kwambiri pa nkhani ya nkhanza zokhunzana ndi
kugonana kusiyana ndi anyamata.
Mapulogalamu ambiri okhudzana ndi kapewedwe ka HIV kawirikawiri saganizira za mfundozi
komanso zina zomwe zimapangitsa atsikana kukhala pa chiopsezo ku HIV ndipo sakhala ndi
chidwi chapadera choti atsikanawonso atengepo mbali. Tiyeni Atsikana! Inali ndi chiyembekezo
chosintha zimenezi poyika chidwi pazosoweka za atsikana otha msinkhu.
Kugwiritsa ntchito mabuku a Tiyeni Atsikana!
Ndandanda wa mabuku a Tiyeni Atsikana analembedwa kuti athandizire pulogalamu
yomwe cholinga chake ndi kuchepetsa chiopsezo cha atsikana ku mliri wa HIV/EDZI
pofikira Madera, sukulu, makolo, anyamata ndi atsikana achichepere pogwiritsa
ntchito njira zomwe anthu amatenga nawo mbali powazindikiritsa, Madera kuchitapo
kanthu, komanso zida zokwezera maluso osiyanasiyana. Mabukuwa ayesedwapo kaye
m’maiko atatu omwe agwiritsiridwe ntchito a - Malawi, Mozambique ndi Botswana –
ndikusinthidwa potengera mayankho ochokera kwa Otsogolera komanso ophunzira
mu dziko lirilonse la maiko atatuwa.
Mabuku asanu a Tiyeni Atsikana mu ndandanda wawo ndi awa:
• Tiyeni Atsikana! Maluso okhudzana ndi umoyo wa Atsikana ndi anyamata m’sukulu: buku
la Mphunzitsi – bukuli limathandiza aphunzitsi pophunzitsa maluso osiyanasiyana okhudzana
ndi umoyo womwe angathandize ophunzirawo kuti athe kudziteteza ku mliri wa HIV/EDZI.
• Tiyeni Aphunzitsi! Kukonza malo oteteza ndi olimbikitsa atsikana m’sukulu: buku
lophunzitsira la aphunzitsi ndi atsogoleri ena pa sukulu – bukuli limathandiza atsogoleri
a pasukulu kumvetseta ndi kulimbikitsa maudindo awo monga oteteza atsikana omwe
ali pachiopsezo komanso ngati othandizira kusintha m’sukulu mwawo polimbikitsa njira
zophunzitsira zosasiyanitsa amuna ndi akazi ndi kuthetsa makhalidwe onse omwe amayika
atsikana pa chiopsezo chotenga kachilombo ka HIV.
10
• Tiyeni Mabanja! Kukweza maluso anthu akuluakulu kuti athe kulankhulana ndi
achinyamata: Buku lophunzitsira – bukuli limathandiza makolo, opereka chithandizo, ndi
achikulire onse omwe ali okhudzidwa kuti athe kuyankhulana ndi achinyamata. Cholinga
cha pulogalamuyi ndi kulimbikitsa maluso a achikulire pa kayankhulidwe, kukhala zitsanzo
zabwino komanso ubale wawo ndi achinyamata.
• Tiyeni Madera! Buku lolimbikitsa Madera kuchitapo kanthu pochepetsa chiopsezo cha
atsikana ku mliri wa HIV/EDZI – bukuli ndi mlozo wa tsatanetsatane wolimbikitsa Atsogoleri
omwe amalimbikitsa Madera kuthana ndi chiopszo cha atsikana ku mliri wa HIV/EDZI.
• Tiyeni Atsikana! Maluso okhudzana ndi umoyo wa atsikana m’madera- buku lophunzitsira
– bukuli lalembedwa kuti lirimbikitse maluso a umoyo wa atsikana a zaka za pakati pa 13
mpaka 17 omwe sali pasukulu kapena ali m’malo osatetezedwa.
Pa m’ndandanda wa mabukuwa palinso mabuku awiri omwe ndi milozo pa 1) Kulimbikitsa njira
zopezera chuma kwa atsikana omwe ali pachiopsezo ndi mabanja awo komanso 2) Kukweza
chithandizo cha m’Madera kwa atsikana omwe ali pachiopsezo kudzera pa wailesi.
Mndandanda wa mabuku a Tiyeni Atsikana! Unakhazikitsidwa pofuna kuthana ndi nkhani
zosiyanasiyana zomwe zimapangitsa atsikana kukhala pa chiopsezo ku mliri wa HIV kotero kuti
mapulogalamu onsewa ndi oyenera kuchitidwa pamodzi. Komabe, ngati ndalama zoyendetsera
mapulogalamu onsewa nthawi imodzi palibe, mapulogalamuwanso angathe kuchitidwa paokha
paokha.
Kugwiritsa Ntchito bukhuli
1. Tiyeni Ophunzira! Mlozo wamaluso okhudzana ndi moyo wa achinyamata
omwe ali mu sukulu uli ndi magawo okwana makumi awiri ndi mphambu
zinayi(24). Magawowa ayalidwa motere:
•
•
•
•
•
•
•
•
•
•
Mutu wagawo
Kufotokozera za gawolo
Zolinga za phunziro
Nthawi
Zipangizo
Kukonzekera kwa wotsogolera
Zochitikachitika ndi malangizo akachitidwe kake pa ndime iliyonse.
Kuomba mkota wa chigawo
Phunziro Lotsatila
“Zoyenera kudziwa mphunzitsi/mtsogoleri” Pena paliponse pamene pakuyenera kutero
m’chigawomo.
No final do Manual existe um glossário com as definições das palavras e dos conceitos nele
utilizados.
11
2. Zipangizo ndi uthenga wofunika
1. Mapentopeni ndi matchati kapena choko ndi bolodi ndi zofunika mmagawo ambiri.
Ngati zinthuzi palibe pezani njira zina zoyenera.
2. Zolemba zoonjezera ndi zofunikanso mmagawo ena. Zolemba zoonjezerazi
zaphatikizidwa kumapeto kwa gawo. Ngati simungapange zolemba zoonjezera
zokwanira anthu onse otenga mbali, yesetsani kupanga zochepa zomwe anthu otenga
mbali angagawane.
3. Buku la Tiyeni Atsikana! Uthenga m’zithunzi lingakhale lothandiza kwa wotsogolera
maphunzirowa ndipo liyenera kukhala pafupi kuti lithe kuthandizira pamene
pakuyenerera.
4. Maphunzirowa asanayambike, mphunzitsi akhale kuti akudziwa za:
•
•
•
Kulera
Kayezetsedwe ndi kulangizidwe pa mliri wa HIV
Mmene amayi angapewere kupatsira kachilombo ka HIV kwa mwana
wamngono
5. Ayitaneni achipatala komanso mabungwe okhudzana ndi za kulera komanso kachilombo
ka HIV kuti adzakhale ngati ”wophunzitsa Ongobwera” kuti athandizire pa maphunziro.
Dziwani Ophunzira Anu
Kutengera ndi gulu la anthu omwe mukugwira nawo ntchito, mangafunike kusintha njira
yotsogolerera gawo. Kwa gulu la anthu odziwa pang’ono kulemba ndi kuwerenga mungafunike
kujambula zithunzi zambiri komanso kugwiritsa ntchito zizindikiro kwambiri polemba pa tchati
kapena pa bolodi.Gwiritsani ntchito mawu omveka bwino. Onetsetsani kuti malangizo amveka
bwino musanayambe zochitika ziri zonse. Musafunse mafunso oposa atatu kumapeto kwa
phunziro lironse.
Kukula kwa gulu
Gulu labwino ndi lomwe liri ndi ophunzira a pakati 15 ndi 20. Tiyeni Atsikana! Limagwiritsa
ntchito njira zophunzitsira zomwe ophunzira amatenga nawo mbali komanso zimalimbikitsa
kukambirana. Pokhala ndi gulu laling’ono, ophunzira onse adzakhala ndi mwayi wotenga nawo
mbali mu pulogalamuyo ndipo wotsogolera maphunzirowa adzakwaniritsa kumaliza zokambirana
zonse mu Ola limodzi ndi theka.
Khalani okonzeka ku zovuta ndi zolepheretsa
Phunziro lirilonse lingathe kubweretsa zovuta kapena zolepheretsa. Njira yabwinno yogonjetsera
vutazi ndi kukhala okonzekera. Dziwani zomwe mukuyenera kukaphunzitsa ndipo yesezerani
kuphunzitsa ndi mnzanu kapena mphunzitsi wina musanakaphunzitse.
12
Phunzitsani magawo a mu bukuli motsata ndondomeko
Magawo a mu bukuli analembedwa kuti gawo lirilonse lidziwonjezera ndi kupitiriza pomwe
phunziro la m’mbuyo lalekezera, choncho ndi bwino kuti magawowa adziphunzitsidwa
mwandondomeko kuyambira gawo 1 kukafika gawo 24.
3. Tiyeni Atsikana! Njira zophunzitsira
Zomwe ndamva, ndimaiwala.
Zomwe ndaona, ndimakumbukira.
Zomwe ndachita, ndimazimvetsetsa.
Magawo a m’bukuli amagwiritsa ntchito njira zophunzitsira zomwe ophunzira amatenga nawo
mbali pa zokambirana monga kukambirana m’magulu, kulingalira, timasewero, tintchito ta
m’magulu, masewera ophunzitsa, zisudzo, kuzenga nkhani zosiyanasiyana ndi kukamba tinthano.
Ophunzira adzakhala ndi mwayi wogwiritsa ntchito maluso omwe angopeza kumene monga
kutha kulumikizana ndi anzawo komanso kupanga zisankho zoyenera.
Ubwino wa njira zophunzitsira zomwe ophunzira amatenga nawo mbali ndi:
•
•
•
•
Kukweza luso lotha kuganiza mozama;
Ophunzira ali ndi mwayi wonse wokumbukira zomwe aphunzira ndikutha kufotokozera ena;
Kulimbikitsa chikoka pa phunzirolo; komanso
Kukweza luso lotha kulumikizana ndi anthu ena.
Njira zomwe ophunzira amatenga nawo mbali
Kulingalira: Kulingalira ndi njira yomwe pamakhala kufukufuku wa mfundo ndipo ndi yabwino
kuyambira zokambirana. Pamene njira ikugwiritsidwa ntchito, munthu aliyense sayenera kutsutsa
zomwe wina wanena. Yankho lirilonse limangolembedwa papepala kapena pabolodi kuti gulu
lonse lithe kuona. Njirayi imalimbikitsa ophunzira kukweza kaganizidwe kawo pa mutu womwe
apatsidwa ndipo amalingalira za mutuwo pa ngodya zosiyanasiyana.
Kukambirana m’magulu: Kukambirana m’magulu kumabweretsa mayankho osiyanasiyana
kuchokera kwa ophunzira pa mutu womwe waperekedwa ndipo zimamuthandiza wotsogolera
kapena mphunzitsi kuzindikira zina zomwe samazidziwa kapena zomwe analakwitsa. Kupambana
kwa njirayi kumadalira luso la wotsogolera kapena mphunzitsi pa kagwiritsidwe ntchito ka
mafunso omwe amafuna mayankho ofotokozera, osati mayankho ake ongoti “eya” kapena “ayi”.
Mafunso amenewa amathandiza kutulutsa zakukhosi pa mutu womwe ukukambidwa kapena pa
chochitika.
1. “Kodi mwaphunzirapo chiyani pa chochitikachi?” ndi funso lomwe limafuna yankho lofotokoza
chifukwa limamufunsa munthu kuti afotokoze maganizo ake. ”Kodi chochitikachi chakukhudza
bwanji?” ndi chitsanzo chinanso cha funso lofuna yankho lofotokozera.
13
2. “Waphunzirapo china chilichonse?” si funso lofunika yankho lofotokozera, chifukwa ophunzira
akhoza kungoyankha kuti “eya” kapena “ayi”. “Zikumveka?” ndi chitsanzo chinanso cha funso
lomwe silifuna yankho lofotokoza.
Timasewero: Kuchita timasewero zimathandiza ophunzira kukhala ndi mwayi wochita zinthu
zomwe zimachitikadi mmoyo popanda kukumanadi ndi mavuto enieni omwe munthu amakumana
nawo. Ndikofunika kuti ophunzira akamakonza timaseweroti tizikhala nkhani yowona osati
zongopeka.
Malamulo okhudzana ndi kapangidwe ka timaseweroti ndi awa::
1.
2.
3.
4.
5.
Kambiranani zokhudzana ndi sewerolo ngati gulu
Gwirizanani za mmene sewerolo liyendere
Gwirizanani za omwe atenge mbali ndi zomwe ati achite, aliyense apange
Yesezerani
Pangani sewerolo ku gulu lonse
Zochangamutsa-Musanayambe : zokambirana tsiku lilonse, atsogoleri akhonza kufuna
kuwaphunzitsa ophunzira kasewero komwe kangawachangamutse ophunzira, kuti akhale
omasuka, asangalare komanso athe kulumikizana wina ndi mzake. Ophunzira nawo nthawi zambiri
amakhala ndi zitsanzo zabwino za masewero ochangamutsa. Mungathe kufunsa ophunzira
mmodzi kapena awiri mu gawo lirilonse atsogolere zochitika zachidule zochangamutsa ndi
kulipanga gulu kukhala lochangamauka tsiku lonse.
Zitsanzo za zochitika zochangamutsa:
1. Mtsogoleri ndi ndani?
• Ophunzira ayimirire kapena kukhala atapanga bwalo. Munthu mmodzi wodzipereka
atuluka panja.
• Akatuluka, gulu lotsalira lija lisankha mtsogoleri.
• Mtsogoleri yemwe ali mbali imodzi ya bwalo apanga zinthu zingapo (kuomba mmanja,
kugwedeza mwendo, kuseka) zomwe gulu lonse liti liwonerere.
• Wodzipereka uja ayitanidwa kuchokera panja ndipo auzidwa kuti aiyimirire kapena
kukhala mkati mwa bwalo. Iye afunsidwa kuloteza yemwe gulu lija linamusankha
kukhala mtsogoleri.
• Gululo limuteteza mtsogoleri uja kuti asagwidwe posamuyang’ana kapena posaonetsera
kuti akutsatira iyeyo.
• Wodzipereka akakwanitsa kuloza mtsogoleri (patha kutenga kanthawi) iyeyo akhoza
kukhalano mtsogoleri ndipo mtsogoleri woyamba uja asanduka wodzipereka.
• Bwerezani mpaka pomwe mutopere.
2. Kuyesezera kunama
• Funsani ophunzira kupanga bwalo.
• Mtsogoleri ayamba ndi kuyesezera kupanga chinthu.
• AKafunsidwa ndi yemwe ali naye kumanja kwake kuti “ukupanga chiyani?”, mtsogoleriyo
atchula chinthu china chosiyana kwambiri ndi chomwe amayesezera chija. Mwachitsanzo,
mtsogoleri ayesezera kusambira koma ayankha kuti “ndikutsuka tsitsi langa”.
14
•
•
Munthu yemwe ali kumanja kwa mtsogoleriyo naye ayesezera zomwe mtsogoleri uja
ANANENA kuti akuchita (kutsuka tsitsi). Munthu yemwe ali kumanja kwa iyeyu afunsa
kuti “ukupanga chiyani?” ndipo ayankha chinthu china chosiyana kwambiri ndi chomwe
amachitacho.
Zungulurani bwalo lonse mpaka aliyense atapangako.
3. Kupanga mvula
• Funsani ophunzira kupanga bwalo.
• Funsani ophunzira kutsatira zomwe mtsogoleri awalamule kuchita. Muwauze kuti
munthu aliyense adzitsatira malamulolo pamene mukuzungulira bwalo lonse
kuyambira kumanja kumapita kumanzere. (Malamulowo ndi: ikani manja pamodzi ndi
kuwatikita; kodolani zala; menyani ndi manja anu mumtunda mwa ntchafu; pondani
pansi mwamphamvu ngati perete).
• Kumbutsani ophunzira kuyamba lamulo lina pokhapokha yemwe ali kumanja kwawo
wayamba.
• Mtsogoleri ayamba ndi kuyika manja ake pamodzi ndikumawatikita. Mtsogoleri achite
lamulo limeneli mpaka aliyense bwalomo atayamba kutsanzira zomwezo. Zikatero,
mtsogoleri ayambitse lamulo lina. Kuchita lamulolo mosalekeza kungatulutse phokoso
la ngati chiphaliwali.
• Bwerezani mozungulira bwalolo kangapo.
• Pamene mtsogoleri waona kuti seweroli lafika kumapeto angoika manja ake mbali
osachita chilichonse. Zimenezi zitsanziridwa ndi aliyense mu bwalomo monga momwe
amachitira poyamba paja mpaka pakhala bata.
4. Maluso ndi mfundo zofunikira zokhudza otsogolera magawo a mu Tiyeni
Atsikana!
Mpoyenera kuti mtsogoleri kapena mphunzitsi akhale wamkazi woti:
•
•
•
Anaphunzirapo za kaphunzitsidwe kogwiritsa ntchito njira zomwe ophunzira amatenga nawo
mbali pa zokambirana;
Akudziwa za nkhani zokhudza kusasiyana pakati pa amuna ndi akazi; ndi,
Kutha kudzindikira yekha za mfundo za moyo wake pa nkhani zokhudza achinyamata; ndi
zofunikira kuti atsogoleri azigwira ntchito ndi achinyamatawa atawavomereza mmene
anyamata alili osati mmene akufunira kuti iwo akhalire.
Nzeru kwa Aphunzitsi
M’munsimu muli mfundo zina zomwe zingakuthandizeni inu monga otsogolera kuti mupange
ntchito yapamwamba.
Mphunzitsi wabwino:
• Amaona ophunzira ake ngati akatswiri omwe ali ndi nzeru komanso maluso oti angapereke
osati kudziwona ngati iye yekha ndiye wodziwa kwambiri kuposa aliyense m’chipindamo;
• Amalimbikitsa aliyense kuphunzira kuchoka kwa mzake, ndipo amadzitenga iye kukhala
wongotsogolera chabe osati kuwatenga ophunzira kukhala ngati zitini zopanda kanthu
zongobwera kudzapeza nzeru kuchokera kwa mphunzitsi;
15
•
•
•
•
•
•
Amakhulupirira kuti timaphunzira kudzera mu kuchita, kuyeserayesera ndi m’malingaliro osati
kuloweza ndi kumangobwereza chimodzimodzi kapena kungosunga zomwe tamva;
Amakonzekera bwino koma amakhala olora kusintha zomwe wakonza molingana ndi mmene
ophunzira akufunira
Amakhala osangalala ndi phunziro komanso ophunzira
Amasunga malonjezo omwe walonjeza gulu=amawalora ophunzira kuyankhulapo komanso
kupumila
Amakhala odekha komanso omvetsera bwino
Amadziwa mmene angachitile ndi momwe iye akumvera.
Aphunzitsi akumbukile izi:
• Werengani buku lonseli musanayambe kuphunzitsa;
• Dziwani magawo onse musanayambe kuphunzitsa magawowa ndipo muonetsetse kuti muli
ndi zida zophunzitsira zokwanira musanayambe kuphunzitsa;
• Sinthani, poyenera kutero, zochitika ndi zokambirana zam’magulu kuti magawowa
akhale ogwirizana ndi msinkhu ndi nzeru za ophunzira anu;
• Ganizirani ndi kukonzekera za nkhani “zovuta” zilizonse zomwe zingadze mkatimkati mwa
magawo “ovuta”;
• Nthawi zonse yesetsani kupereka zitsanzo zodziwika bwino ndipo zochitachita zanu zikhale
zoti zikugwirizana ndi moyo ndi zosowa za ophunzira anu;
• Ngati nkotheka, yambani kuphunzitsa zophweka kumalizila ndi zovuta;
• Khalani ndi “pamalo posunga nkhani” pomwe mungamaike mitu yina yomwe yalowa
mkati mwa phunziro/gawo, yomwe sikugwirizana ndi zolinga za phunzirolo. Mungathe
kudzayikambirana nthawi yina kapena kufotokozera pamampeto pa gawoli kuti mituyo inali
yofunikira koma simagwirizana ndi mutu womwe umaphunzitsidwa;
• Konzani zochita zina zapadera zomwe zingakhale zothandizira pamene mukuchoka pa gawo
lina kupita pa gawo lina kapena pamene ophunzira chidwi chachepa kapena atopa;
• Onetsetsani kuti pamene zokambirana zili mkati wotsogolera akutola mfundo zofunikira ndi
kuzilemba pa tchati kuti zigwiritsidwe ntchito powomba mkota wa gawolo kapena phunzirolo.
Pangakhale povuta kuti inu nomwe mutsogolere komanso mulembe mfundozo kotero khalani
ndi wina wokuthandizani kulemba mfundozo;
• Onetsetsani kuti mukumaliza maphunziro anu mwabwino/mosangalatsa, ndi uthenga woti
ophunzira atenge. Poyenera kutero, fufuzani zina zozaphunzira mtsogolo komanso pezani
njira zothetsera vuto lomwe liripo.
• Onani ngati simukuyankhula kwambiri kuposa ophunzira. Ngati mmwapeza kuti mukuyankhula
kwambiri kusiyana ndi ophunzira, alimbikitseni kuti adziyankhana okha mafunso omwe
afunsa, mwachitsanzo, ngati wina wafunsa funso, liperekeni kwa ophunzira, “pali yemwe ali
ndi yankho ku funsoli?”;
• Mmene mukuchitila pamene mukuphunzitsa zingathandize kuti muphunzitse momveka
bwino. Mwachitsanzo kumuyang’anitsitsa ophunzira ndi kugwedeza mutu zimalimbikitsa
ophunzira kudziwa kuti zimene akuyankhula ndi zaphindu, Kuyang’ana kumbali kungamuuze
munthu kutiasayankhule komanso asatenge nawo mbali
• Sangalalani!
16
Kuyankhula nkhani zokhudzana ndi kugonana
Nkhani zambiri zomwe zili m’bukuli ndi zokhudzana ndi kugonana, maubwenzi ndi HIV zimene
zikupangitsa kuti wotsogolera pamodzi ndi ophunzira adzikambirana nkhani zomwe zili
zowoneka zolaula. Aphunzitsi ena angaganize kuti pokambirana ndi ophunzira nkhani zokhuza
kulera ndi kugonana ndiye kuti akulimbikitsa mchitidwe wogonana. M’malo mwake, Kafukufuku
akuonetsa kuti pokambirana ndi achinyamata nkhani zotere komanso powapatsa mfundo ndi
zotsatira zokhudza kugonana zimawalimbikitsa achinyamata kuchedwa kuyamba mchitidwe
wogonana komanso kuganizira zoti akhale wodziletsa. Aphunzitsi asaone ngati ophunzirawo
sachita mchitidwe ogonana.
Mmene mungawaonetsere ophunzira kuti muli omasuka kukamba nkhani zoterezi:
• Vomerani mawu omwe ali achilendo. Mungathe kuwafunsa matanthauzo ake a mawuwo
ngati simuwakudziwa.
• Nenani kuti simukudziwa, ngati musakudziwa. Koma muwauze kuti muwapatsa yankho
la funso lawo nthawi ina; kambani ndi wazachipatala kapena katswiri wina aliyense yemwe
angathe kukupatsani yankho loyenerera ndi kudzawayankha ophunzira anu.
• Musaweruze. Fotokozani mfundo zowona zokhazokha osati kunena maganizo akukhosi
kwanu.
• Musayankhe mafunso okamba za nkhani yanu yomwe yokhudzana ndi kugonana.
• Masukani. Mozama bwino, kambiranani kaye ndi aphunzitsi amnzanu pa gulu lanu kuti
mukakhale omasuka mukamakakambirana nkhani zotere ndi ophunzira anu.
Kuthana ndi mkwiyo
Ophunzira angathe kukhumudwa mkati mwa zokambirana. Aphunzitsi azitha kuthana ndi vuto
lotero zinthu zisanafike povuta kwambiri ndikusokonezetsa gulu lonse kapena kuapangitsa
wokhumudwayo kuvutika m’maganizo. Zina mwa njira zothanirana ndi kukhumudwako ndi
monga: kusintha nkhani yomwe yabweretsa mkwiyoyo, kufananitsa nkhaniyo ndi nkhani yina,
kuyamba mutu wina kapena kuyamba mwapuma.
Ophunzira angathe kukhumudwa chifukwa cha mitu yomwe ili m’bukuli. Atha kukhala ozikayikila
okha kapena omangika kuti akambirane ndi achinyamata anzawo nkhani zokhudza kugonana.
Zochitika zina za m’pulogalamu zingathe kuwakumbutsa zinthu zina zomwe zinayamba
zawachitikirapo mwina kusukulu kapena ku kunyumba kwawo.
Ngati wophunzira wakhumudwa chifukwa chifukwa cha chochitika, mphunzitsi amutengere
pambali kukakambirana za chomwe chamupangitsa kuti akhumudwe. Mphunzitsiyo angathe
kupereka mwayi kwa wophunzirayo kuti achokepo pagululo. Mphunzitsi sayenera kukakamiza
wophunzira kufotokoza zomwe zamupangitsa kuti akhumudwe. Mvetserani ku zomwe
wophunzirayo akufotokoza. Udindo wanu ndi kumumvetetsa, kupereka chilimbikitso komanso
chithandizo. Musamuwuze mmene ayenera kumvera kapena mmene mukuganizira kuti iye
akumvera. Mulimbikitseni kuti ndi umunthu kukhumudwa. Dziwani: muyenera kukhala okonzeka
kumuthandiza wophunzira yemwe wachitiridwa nkhanza za komwe angakamupatse uphungu
woyenera. Mudziwiretu za malo ngati amenewa kuyambirira komwe musanayambe kuphunzitsa
gawo loyamba.
17
Muuni wa zizindikiro
Mubuku lonseli, zizindikiro zina zochepa zaikidwa ndi cholinga chofuna kukuthandizani kupena zinthu
zosiyanasiyana:
Nthawi yomwe yaperekedwa pa gawo kapena chochitika
Zipangizo zofunikira
Aphunzitsi adziwe izi
Tsamba lokhala ndi zothandizira pa phunziro
18
Gawo 1
Tiyeni Atsikana! (GGI) – Tiyembekezere zotani?
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira akhala ngati atolankhani ndipo afunsana mafunso kuti apeze
zolinga za pulogalamuyi. Wotsogolera afotokoza zolinga za pulogalamu
ya GSI ndipo ophunzira ndandanda wa malamulo wotsogolera, kudzera
mu njira yolingalira n’cholinga chokonza chiyambi chabwino cha malo
ophunzirira omwe ndi otetezeka ndi osangalatsa.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha pa gawoli ophunzira athe:
1. Kufotokoza zolinga za GGI.
2. Akhazikitse zoyembekezera zawo pa za GGI.
3. Alingalire ndi kugwirizana malamulo wotsogolera pa za GGI.
Nthawi:
Mphindi 50
Zipangizo
zofunikira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Dziwani cholinga cha pulogalamu ya GGI (onani m’munsimu)
99 Lembani cholinga cha pulogalamu ya GGI pa bolodi kapena pa tchati
Cholinga cha pulogalamu ya Tiyeni Ophunzira!
“Cholinga cha pulogalamu ya GGI ndi kupereka maphunziro omwe ndi oteteza
komanso osangalatsa amene amapatsa ophunzira maluso okhudzana ndi umoyo
ndi nzeru pofuna kuwathandiza kukhala m’moyo wosangalala ndi wabwino,kukhala
m’sukulu ndi kudzimva kukhala otha kudziteteza okha ku mliri wa HIV/EDZI “
Mphindi 20
Zochitika 1: Kodi chichitike ndi chiyani mu GGI?
1. Lembani ndandanda wa zochitika za mu pulogalamuyi, kuphatikiza zinthu zina monga komwe
ophunzira adzikumanirana, masiku ake, nthawi ndi zina. Lembani ndi kumata mu chipindamo,
ngati ndi kotheka.
2. Mwachidule lembani cholinga cha pulogalamu ya GGI, yomwenso yalembedwanso pa bolodi:
“Cholinga cha pulogalamu ya GGI ndi kupereka maphunziro omwe ndi oteteza ndi osangalatsa
amene amapatsa ophunzira maluso okhudzana ndi umoyo ndi nzeru pofuna kuthawandiza
kukhala m’moyo wosangalala ndi wabwino, kukhala m’sukulu ndi kudzimva kukhala otha
kudziteteza okha ku mliri wa HIV/EDZI.”
19
3. Funsani ophunzira kuti akhale awiri awiri. Funsani ophunzira kuti aliyense akhale ngati
mtolankhani ndipo afunse mnzake mafunso otsatirawa:
• Ndi chiyani chingapangitse kuphunzira kukhala kosangalatsa?
• Kodi ndi chiyani mukuyembekezera kupeza kuchokera mu pulogalamu ya GGI?
4. Pamene wophunzira aliyense wafunsa mnzake ndi kufunsidwa, afunseni ophunzira kuti
apange bwalo.
5. Afunseni ophunzira: Ndi chiyani chomwe chimakupangitsani ambiri a inu kuphunzira kukhala
kosangalatsa? Ndi chiyani chomwe chimakupangitsani kuti mukhale ndi chidwi chotenga
nawo mbali pa phunziro?
6. Fotokozani kuti zochitika za GGI ndi zoti aliyense adzitenga nawo mbali ndipo afunseni ndi
kuwalimbikitsa kuti adziyankhula, kukambirana ndi kusewera. Afotokonzereni kuti patsogolo
pa gawloli akhonza malamulo wotsogolera n’cholinga choti kukambirana kukhale kwabwino
ndi kowasangalatsa.
7. Funsani wophunzira aliyense kuti apeze chomwe akuyembekeza kupindula mu kutenga nawo
gawo pa za pulogalamuyi. Lembani zimenezi pa bolodi kapena pa tchati. Kwa mayanko omwe
abwerezedwa lembani mzereb kunsi kwake pofuna kusonyeza kuchuluka kwa anthu omwe
apereka yankho limenelo. Funsani ophunzira kuti adzifotokoza maganizo awo, ngakhale
pamene wina wanena kale maganizo ofanana ndi omwewo.
8. Onani ndandanda wa mayankho pamene ophunzira onse amaliza kupereka mayankho awo
ndipo perekani ndamanga pa za mayankho omwe ali olondola ndi omwe ali osalondola
mokhudzana ndi pulogalamu ya GGI.
Zochita 2: Malamulo Aphunzitsi a GGI
Mphindi 15
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Malamulo otsogolera: Malamulo otsogolera ndi ndandanda wa mfundo zotsogolera
zomwe zimakhazikitsidwa ndi ophunzira mothandizana ndi wotsogolera pofuna
kuonetsetsa kuti malo ophunzirirawo ndi otetezedwa, aulemu, ndi achilimbikitso.
Malamulo amenewa nthawi zonse ayenera kumatidwa mu m’kalasi ndipo ophunzira
adzikumbutsidwa za malamulowa pachiyambi cha gawo lililonse.
1. Funsani ophunzira ngati amadziwa za malamulo otsogolera kapena malamulo a pagulu.
Funsani ophunzira kuti akambirane kufunika kokhazikitsa malamulo owatsogolera mu
pulogalamu monga ya GGI.
2. Auzeni ophunzira kuti ngakhale mu pulogalamu imeneyi aliyense akuyenera kutenga
mbali, palibe amene adzakakamizidwe kutero ngati asakufuna. Alimbikitseni ophunzira
kudzibetchera koma osati kutenga nawo mbali pamene ali omangika kapena osatakasuka.
Limbikitsani ophunzira “kuyesera, kukhala omasuka, ndi kulemekeza malire awo.” Pofuna
kuthandiza ophunzira kukhala omasuka malamulo otsogolera ayenera kukhazikitsidwa.
20
3. Funsani ophunzira kuti alingalire za malamulo otsogolera.
4. Lembani malamulowa pa tchati kapena pa bolodi ndi kuwamata kuti adzigwiritsidwa ntchito
nthawi zonse mu pulogalamuyi.
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Mukuyenera kumasinthasintha malamulo amenewa mogwirizana ndi ophunzira
amene muli nawo panthawiyo monga zaka zawo, ndi ubale womwe ulipo pakati
pawo.
Kuomba mkota pa gawoli
Mphindi 15
1. Unikaninso malamulo otsogolera amene mwagwirizana.
2. Unikaninso za zolinga za pulogalamu ya maluso okhudzana ndi umoyo ya GSI.
3. Athokozeni ophunzira potenga nawo mbali pa zochutika zonse. Fotokozani kuti kwa ena
zikhoza kukhala zachilendo kukhala omasuka kutenga nawo mbvali pa gulu chonchi koma
muwalimbikitse kuti pakupita pa nthawi azolowera ndi[po zikhala zophweka ndi zosangalatsa.
4. Fotokozani kwa ophunzira aliyense kuti ali ndi ufulu: wosatenga nawo mbali; okhal momasuka;
opangazinthu mosakakamizidwa; kuyankhula ndi aphunzitsi; kufunsa mafunso ndi zina
zambiri.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali.
2. Kambiranani za kalazi yotsatira:
•
•
•
NTHAWI YAKE ;
MALO AKE; komanso
MITU/MUTU odzakambirana.
21
Malamulo oyembekezereka a Tiyeni Atsikana!
• Chinsinsi: Zokambidwa muno siziyenera kunenedwanso kwina kulikonse.
• Kutenga mbali– Konzekerani kutenga mbali pa zokambirana ndi zochitika zonse. Lamulo
lokhudzana ndi chinsinsi lidzalimbikitsa chidwi cha ophunzira kuti adzitenga mbali ndi kukhala
omasuka kunena zakukhosi.
• Osaweruzana: Nzoloredwa kutsutsa koma nzosaloredwa kunena mnzanu kapena kumuzenga
mlandu chifukwa cha maganizo ake.
• Kulemekezana: Izi zingatanthauze mosiyana kwa anthu osiyanasiyana, koma kwambiri
zikutanthauza kumvetserana, kusaweruzanandi kuchitira anzathu zomwe ife tikufuna kuti iwo
adzitichitire.
• Mvetserani ndipo osamudula mnzanu pakamwa: Mvetserani amnzanu ndipo muwapatse
chidwi chanu chonse oswadula pakamwa. Aliyense adzapatsidwa mpata wotenga mbali.
• Ndi ufulu wa aliyense kukana kutenga nawo mbali: Ngakhale kuti pulogalamuyi
ikulimbikitsa aliyense kutenga mbali, nkoloredwa kungokhala osayankha kapena osatenga
mbali pamene akufunsani.
• Palibe funso lopusa kapena lopepera: Funso lina lirilonse ndi lanzeru. Pamakhala mwayi
wonse woti wina akhonza kukhala ndi funso lofanana ndi lomwelo.
• Osaganizirana: wophunzira ndi mphunzitsi asamangothamangira kutsirizitsa za maganizo,
mfundo, kapena khalidwe la munthu wina popanda umboni wokwanira.
22
Gawo 2
Mphamvu ndi Masomphenya a moyo wanga
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Pogwiritsa ntchito chithunzithunzi cha mumtima, ophunzira aganizira
za ziyembekezo ndi maloto a tsogolo lawo. Mtsogoleri awathandiza
ophunzirawa kudzera mu chochitika chomwe chili ndi cholinga
chodziwika bwino powathandiza kuti athe kukhazikitsa cholinga
chimodzi chodziwika bwino cha tsogolo lawo.
Zolinga za phunziro: Pakutha pa phunziroli, ophunzira athe:
1. Kutchula maonekedwe abwino a kakhazikitsidwe ka cholinga.
2. Kupanga cholinga chimodzi cha moyo wawo.
3. Kupeza njira zogonjetsera anthu komanso zinthu zobetchera zolinga
zathu.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Pepala kwa ophunzira aliyense
99 Lembani mfundo zofotokozera za cholinga chomwe chingatheke
kukwaniritsidwa pa bolodi
Ntchito 1: Masomphenya anga
Mphindi 40
1. Funsani ophunzira kuti aganizire za mafunso awa:
•
•
Ndi chinthu chiti chomwe amanyadira kuti anakwaniritsa?
Nanga ali ndi cholakalaka chanji chokhudzana ndi tsogolo lawo?
2. Funsani ophunzira kuti auzane zomwe amanyadira. Auzeni kuti adziomba m’manja mokweza
wina akamaliza kunena zomwe iye amanyadira m’moyo wake.
3. Momveka bwino adziwitseni ophunzira kuti ali ndi zowayenereza chifukwa ngati si choncho
sakanatha kukwaniritsa zinthu zomwe akunyadirazi. Afunseni ophunzirawa kuti atchuleko
zina mwa zomwe zinawathandiza kuti akwaniritse zimenezi. Zilembeni pa bolodi kapena pa
tchati. Zina mwa zomwe angatchule ndi monga: nzeru, kudekha, kukula, luntha lotha kupeza
zosowekera ndi zina zambiri.
23
4. Funsani ophunzira kuti aganizirenso za chinthu chomwe anakwaniritsapo chija. Pa nthawi
yomwe ankakwaniritsa chinthu chimenechi kodi padali zotchinga ndi zobetchera zilizonse?
Nanga anatha nazo bwanji? Anaika luso lanji? Nchiyani chomwe chinawapangitsa kuti asagwe
mphwayi?
5. Afunseni ophunzira kuti atseke m’maso ndipo aganizire za tsogolo lawo. Afunseni iwo kuti
alingalire za masana ano poyankha mafunso awa:
•
•
•
•
Muli kuti?
Mukutani?
Ndi chiyani chomwe mukusangalala nacho?
Ndi zinthu ziti zomwe mwasintha m’moyo wanu?
6. Tsopano awuzeni kuti adzilingalire mu mwezi ukubwerawu…? Chaka chikubwerachi…?
M’zaka zisanu…? M’zaka khumi…?
7. Fotokozani kuti pofuna kukwaniritsa zolinga za m’moyo wathu pamafunika kukhala ndi
ndondomeko yoyenera kutsatira.
Masomphenya omwe angathe kukwanitsidwa akhale:
• Owona: khazikitsani masomphenya omwe ali otheka ndi achilungamo. Ndi
zosangalatsa kukhala ndi Masomphenya odzakhala osewera mpira mwa ukadaulo,
koma kodi palibe masomphenya ena omwe mungathe kukwaniritsa mwachangu?
• Achindunji: khazikitsani masomphenya omwe ali achindunji ndipo mungawaloze
(mwachitsanzo, kumaliza maphunziro aku sekondale, kukhoza malikisi abwino
zedi m’masamu). Pewani kukhazikitsa masomphenya omwe ndiwovuta kuwaloza
komanso opanda chindunji (mwachitsanzo, kukhala wopambana, kukhala
wosangalala, kapena kutsatira maloto anga).
• Osinthika: Khazikitsani njira zingapo zomwe mungakwaniritsire masomphenya
anu. Khalani okonzeka kukumana ndi zobetchera ndipo gwiritsani ntchito zinthu
zomwe muli nazo m’moyo wanu kuti mugonjetsere zobetcherazi. Zikhulupirireni
nokha, mwagonjetsapo zobetchera zina m’mbuyomu.
• Osangalatsa/Olimbikitsa: sankhani masomphenya opatsa chidwi kuti
muwakwanitse, osati omwe wina akufuna kuti iwe uwakwanitse kapena kutengera
za dera lanu, kalasi lanu kapena chifukwa choti ndiwe mnyamata kapena mtsikana.
8. Fotokozani za masomphenya omwe angathe kukwanitsidwa:
9. Funsani ophunzira kukhala ndi mphindi zisanu zoti akonzere masomphenya a m’moyo wawo
pogwiritsa ntchito zofotokozera za masomphenya omwe angatheke amene alembedwa
m’bokosi liri pamwambali. Yenderani ophunzirawa ndi kuwathandiza kukonza cholinga cha
m’moyo wawo aliyense.
24
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Ophunzira ena sangathe kupeza masomphenya awo chifukwa amadziona osowa
chithandizo ndi opanda chiyembekezo. Muyenera kuwalimbikitsa mwapadera kuti
athe kukhazikitsa masomphenya omwe angawasangalatse ndi kuwalimbikitsa.
Ophunzira ena angathe kukhazikitsa zinthu zomwe zimayembezereka kuchokera kwa
iwo monga kukwatira ngati masomphenya a m’moyo wawo, alimbikitseni amenewa
kuti akhazikitse masomphenya omwe ndiwogwirizana ndi maphunziro awo.
10.Funsani ophunzira kuti anene kwa anzawo za masomphenya awo m’chiganizo chimodzi.
Ngati kalasiyo ndi yaikulu mungathe kuwagawa ophunzirawo m’magulu kuti awuzane
masomphenya awo m’magulumo.
11.Fotokozani kuti ophunzirawa akhala akugwiritsa ntchito masomphenya awowo mu
pulogalamu yonse ya GGI.
12.Chidwi chikhale pa kukakamira ndi kupirira kwa achinyamata pa kufuna kukwaniritsa maloto
awo ndi zolinga zawo ngakhale pamene akumana ndi zobetchera. Akumbutseni ophunzirawo
kuti ali ndi zowayenereza zonse kugonjetsa zovuta ndi kukwaniritsa zolinga zawo.
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
N’kofunika kuthandiza ophunzira kuika chidwi chawo pa masomphenya omwe
angathe kuwakwaniritsa. Ngakhale kukhala katswiri wampira kapena woyimba
wotchuka ndi maloto abwino, ophunzira ayenera kupeza masomphenya ena
oyambawa atalephereka.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Akumbutseni ophunzira kuti anakwaniritsapo kale zina zomwe amanyadira zija. Anagonjetsapo
kale zobetchera ndi zotchinga.
2. Tsimikizani kuti tsopano akhazikitsa masomphenya a m’moyo wawo ngati imodzi mwa mbali
ya gawo, ndipo apeza njira zomwe angagonjetsere zobetchera zilizonse ku masomphenyawa.
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga nawo gawo pa zokambiranazi
2. Kambiranani mmene kukumana kotsatira kudzakhalire:
•
•
•
NTHAWI YAKE;
MALO AKE; komanso,
MUTU/MITU yodzakambirana.
25
Gawo 3
M’bokosi langa, kutuluka bokosi langaa
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Pogwiritsa ntchito mabokosi owoneka, ophunzira athe kupeza zomwe
dziko limayembekezera kuchokera kwa iwo monga anyamata ndi atsikana
komanso zomwe dziko limawaletsa anyamata ndi atsikana kuchita.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kupeza mmene zoyembekezereka kuchita mnyamata kapena
mtsikana zingawabwezere m’mbuyo.
2. Kukonza njira zotulukira mu maudindo okakamizawa.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 Bolodi/Choko kapena tchati/pentopeni
99 Jambulani mabokosi awiri pa bolodi kapena pa tchati. Alembeni yina
“mnyamata” yina “mtsikana”.
99 Unikani chitsanzo cha mndandanda wa maudindo ogwira amuna ndi
maudindo a akazi ngati ophunzira angapeze vuto lolingalira( onani
ntchito yoyamba).
Ntchito 1:Sewero lochita ngati
mnyamata/kuchita ngati mtsikana
Mphindi 25
1. Gawani kalasi yanu m’magulu awiri: anyamata gulu lina atsikana gulu lina.
2. Funsani anyamata kuti akonze kasewero komwe azipanga zinthu ngati atsikana. Sewero
lisankhale lonena za munthu yemwe alipo m’kalasimo. Funsani gulu la atsikana kuti lichite
zomwezo ndipo lipange zinthu ngati anyamata.
3. Funsani gulu lirilonse kuti lowonetse kasewero kawo kwa mphindi ziwiri.
4. Pogwiritsa ntchito timasewero tija, afunseni ophunzira kuti alingalire zilizonse zokhudza
atsikana zomwe akuganiza kuti “amaloredwa kapena amayembekezereka kuchita” ndi
chikhalidwe, dziko, dera, banja, anzawo ndi ena otero. Lembani mayankho awo mwachidule
mkati mwa bokosi la “atsikana”.
26
5. Kenaka funsani ophunzira kuti alingalire zonse zokhudza atsikana zomwe akuganiza kuti
atsikanawo “saloredwa kapena sayembezereka kuchita” ndipo muzilembe kunja kwa bokosi
la “atsikana”.
6. Ophinzira angathe kugwiritsa ntchito timasewero tija koma alimbikitseni kuti aganizirenso
zoyembekezera zina zomwe sanaonetse m’timaseweroto koma zoti zimachitikanso.
7. Bwerezaninso zomwezi ndi bokosi la “anyamata”
Mwachitsanzo:
Mnyamata
Kukhala
wawukali,
wolimbika
ntchito,ophunzira,
wandeu,ofunsa
mafunso ambiri,okwatira, okhala ndi ana
ambiri, kukhala bwana, ovuta, omwa
mowa kwambiri
Mtsikana
Kuthandiza ntchito za pa khomo, kukhala
odekha, kukhala ofatsa, kukhala ndi ana,
Kusamala apa banja lake, kuphika, opanda
makani, aziyang’ana pansi akamayankhula,
Kukhala wawukhondo,wooneka bwino
Anyamata (Kunja kwa bokosi): Kusamalira,
kusamala ana, ofatsa
Atsikana (Kunja kwa bokosi): Kulira, Kuchita
bwino mkalasi, kufunsa mafunso, Awukali,
aukhondo
8. Fotokozani kuti anyamata ndi atsikana amakembezereka kuchita zinthu zina chifukwa choti
ndi mnyamata kapena chifukwa ndi mtsikana.
9. Funsani anyamata: pali chirichonse mu bokosi la atsikana chomwe mukulakalaka chikadakhala
m’bokosi la anyamata? Chifukwa? Pali chilichonse m’bokosi la anyamata chomwe mukulakalaka
kuti sichidakhalamo? Chifukwa? Pali chilichonse chomwe chiri panja pa bokosiri chomwe
mukulakalaka chikadakhala mkati mwa bokosiri?
10.Funsani atsikana: pali chirichonse chomwe chiri mu bokosi la anyamata koma mukulakalaka
chikadakhala mubokosi la atsikana? Chifukwa? Pali chirichonse mkati mwa bokosi la atsikana
chomwe mukulakalaka chidakachokamo? Chifukwa? Pali chiriconse chomwe chiri panja pa
bokosiri chomwe mukulakalaka chikadapezeka mkati mwa bokosiri?
Ntchito 2: Maudindo oyenera Amuna
kapena oyenera Akazi ndi Ine
Mphindi 15
1. Funsani ophunzira ngati, monga mmene ziriri mu mabokosimo, anauzidwapo kuchita china
chake kapena osachita chifukwa choti ndi amuna kapena ndi akazi? Funsani zitsanzo.
2. Funsani ophunzirawa mmene anamvera mumtima mwawo atuzidwa kuti apange choncho
chifukwa choti ndi amuna kapena akazi?
27
3. Funsani ophunzira zomwe zimachitika ngati mtsikana wapanga zinthu ngati mnyamata?
Chimachitika n’chiyani mnyamata akapanga chinthu ngati mtsikana?
4. Kodi tiri ndi mayina apadera a anthu amene amaterowo? Mayina ndi oti chiyani? Kodi mayina
amenewa ndi abwino kapena oyipa?
5. Ndi ubwino wanji womwe ungabwere pamene anyamata ndi atsikana akupanga zokhazo
zomwe amayembezereka kuchita? Nanga zimenezi n’zolakwika bwanji?
6. Funsani ophunzira ngati pali chirichonse chomwe tingachite pa zomwe timayembezereka
kuchita monga ife poti ndi anyamata kapena atsikana koma zoti sitisangalala nazo? Kodi
tingazisinthe? Mwa njira yanji?
7. Fotokozani kwa ophunzira kuti cholinga cha ntchitoyi sikuzenga mlandu aliyense koma
kuwathandiza kusankha “zoyembezereka za ine monga mnyamata kapena monga ine
mtsikana zomwe ndi zaphindu ndipo sindikufuna kuzisintha; ndi zoyembezereka za ine monga
mnyamata kapena mtsikana koma sindisangalala nazo ndipo ndikulakalaka kuti ndizisinthe.”
8. Funsani ophunzira ngati pali zoyembezereka za anyamata kapena atsikana zomwe kalasi lonse
likufuna zitasintha mkati mwa pulogalamuyi.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Funsani ophunzira kuti auze gulu zomwe iwo aphunzira zokhudza maudindo a amuna ndi a
akazi.
2. Funsani ophunzira ochepa kuti ofotokoze chomwe akuganizira kuti kuzindikira za maudindo
okhudza amuna ndi maudindo okhudza akazi ndi kothandiza pa moyo wawo.
3. Funsani ophunzira mmene nzeru zimenezi zisinthire moyo wawo.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga mbali pa zokambiranazi.
2. Kambiranani za mmene kukumana kotsatira kudzachitikire:
•
•
•
28
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 4
Maubwenzi abwino
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Pogwiritsa ntchito zitsanzo zochitika ophunzira afufuza zoyenereza
mnzawo komanso kukhazikitsa malire a ubwenzi wawo.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kutchula zoyenereza maubwenzi abwino.
2. Kunena malire a maubwenzi.
3. Kuonetsera malire a maubwenzi abwino.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Pepala limodzi losalembapo kwa wophunzira aliyense Zopinira
99 Lembani zitsanzo zochitika m’maubwenzi pa bolodi (onani Ntchito 2)
Ntchito1: Kufufuza mnzako
Mphindi 20
1. Funsani ophunzira kuti aganizire za munthu amene angalakalake kuti akhale mnzawo wabwino
kapena amene akufuna kuti akhale mnzawo
2. Funsani ophunzira kuti aganizire za chiganizo ichi: ‘mnzanga wa pa mtima ndi mnzanga mnzanga
wa pamtima chifukwa ….’ Funsani wophunzira wina aliyense kuti anene makhalidwe awiri amene
mnzawo wa pamtima ali nawo ndipo lembani mayankho pa bolodi kapena pa tchati, monga wa
chidwi, wamnsangala ndi zina.
3. Tsopano funsani ophunzira kuti akonze choyitanaira malonda ndi mutu woti “Amene akufufuza
mnzake” Malondawo awonetse zimene zimakusangalatsani, zokonda zanu ndi makhalidwe abwino
amene mukudikilira mwa munthu amene mukufuna kuti akhale mnzanuyo.
4. Funsani ophunzira kuti apachike malonda awo pa khoma kuti akambirane. Funsani ophunzira
mafunso awa woti akambirane:
•
•
Kodi ndi makhalidwe ati ofunikira amene mukuyembekezera, mogwirizana ndi malonda
anu?
Kodi ndi makhalidwe ati amene ali ofunikira kwambiri?
29
•
•
•
•
•
•
Kodi ndi khalidwe liti limene ndi losavuta kulipeza mwa mnzako?
Kodi ndi khalidwe liti limenen ndi lovuta kulipeza mwa mnzako?
Kodi mumayembekeza makhalidwe ofanana kuchokera kwa amnzanu amuna kapena
kwa amnzanu akazi?
Kodi mukuganiza kuti nthawi zambiri anyamata kapena atsikana amafuna makhalidwe
ofanana kuchokera kwa amnzawo? Chifukwa chiyani?
Kodi ndi makhalidwe wotani amene amnzanu angaone kuchokera kwa inu?
Kodi anyamata ndi atsikana amasiyana makhalidwe awo pa ubwenzi?
Ntchito 2: Ndingatani?
Mphindi 20
1. Mzanga atandipempha kuti ndimwe mowa, ndinga…
2. Mzanga atandipempha kuti ndisalowe mkalasi, ndinga…
3. Mzanga atandipempha kuti ndimuthandize kuwerenga kukonzekera mayeso,
ndinga…
4. Mzanga atandipempha kuti ndibe, ndinga…
5. Mzanga atandilimbikitsa kuti ndizigonana mosinthana ndi ndalama, ndinga…
6. Mzanga atandipempha kuti ndiname mmalo mwake, ndinga…
7. Mzanga atandipempha kuti ndimuthandize kuyang’anila mwana wa kwawo,
ndinga…
8. Mzanga atandiuza kuti ndikagonane, ndikakana ndiye kuti sindine mkazi/mamuna,
ndinga…
9. Mzanga atandipempha kuti ndimuthandize kunyamula dengu lolemera kupita
nalo kumsika, ndinga…
10.Mzanga atandiuza kuti ndisiye kchita ntchito yakusukulu yochitila kunyumba,
ndinga…
1. Funsani ophunzira akhale awiri awiri.
2. Funsani magulu a ophunzira asankhe zina mwa zitsanzo zili bokosizi ndipo akambirane
mmene iwo akanachitira. Funsani iwo kuti ayesetse kuchita izi mwa chilungamo.
30
3. Bwezerani ophunzira pamodzi.
4. Kambiranani ntchito iyi ndi gulu, potsatira mafunso awa:
•
•
•
•
Kodi ndi zinthu ziti ziwiri zimene mungachite pofuna kuthandiza mnzanu?
Kodi ndi zinthu ziti ziwiri zimene simungawachitire amnaznu ngakhale zitavuta bwanji?
Kodi pali zinthu zina zimene simungachite, koma mungathe kuchita ngati mnzanu wabwino
atakufunsani kutero? Ophunzira sayenera kuwulutsa zimenezi, koma yesetsani kuwafotokozera
kapena kumvetsetsa chifukwa chimene munthu angathe kuchitira
Ndi nthawi iti yomwe ubwenzi umakhala wosasangalatsatso kwa inu?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Funsani ophunzira zomwe angachite pofuna kupeza ndi kusunga maubwenzi abwino omwe
akukwaniritsa zimene analemba ngati zofunikira pamene amasatsa malonda awo mu Ntchito1.
2. Akumbutseni ophunzira kuti maubwenzi abwino ndi wofunika pachinyamata chawo, koma
nthawi zina akuyenera kukhala ndi malire. Awuzeni “nthawi zina amnzanu amafuna kuti
muchite zomwe inu simukufuna ndipo muyenera kukhala olimba ndi kuchita zokhazo zomwe
zilim zokukomerani” poganizira za phunziro la kukhazikitsa masomphenya lomwe anali nalo
m’mbuyomu, akumbutseni ophunzira kuti ali ndi zonse zowayenereza zomwe zingawathandize
pa nthawi ngati zimenezi.
3. Funsani ophunzira zina zomwe aphunzira mu gawo limeneli ndi mmene ziwathandizire mu
moyo wawo wa tsiku ndi tsiku.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira potenga mbali pa zokambiranazi.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
31
Gawo 5
Yankhulani! Kulumikizana ndi Ena
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira awone njira zosiyana zolumikizirana monga kuyankha
modzikhulupirira, modzikaikira, ndi mwamakani ndipo pamapeto pake
athe kugwiritsa ntchito luso loyankha modzikhulupirira.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kutanthauzira kulumikizana modzikaikira, mwamakani,
modzikaikira.
2. Kupeza ndi kugwiritsa ntchito maluso abwino olumikizirana.
ndi
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Pali chionetsero pachiyambi penipeni pa Ntchito 1. Chiwonetserochi
chiri pa kulumikizana modzikhulupirira, modzikaikira ndi mwamakani.
Wotsogolera atha kuchita chiwonetserochi ndi wophunzira kapena
mphunzitsi mnzake- muyenera kukonzekera mwapadera gawoli
lisanayambike.
99 Lembani matanthauzo a kulumikizana modzikhulupirira, modzikaikira
ndi mwamakani pa bolodi (onani Ntchito 1). Ophunzira mwina
angazunguzike ndi mawu oti”modzikhulupirira”, “modzikaikira”, ndi
“mwamakani”. Ngati ndi choncho gwiritsani ntchito “mwamphamvu”,
“mwaulesi”, ndi “mwandewu”.
99 Kugwiritsa ntchito manja poyankhula komanso ndi akapandamneni ndi
zina mwa zitsanzo zomwe mungagwiritse ntchito. Mukulimbikitsidwa
kugwiritsa ntchito zitsanzo zogwirizana ndi chikhalidwe chanu kapena
dera lanu. Zolembedwa zoonjezera zomwe ziri m’munsizi zonena kuti
“Kuyankhula zomwe tikufuna ndi zomwe tikumva m’mtima mwathu”
zomwe ziri kumapeto kwa gawoli zingathandize kukhala ndi mfundo
zothandiza kuti timvetsetse za mitundu itatu yakayankhulidweka.
Ntchito 1: Njira zitatu zonenera chinthu chimodzi
Mphindi 15
1. Fotokozerani ophunzira kuti mupanga chiwonetsero cha njira zochepa zosiyana zomwe
zimagwiritsidwa ntchito polumikizana, pogwiritsa ntchito wophunzira kapena mphunzitsi
mnzanu kuti akuthandizeni. Funsani ophunzira kuti akutengeni ngati inunso ndi wophunzira
32
mnzawo amene mukufuna kufunsa ophunzira winayo kuti akuthandizeni ntchito yochitira
kunyumba yomwe akupatsani kusukulu.
• Mwaulesi/mopanda
mphamvu:
Mopanda
kumuyang’ana
mnzanu
amene
mukumuyankhulayo nenani kuti”Zikadakhala zosangalatsa ngati wina anakandithandiza
ntchitoyi, chifukwa popanda kundithandiza ndiye ndilakalakwa”.
• Mwamakani/Mwandewu: Muyang’aneni mnzanuyo ndipo mumuyandikire ndikumuuza
mokweza kuti “ukuganiza ndiwe wochenjera, uyenera kundithandiza ntchito yangayi kupanda
kutero ndikakalakwa ndi iweyo.”
• Modzikhulupirira/Mochangamuka: Muyang’aneni mnzanuyo koma mwaulemu,
“ndikuganiza ndiwe wanzeru ndipo ndikufuna munthu woti andithandize ntchito yangayi.
Kodi ungandithandizeko ntchitoyi tikamaliza makalasi leroli?”
Funsani ophunzira zomwe angotha kuonazi. Afunseni zomwe angachite pa njira iliyonseyi? Ndi
njira iti yomwe inakawapangitsa kuti amuthandize mzawoyo kapena kuti asamuthandize? Ndi
njira iti yomwe ingawapangitse kuti iwo amve kulemekezeka? Ndi njira iti yomwe ingawawopse?
Chifukwa?
2. Kumbutsanani matanthauzo a kulumikizana aja tinawapeza kumayambiriro kwa gawoli.
Afunseni ophunzira pa njira zomwe zinawonetsedwa pa chiwonetsero paja kuti ndi iti yomwe
ili chitsanzocha kulumikizana kwa ulesi? Kwa mphamvu? Kwa ndewu?
Njira zitatu zolumikizirana ndi matanthauzo ake
• Mwamakani/mwandewu: kupereka uthenga mwankhanza mopanda kuganizira
kuti winayo amva bwanji; kuyankhula mwamavuvu. Kulumikizana “mwandewu”.
• Mwaulesi/mopanda mphamvu: kupereka uthenga mosanena zowona zenizeni
zomwe ukufuna kapena ukuganiza ndipo nthawi zina umangokhala chete.
Kulumikizana “mwaulesi”.
• Modzikhulupirira/mwamphamvu:
Kupereka
uthenga
poyankhula
mwachilungamo zakukhosi; mwachindunji ndi momveka; mopatsana ulemu.
Kulumikizana “mwamphamvu”.
3. Funsani ophunzira kuti anene nthawi zomwe kungakhale koyenera kugwiritsa ntchito njira
zolumikizirana za makani kapena za ulesi.
4. Dziwani kuti, monga zitsanzo za ophunzira zikuonetsera, pali nthawi zomwe njira za makani
kapena zaulesi zingakhale zabwino kugwiritsa ntchito polumikizana, koma gawo lino chidwi
chake chikhala pokweza maluso a njira ya mphamvu/yodzikhulupirira.
33
Chochitika chachiwiri: Mmene tingakwanitsire
njira yolumikizirana yodzikhulupirira
Mphindi 10
Perekani ndi kufotokozera njira zinayi zokwanitsira njira yolumikizirana ya kudzikhulupirira:
1. “Ndikumva …”pamenepa wophunzira ayenera kunena mmene akumvera mtima mwake.
2. “Pamene iwe wa…” pamenepa wophunzira amanenena zomwe mnzake wamuchitira kuti iye
amve mmene akumveramo. Tiyenera kuzindikira kuti cholinga cha ichi sikumunena mnzathuyo
koma kufotokoza mmene ife tikumvera.
3. “Chifukwa…” wophunzira amafotokoza chifukwa chomwe chochitikachomchimamupangitsa
kuti iye amve choncho.
4. “Ndipo ndikufuna…. Kodi wophunzira akadakonda chikadachitika ndi chiyani kuti amve bwino?
Zina mwa zitsanzo zomwe mungapereke:
a. Ndimamva kuwawa…
pamene ukandiitana kuti mwana...
chifukwa sindifuna kusuta chamba kapena kuchita zachiwerewere ndi anyamata omwe
sindikuwadziwa…
ndipo ndikufuna kuti iweyo udzivomelemekeza mmene ine ndimamvera zokhudzana ndi
makhwala ozunguza bongo komanso chiwerewere.
b. Ndimachita mantha…
ukandiyandikira kwambiri...
chifukwa ndi nzopatsa mantha...
ndipo ndikufuna uzinditalikira
c. Sizimandisangalatsa…
pamene ukundiuza ndisamapite ku sukulu...
chifukwa ndimaganiza kuti umandiona opusa …
ndipo ndikufuna iwe uzindivomereza maganizo anga opita ku sukulu
Ntchito 3: Ndinganene chiyani?
Mphindi 15
1. Funsani ophunzira kukhala awiri awiri ndipo aliyense atenge mbali poyankha mafunso
okhudzana ndi njira yolumikizirana ya kudzikhulupirira/ya mphamvu.
•
•
34
Mnyamata/Mtsikana amene umamukonda akufuna mupite kukamwa mowa.
Munthu amene sukumudziwa wakumana nawe panjira ukupita kusukulu ndiye
wakupatsa mwayi woti akutenge pagalimoto.
2. Funsani ophunzira mafunso okambirana awa:
•
•
•
Mukumva bwanji za kugwiritsa ntchito maluso a njira yakudzikhulupirira/mphamvu
polumikizana?
Munamvapo mawu aliwonse amphamvu omwe inu nmungagwiritse ntchito? Mawu oti
chiyani?
Kodi mawuwa munawamva bwino? Panali povuta kuwadzudzula amnzanu? Chifukwa?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Funsani ophunzira afotokoze mmene kuyankhula mochangamuka kungawatetezere iwo
komanso amnzawo?
2. Funsani ophunzira mmene luso lokhala ochangamuka lingawathandizire kukwaniritsa
cholinga cha tsogolo lawo
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Fotokozani kwa ophunzira kuti nthawi zambiri pamakhala povuta kuwadzudzula
amnzathu chifukwa chofuna kuteteza zinthu monga kutchuka, kunenedwa kapena
kunyozedwa. Fotokozani kuti kutsogolo kwa maphunzirowa kuli njira zomwe
tingagwiritse ntchito pothana ndi mavuto ngati amenewa.
3. Auzeni ophunzira kuti mu nthawi zoopsa, pamene anthu akulamuliridwa ndi mphamvu
ya mowa kapena chamba, kulumikizana kudzera m’njira ya kudzikhulupirira/mphamvu
sikungathandize ndipo chomwe akuyenera kuchita ndi kungochokapo pamalopo mwachangu.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali pa zokambirana.
2. Kambiranani mmene phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
35
Kunena mmene tikumvera ndi zomwe tikufuna
Njira zingapo za mmene timakhalira
Mabanja athu amatiphunzitsa mmene tikuyenera kukhalira kuymbira tikadali ang’ono. Pali njira
zosiyanasiyana za mmene tingachitire pamalo ndipo izi zimabweretsa zotsatira zabwino kapena
ziopa malinga ndi mmene tachitira.
Timapanga zinthu mopepera ngati:
•
•
•
•
•
•
•
•
•
Sitikupangapo kanthu pofuna kudziteteza tokha
Pololera kuchita zinthu zomwe ena akufuna.
Pokhala chete pamene sitikugwirizana kapena sitikusangalala ndi zomwe zikuchitika
Tikuvomereza chilichonse
Kunena kuti “pepani” nthawi zambiri
Tikubisa zokhumba zathu
Sitikufuna kuyamba chinthu chatsopano chifukwa tikuopa kulephera pamapeto
Tikulora ena adzingonena okha zoti zichitike
Tikungotsatira chigulu kapena kuonera anzathu
Timaonetsa m’khalidwe wamakani/wandewu pamene:
•
•
•
•
•
•
•
•
Tikupanga chinthu osaganizira kaye anzathu
Tikunena kuti timupangira wina choipa n’cholinga chokwaniritsa zomwe ife tikufuna
Tikudziika patsogolo ngakale ena akupwetekeka nazo
Tikungolamula osamva kaye maganizo komanso zomwe amnzathun akufuna
Tikukwiya msanga pamene ena atsutsana nafe
Tikukalipa, kukankha kapena kuumiriza amnzathu
Tikupangitsa ena kumva kuti akufunika kudziteteza
Tikupangitsa anthu ena kuoneka ang’ono kuti ife tioneke akulu
Timagwiritsa ntchito m’khalidwe wochangamuka pamene:
•
•
•
•
•
•
•
•
•
•
36
Tikudzichitira kanthu mosakhumudwitsa ena
Tikudzilemekeza tokha pamodzi ndi anzathu ena
Tikunena maganizo ndi zokhumba zathu mwachilungamo ndi momveka
Tikakamira pa mfundo zoyendetsera moyo wathu
Tigwirizanitsa zonena zathu ndi zochita zathu
Tichita zinthu molimba mtima koma mwaulemu
Tivomera kutiyamikira ndi kusangalala tokha ndi zochita zathu
Tikuvomereza maganizo abwino kuti atisinthe ndi kuphunzirako kuchokera ku maganizo
amenewo
Tinena kuti “ayi” mosakhumudwa
Titsutsa koma osakwiya
Gawo 6
Akuluakulu ngati othandiza
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira aunika zomuyenera munthu wamkulu wothandiza. Ophunzira
anena nkhani zomwe zikuonetsera maonekedwe a munthu wamkulu
wothandiza ndi wosathandiza.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kufotokoza mmene ubale wabwino ndi munthu wamkulu umakhalira.
2. Kunena maonekedwe a munthu wamkulu wothandiza.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunkira:
99 PBolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Zomatira kapena zopinira
99 Lembani ndandanda wa Mkulu Wothandiza womwe uli m’munsiwu
ndipo muwumate pakhoma mchipinda, ngati chithunzi kapena
pabolodi.
Mkulu wothandiza...
• Amamvetsera zokamba achinyamata.
• Amakhulupirira kuti achinyamata nawo ali ndi zofunikira zomwe zingathandize ku
dziko.
• Amazindikira kuti achinyamata ali ndi ufulu.
• Amadziwa kuti achinyamata nawo ali ndi zolinga m’moyo wawo.
• Amawapatsa zofunikira ndi kuwathandiza kuti apeze zofunikira.
• Amalemekeza achinyamata.
• Amaona achinyamata kukhala anthu omwe ali ndi mwayi wotha kuchita bwino
osati ngati ovuta, ongoyendayenda.
• Amamasuka kwa achinyamata.
• Amakhala chitsanzo chabwino.
Ntchito 1: Maonekedwe othandiza/osathandiza
Mphindi 15
1. Funsani ophunzira kuti alingalire ena mwa maubwino wokhala ndi munthu wamkulu
wothandiza pa moyo wawo. Fotokozerani mwachidule.
37
2. Fotokozani kuti nthawi zina ophunzira amathandizika ndi kuwunikira, kuthandiza, ndi
kuphunzitsa komwe akulu akulu wothandiza amachita. Nthawi zina akulu akulu amenewa
amatchedwa atsogoleri. Funsani maina ena omwe akulu akulu wokhulupirikawa, wothandizawa
angadziwike nawo.
3. Funsani ophunzira aganizire nthawi yomwe anapindulapo kuchokera ku ubale wangati
umenewu. Kodi anakuchitirani chiyan? Anakuphunzitsani chiyani? Ndi chithandizo chanji
chamumtima chomwe munapeza kuchokera kwa munthuyu?
4. Gawani ophunzira kukhala magulu awiri. Fotokozani kuti malingana ndi zochitika zotsatira
titchula kuthandizika kwabwino ndi akuluku kuti ”Wamkulu wothandiza”. Funsani gulu limodzi
kuti liringalire ndi kulemba pa tchati ”wamkulu wothandiza ndi amene...”. Funsani gulu linalo
kuti lilingalire ndi kulemba pa tchati ”wamkulu wosathandiza ndi amene…”
5. Khomani matchati onsewa pabolodi ndi kukambirana.
6. Mukuloza patchati yandandanda “wabwino”, funsani ophunzira kuti afotokoze chifukwa
chomwe mfundo zimenezi zikuonetsera mkulu wothandiza? Tingadziwe bwanji kuti
zitsanzozimenezi zikuonetsera kuthandiza kwabwino?
7. Mukuloza pa tchati ya ndandanda wa “zoipa”, afunseni ophunzira chifukwa chomwe mfundo
zimenezi zikuonetsera mkulu wosathandiza? Tingadziwe bwanji kuti zitsanzo zimenezi
zikuonetsera kuthandiza kolakwika?
8. Funsani ngati akulu wosathandiza amaganizako kuti akukhala akulu wothandiza? chifukwa?
Ntchito 2: Munamva?
Mphindi 25
1. Funsani ophunzira kukhalanso m’magulu awiri ngati mmene anachitira poyamba muja. Gulu
lililonse likonze nkhani ziwiri zosiyana zomwe auze anzawo kudzera mu kucheza. Fotokozani
kuti nkhani zonse zikhale ndi mutu wofanana, kuonetsera maonekedwe abwino a mkulu
wothandiza.
2. Funsani ophunzira kuti agwirizane “zoti zikhale m’nkhanizo”. Mwachitsanzowophunzira apite
kwa wamkulu chifukwa ophunzira ena akumuwopseza kuti amumenya.
3. Lolani kuti ophunzira akonzekere nkhani zoti auze anzawozo mokwanira. Nkhanizo zikhale
zopatsa mudyo ndipo ziwonetsere mmene zinthu zimakhalira muja ana akamakamba nkhani
ndi makolo kapena agogo awo.
4. Abweretseni ophunzira onse pamodzi kuti akambe nkhani zawo.
38
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Ophunzira ambiri apusitsidwapo kapena kunyengeleredwa kuchita zachiwerewere
ndi akulu akulu pomanamizira kuwathandiza. Nthawi zina akulu otere amayamba
amuthandiza mwanayo kwa kanthawi asanamuchite chipongwe. Zikatero anawa
akhumudwa chifukwa chachimenechi ndipo amadzida. Ndo koyenera kuwafotokozera
ophunzira za choopsachi, komwe angapeze chithandizo, ndi kuti si vuto lanu kotero
sayenera kudzida.
5. Gulu lirilonse likamaliza kufotokoza nkhani yawo; afunseni:
•
•
•
•
•
Ndi chiyani chomwe mwamva kuchokera m’nkhaniyi chomwe chinali chabwino kapena
chothandiza kwa wophunzira yemwe amathandizidwayo?
M’nkhaniyi, ndi chiyani chomwe mwamva chomwe chinali chosathandiza kapena choipa
kwa wophunzirayo?
Mungaganizeko nthawi yomwe wamkulu angathe kumupusitsa wophunzirayo
ndikumuchita chipongwe m’njira iliyonse?
Kodi ukuyenera kuchita chiyani pamene wamkulu wakuchita chipongwe mokupusitsa?
Kodi ungapite kuti kukapeza chithandizo nzoterezi zitakuchitikira?
6. Perekani maganizo a komwe ophunzira angapite kukapeza chithandizo.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Akumbutseni ophunzira za maonekedwe a wamkulu wothandiza.
2. Limbikitsani ophunzira kukhala atcheru ngati maonekedwe a mkulu wothandiza
akuwakayikitsa kapena akuwachititsa mantha. Akumbutseni kuti akuyenera kutsatira zomwe
mtima wawo ukuwauza.
3. Akumbutseni ophunzira kuti ngati wamkulu wagwiritsa molakwika ubale wawo ndi kuphwanya
ufulu ndi chikhulupiriro cha wachinyamata yo ndipo izi n’zosaloledwa.
4. Afunseni ophunzira, kutengera ndi zomwe aphunzira, komwe angapite kukapeza chithandizo
ngati zimenezi zitawachitikira. Unikani anthu/malo omwe kungapezeke chithandizo ngati
wamkulu aliyense atagwiritsa molakwika udindo wake ngati wamkulu wothandiza.
39
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali pazokambiranazi.
2. Kambiranani momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
40
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTI/MITU yodzakambirana.
Gawo 7
Thupi langa likusintha-ndiri bwinobwino? Gawo 1
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira akambirana kusintha m’maganizo ndi m’thupi kosiyanasiyana
munthu akatha msinkhu.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha pa phunziroli, ophunzira athe:
1. Kufotokoza kusinthika m’maganizo komanso m’thupi pamene
munthu watha msinkhu.
2. Kuzivomereza zosinthika zones m’thupi mwawo akathera msinkhu.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Mapepala a notsi owonetsa kusintha kwa thupi la mtsikana komanso
mnyamata pamene watha msinkhu (kumapeto kwa phunziro): ngati
n’kotheka aliyense akhale ndi mapepala awiri onsewa.
99 Pepala losalembapo kanthu pa gulu la ophunzira asanu aliwonse
99 Unikaninso ndi kumvetsetsa notsi zosonyeza kusinthika kwa
mnyamata/mtsikana akatha msinkhu zomwe zili kumapeto kwa
gawoli.
99 Unikaninso ndi kumvetsetsa tsamba lowunikira la “Mmene
Tingayankhulire ndi Achinyamata Zokhudzana ndi Kugonana” lomwe
lili kumapeto kwa gawoli.
Ntchito 1: Kutha Msinkhu– N’zabwinobwino
Mphindi 40
1. Auzeni ophunzira kuti kutha msinkhu ndi nthawi yosangalatsa kwambiri pa moyo wa munthu
pamene pamakhala kusinthika kosiyanasiyana kosangalatsa. Afunseni ophunzira kuti
aganizire mawu oti “kutha msinkhu”. Amawamva bwanji mawuwa? Chimachitika ndi chiyani
pa nthawiyi? Lembani mayankho awo papepala kapena pa bolodi.
2. Fotokozani kuti kusintha komwe kumachitika panthawiyi kumachitika m’thupi ndi m’maganizo.
Afunseni ophunzira kuti muthandizane kugawa mayankho kuchokera pa 1 m’magawo awiri:
m’thupi kapena m’maganizo.
41
3. Afotokozereni ophunzira mfundo zokhudza kusintha kwa m’thupi ndi m’maganizo komwe
kumachitika munthu akamatha msinkhu. Pamene mukufotokazapo muzichonga zomwe
ophunzira aja ananena kale ndipo muwonjezere zomwe ophunzirawo sanazinenem pa
ndandanda wawo uja:
•
AKutha msinkhu kumayamba ndi kutha nthawi zosiyana kwa anthu osiyananso
(anyamata ndi atsikana). Ophunzira amasintha pa mlingo wosiyana malinga ndi thupi
lawo. Zimenezi sizingasinthidwe chifukwa ndi chibadwa. Kusiyasiyana kumeneko ndi
kwabwinobwino.
•
Atsikana nthawi zambiri amatha msinkhu mwamsanga kuposa anyamata. Kusiyana
kumeneku ndi chilengedwe kotero ndi kwabwinobwino.
•
Panthawi yomwe munthu kutha msinkhu, thupi limatulutsa zinthu zotchedwa mahomoni
omwe amapangitsa kuti thupi lisinthe m’makhalidwe ndi m’zikhumbokhumbo.
Zimatheka nthawi zina kudzimva mphamvu kwambiri ndipo nthawi yosakhalitsa ndi
kudzimva kufooka. Kusinthasintha kwa m’thupiku ndi kwabwinobwino.
•
Panthawi yotha msinkhuyi, anyamata komanso atsikana amakhala ndi
chikhumbokhumbo chogonana. Chikhumbokhumbochi chimaonekera mu kusinhtha
kwa m’thupi monga kuthamanga kwa mtima ndi/kapena kuwala kwa nkhope ndi/
kapena ziwalo za kumaliseche zikakhudzidwa. Nthawi zina anyamata amalota akagona.
Izi zimaoneka m’kunyowa kwa zofunda chifukwa chodzithira umuna ndipo n’chifukwa
chake zimenezi zimatchulidwa kuti “maloto onyowa”. Chikhumbokhumbo cha usikuchi
chimachitikanso mwa atsikana koma chifukwa sipamakhala kudzikodzera n’chifukwa
sizimaonekera kwambiri. N’kofunika kudziwa kuti chikhumbokhumbochi komanso
malotowa ndi zabwinobwino ndipo ndi chizindikiro cha thupi labwinobwino.
•
Pa nthawi yotha msinkhu, anyamata komanso atsikana amanyadira kusinthika komwe
kumachitika pathupi lawo. Kusintha komwe kumachitikaku ndi chizikiro choti munthu
wakula ndipo n’chosalakwika kunyadira kukula. Anyamata ndi atsikana nthawi zina
amachita manyazi ndi kusintha kwina kwa thupi lawo. Zimenezi zimachitikira aliyense
ndipo pakapita nthawi zimatha.
•
Pa nthai yotha msinkhuyi, pamakhala kusintha kwina kowonekeratu mwa anyamata ndi
atsikana. Atsikana tsopano atha kutenga mimba ndipo nawo anyamata atha kupereka
mimba. Tikuyenera kudziwa kuti kukhala okonzeka kutenga mimba kuthupi ndi zosiyana
kwambiri ndi kukhala okonzeka kutenga mimba m’maganizo. Fotokozani kuti kalasi
idzakambirana zambbiri za izi m’phunziro la, “Kodi Makamaka Mimba Imatengedwa
Bwanji?”
4. Gawani ophunzira kukhala m’magulu a anthu asanu, amuna pawokha akazinso pa okha.
Perekani mapepala osalembapo ndipo pagulu lirilonse ajambule chithunzi cha thupi la
mnyamata kapena mtsikana amene akungotha kumene msinkhu. Magulu a atsikana ajambule
mtsikana ndipo anyamata ajambule mnyamata. DZIWANI: ngati gulu la ophunzira anu pali
gulu limodzi la anthu (amuna /atsikana) okha ndiye muuze magulu ena ajambule zagulu la
anthu lomwe palibewo n’cholinga chokhala ndi zithunzi za mnyamata komanso mtsikana.
42
5. Gawani zolembedwa zokhuza “Kusintha kwa Thupi la Mtsikana Akamatha Msinkhu” ndi
“Kusintha Thupi kwa Mnyamata Akamatha Msinkhu”. Afunseni ophunzira kuti afananitse
zomwen ajambula ndi zithunzi zomwe mwawapatsazi. Auzeni kuti munthu wamng’ono
wachiwiri kuchokera kumanjayo ali pa chithunzipo ndi amene amakhala ali mkati mosintha
msinkhu. Afunseni awone ngati pali kusiyana kulikonse pakati pa zithunzi zinayizo.
6. Funsani ophunzira ngati zosintha zomwe zalembedwa m’munsi mwa zithunzizo zingachititse
manyazi munthu. Mwanjira yanji mmene zingachititsire manyazi? Kodi achinyamata
anayamba asekedwapo chifukwa cha kusinthikaku? Ndi ndani? N’chifukwa chiyani munthu
wina angaseke mnzake chifukwa cha zinthu zomwe ndi zabwinobwino? N’chifukwa chiyani
wachinyamata angaseke wachinyamata mnzake pa zinthu zoti zikuchitikira onse?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Tsimikizirani kuti kusinthika komwe kumachitika m’thupi la munthu pamene watha msinkhu
ndi kwabwinobwino ndipo zimaonetsera thupi lolongosoka (kutanthauza kusintha mu
kamvekedwe ka mawu, kusinthasintha kwa m’maganizo, kukula kwa mabere ndi zina) ndipo
akumbutseni ophunzira kuti aliyense wa iwo kusinthaku kumachitika pa nthawi yake yake.
2. Apempheni ophunzira kuti azilimbikitsana pa nthawi yotha msinkhuyi.
3. Malizani powauza achinyamata za ubwino wa kutha msinkhu.
4. Pali mfundo zina zabodza zokhudza zomwe zinafotokozeredwa mu notsi za “Mmne
tingayankhulirane ndi achinyamata nkhani zokhudzana ndi kugonana” zomwe zaikidwa
kumapeto kwa gawoli. Chonde adziwitseni achinyamata za komwe angapite kukaphunzira
zambiri zokhudzana ndi kutha msinkhu komanso kusiyanitsa nkhambakamwa ndi mfundo
zenizeni.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
43
Mmene tingayankhulirane ndi achinyamata
pa nkhani zokhudzana ndi kugonana.
1. Vomerani mawu aliwonse ngakhale olawula. Ngakhale funso litakhala ndi mawu olawula
kapena osakhala bwino mvetserani ndipo akamaliza libwerezeni funsolo pogwiritsa ntchito
Chichewa cholondola.
2. Nenani kuti simukudziwa, ngati simukudziwadi. Ngati funso laperekedwa mkati mwa
gawo ndipo wotsogolera sakudziwa kuti ndi zoona kapena ndi zabodza, lilandireni funsolo
ndipo lonjezani kudzapereka yankho lake mu phunziro lotsatira mukakapeza yankho.
3. Musazipangitse kukhala zovuta. Osapangira zinthu kuti akutameni kapena kuwaopseza
ophunzira. Fotokozani m’chichewa chomveka bwino kuti asavutike kumva.
4. Yesani kuyankha funso lenileni lomwe likuyenera kuyankhidwa. Nthawi zina mafunso
amafunsa maganizo chabe a munthu (monga “Zimakhala bwanji anthu akamapsopsonana?”)
malo moyankhula mfundo zovuta kuzifotokozera kapena zoti ndi zabodza (monga “nthawi
zonse zimasangalatsa.”) yesani kuyankha funso lenileni lomwe linayenera kufunsidwa
monga (kuchita manyazi kapena kuchita mantha) ndi umboni wake. Mungathe kunena kuti
sizachilendo kukhala okhudzika kwambiri ndi nkhani za kugonana kapena chiwerewere koma
mfundo yoyenera kugwiritsa ndi yakuti:
a. kuvomerezana (kutanthauza; onse akufuna kupsopsonana)
b. Onse ndi okhwima ndi okonzeka (ana ang’ono angathe kukhala okhudzika ndi
zikhumbokhumbo za chiwerewere ndi kugonana, koma sindiye kuti ndi okonzeka
kuchita molingana ndi zikhumbokhumbozi)
c. Anthu awiriwa amakondana.
5. Osaweruza ndi kutengeka m’mayankhidwe anu. Kakamirani pa mayankho omwe ndi
olondola osati zomwe inuyo mumaganiza. Kukmbukirani malangizo okhudzana ndi amene
akutsogolera zokambiranazi kuti ayenera kukhala wosaweruza. M’kayankhidwe kanu
musamveke mnyozo kapena chiyamikiro chilichonse koma kungoyankha mopanda mbali.
6. Osayankha mafunso okhudzana ndi moyo wanu. Kakamirani ku mfundo osati kuyamba
kuyankha mafunso omwe pamapeto pake mupezeke mukufotokoza zam’moyo mwanu.
7. Masukani. Ngati mtsogoleri sali okonzeka kapena akuonetsa kumangika ophunzira
sachedwa kuzindikira. Ngati ili nkhani yokuvutani, chitani chilungamo. Auzeni achinyamata
simuli omasuka ndi mafunso ena ndipo ngati yokhudza kugonana imakuvutani nthawi zina
kuti muyikambe koma ndi nkhani yofunika kukambirana ndin kudziwa mfundo zolondola pa
nkhaniyi. Achinyamatawo amakumvetsetsani.
44
8. Landirani mafunso a “Nanga zitakhala kuti…” Iyi ndi nthawi yomwe achinyamata amakhala
ndi chidwi kwambiri pa nkhani yokhudza kugonana ndipo wophunzira ambiri amakhala ndi
mafunso a “Nanga zitakhala kuti…” powonjezera, pali maganizo ambiri abodza okhudzana ndi
kutha msinkhu.
Ena mwa mafunso omwe amafunsa nthawi zambiri ndi:
F: kodi mtsikana angatenge pakati ngakhale mamuna atapanda kukodzera?
Y: Inde. Pamakhala timadzi tomwe timatuluka kuchokera ku mbolo mamuna asanakodzere.
Timadzi timeneti timakhala ndi umuna; umunawu umapita ku dzira la mkazi ndipo mimba
ikhoza kutengedwa.
F: kodi ndi zoona kuti kubunyula kumayambitsa matenda kapena kusawona?
Y: kubunyula sikuyambitsa nthenda ina iliyonse.
F: kodi mtsikana angatenge mimba nthawi yoyamba kumene kugonana?
Y: ndi zotheka mtsikana ketenga mimba pa nthawi yake yoyamba kugonana. Nthawi iliyonse
yomwe mtsikana agonana ndi mnyamata amakhala pachiopsezo chotenga mimba. Kutenga
mimba kumatsogozana ndi kukhwima kwa dzira. Chifukwa choti mtsikana amakhwima kaye
dzira lake asanapange msambo, ndi zothekanso kutenga mimba asapange msambo wake
woyamba. Nthawi iliyonse mtsikana wagonana ndi mwamuna akhoza kutenga mimba.
F: Kodi ngati mnyamata watota kapena walota ndipo sanagonane ndi mkazi aliyense
angadwale kapena kukhala wosabereka?
Y: ngati mnyamata watota kapena walota, sakuyenera kugonana kapena kubunyula. Ndipo
ngati sapanga zimenezi sikuti amadwala kapena kukhala wosabereka. Kutota kapena kulota
ndi zizindikiro za thupi la bwino bwino osati kuti munthu agonane ndi mnzake.
45
Kusintha kwa thupi la mtsikana akamatha msinkhu
•
•
•
•
•
•
•
•
•
•
46
Kumera tsitsi mkwapa ndi malo ena obisika
Kukula thupi
Kuchuluka mphamvu
Thupi limasintha kaonedwe
Chiuno chimakula
Nthiti zimacheperapo
Mabere amakula
Amayamba msambo
Nkhungu limakhala la mafuta ndipo amayamba ziphuphu
Kuwonjezera kwa thukuta/mfungo la m’thupi
Kusintha kwa thupi la mwamuna akatha msinkhu
•
•
•
•
•
•
•
•
•
•
•
Kumera tsitsi ku mkwapa, ku malo obisika, pa nkhope ndi pa mtima
Kukula thupi
Kuchuluka mphamvu
Mapewa amakula
Amakakhala ndi minyewa yambiri
Mawu amayamba akulu
Mbolo imakula
Machende amakula
Nkhungu limakhala la mafuta ndipo amayamba ziphuphu
Kuchuluka thukuta ndi mfungo la m’thupi
Amayamba kulota ndi kutulutsa umuna
47
Gawo 8
Thupu langa likusintha-Ndiri Bwinobwino? – Gawo 2
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Gawoli lifufuza mmene kusinthika m’maganizo kwa achinyamata akamatha
msinkhu kumachitikira. Ophunzira aone mmene angathandizirane pa
nthawi yomwe akutha msinkhu.
Zolinga zaphunziro:
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kuzindikira zosowekera zam’maganizo akamathera msinkhu.
2. Apeze njira zomwe ophunzira angathandizirane wina ndi mnzake
pamene akutha msinkhu.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunkira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni notsi zolembapo kuti “Njira
zothandizira amnzawo kukhala odzikhulupirira okha”.
99 Unikani zolembera zoonjezera za “Njira zothandizira amnzathu
kukhala odzikhulupirira okha” ndi njira zina za momwe anyamata ndi
atsikana angathandizirane pa nthawi yomwe wina watha msinkhu.
99 Unikani ndi kuzindikira zolemba zoonjezera zomwe zili m’gawo
7 zonena za “Mmene tingayankhulire ndi achinyata zokhudza
kugonana”.
Ntchito 1: Kodi ndimamva bwanji za kutha msinkhu
Mphindi 30
1. Akumbutseni ophunzira za phunziro lomwe langotha lokhudzana ndi kusinthika kwa thupi ndi
maganizo pamene munthu akutha msinkhu. Mwachitsanzo, tinakambirana kuti kusinthaku
ndi kwabwinobwino komanso nthawi zina ena amachita nako manyazi. Funsani wina anene
chimodzi mwa zochititsa manyazi zokhudzana ndi nthawiyi? Tinakambanso kuti nthawi zina
achinyamata amatha kusekana za kusintha kwa m’thupi lanzawo. Malizani kuwakumbutsa
kuti tinakambirana za mmene tikuyenera kudziperekera pa kuthandizana wina ndi mnzake
pa nthawi yomwe tikutha msinkhuyi. Auzeni kuti phunziro ili liwathandiza nzeru zomwe
angagwiritse ntchito pothandizana wina ndi mnzake.
2. Gawani ophunzira m’magulu ang’oang’ono, anyamata pawokha, atsikana pawokhanso. Kagulu
kalikonse kakambirane izi:
48
•
•
•
•
•
•
Zomwe amaziopa kwambiri kuchokera kwa anyamata ndi atsikana a msinkhu wawo
zokhudzana ndi kutha msinkhu? (Ena mwa mayankho ake akhale oti: kunyowetsa
yunifolomu yawo ndi msambo n’kusekedwa; kuopa kutota pakati pa atsikana
n’kusekedwa ndi zina zambiri).
Ndi chiyani chofunikira pa nthawi ngati imeneyi?
Ndichiyani chochititsa manyazi pa nthawi ngati imeneyi?
Ndichiyani chokhudzana ndi nthawi imeneyi chomwe ophunzira amnzathu angachite
chomwe chingatithandize?
Chinayenera kuchitika ndi chiyani m’nthawiyi kuti zikhale bwino?
Mwachindunji, ndi chiyani chomwe ophunzira, osiyana nawo ziwalo, angawathandizire
mu nthawi yomwe akutha msinkhuyi?
3. Funsani gulu lirilonse kuima pamodzi ndi kufotokoza zomwe akambirana ku gulu la amnzawo
losiyana nawo ziwalo.
4. Mtsogoleri awombe mkota wa zonse zofanana zomwe ophunzira anena mwachitsanzo,
•
•
•
Osanyoza
Osaseka
Kuzindikira kuti onse akudutsa mofanana, uktha msinkhu, ndipo akuyenera kuthandizana
wina ndi mnzake
5. Gawani “Njira zokhala zothathizirana kukhala odzikhulupirira”. Oanani chitsanzo chilichonse.
Ntchito 2: kudzipereka
Mphindi 10
1. Ikaninso ophunzira m’magulu a anyamata okhaokha ndi atsikana okhaokha ngati mmene
anakhalira poyamba paja..
2. kutengera pa zokambirana za m’Ntchito 1, funsani ophunzira kupanga ndi kugwirizana
malonjezo awiri amene adzayetse kuwasunga pofuna kupanga kutha msinkhu kukhala nkhani
yopepuka kwa anzawo osiya nawo ziwalo. Funsani kagulu kalikonse kuti afotokoze zomwe
alonjeza ku gulu lonse.
3. Thokozani ophunzira chifukwa cha kulonjeza kwawo pa za kuthandizana n’choliga chopanga
nkhani ya kutha msinkhu kukhala yopepuka.
49
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Tsimikizirani mfundo yoti kusinthika kwa thupi munthu akamatha msinkhu ndi kwabwinobwino
ndipo aliyense amasitha thupi lake mosiyana ndi mnzake.
2. Funsani ophunzira ngati akudzipereka kuthandizana m’nthawi kudzera mu maluso atsopano
omwe aphunzirawa.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali pa zokambiranazi.
2. kambiranani za mmene phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
50
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Njira za mmene tingathandizirane kukhala odzikhulupirira
•
Kuyamikirana wina akachita bwino ndi kunena zomwe zimatisangalatsa pa moyo wa
mnzathuyo.
•
Kudziwa za zinthu zomwe timazichita bwino ndi kukumbukira za zimenezi zinthu zikakhala
sizikutiyendera.
•
Ngati amnzathu achita zinthu zomwe sizikutisangalatsa, tikuwauza mwaulemu mmene ife
tikufunira kuti zinthu zikhalire.
•
Sitikudzitichitira nkhaza tokha. Aliyense amalakwitsa ndipo tikuyenera kuphunzira kuchokera
pa zimenezi.
•
Tikuthandizana ndi kulimbikitsana zikakhala kuti zasokonekera.
•
Tikugawana nzeru ndi kuphunzitsana pa masamu.
•
Tikulimbikira pa phunziro lililonse.
•
Sitiseka ndi kunyoza amnzathu m’zinthu zomwe zimawakwiyitsa.
•
Tikudzikhulupirira tokha kuti tingathe kukwanitsa, chinthu chimodzi pa nthawi yake.
•
Tikumverana ndi kuvomerezana wina ndi mnzake ngati anthu ofunikira.
•
Tikuganizira za zinthu zomwe takwaniritsa kale m’moyo wathu.
51
GAWO 9
Kodi Mimba Imayamba Bwanji Kwenikweni?
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira aonenso zithunzi zokhunza uchembere wabwino ndi pakati.
Zolinga Za Phunziroli: Pomaliza pa gawoli, ophunzira athe:
1. Kufokozera mmene ziwalo zoberekera za abambo komanso amayi
zimagwirira ntchito.
2. Kufotokozera mmene kutenga mimba kumachitikita.
3. Kufotokozera msambo.
52
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunkira:
99 Bolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Zithunzi komanso kufotokozera mmene msambo umachitikira,
ziwalo zoberekera za amyi komanso abambo ndi mmene mamba
imachitikira.
99 Zindikirani za notsi zokhuza “Kodi tingalankhule Bwanji ndi
Achinyamata Zokhudza kugonana”, (Onani gawo 7).
99 Potengera kupezeka kwa akatswiri a za uchembere wabwino
mderamo, angathe kupempha akatswiri ochokera kwina kuti
atsogolere gawoli. Komabe, onetsetsani kuti katswiriyo katakwedi
pa nkhaniyi KOMANSO womasuka kugwira ntchito ndi achinyamata
mosaweruza komanso mwaulemu pankhani zokhudza kugonana.
99 Zithunzi zikhale zokonzeratu. Ngati nkotheka, perekani zolembera
zoonjezera kwa ophunzira aliyense. Khalani odziwa bwino za zithunzi
za ziwalo zoberekera za abambo komanso amayi ndi matanthauzo
ake munthawi yake kuti mukadziwitse ophunzira za mmene ziwalo
za abambo ndi amayi ziliri, mmene mimba imachitikira, komanso
msambo. Werengani mfundo zotsogolera pachithunzi chilichonse.
99 Khalani okonzeka kugawana ndi ophunzira zinthu zimene
zingawathandize kuphunzira bwino zokhunza mimba. Zinthunzi
zingathe kukhala zolemba kapena wamkulu wokhulupirika yemwe
ali ndi uthenga wolondola pa nkhaniyi.
99 Pali mbali zina za gawoli zomwe zifunike kutengera chikhalidwe
komanso kusinthidwa moyenerera. Mwa chitsanzo, mitu yambiri
siyikukambiranidwa mmagulu ophatikiza amuna ndi akazi. Sinthani
gawo molingana ndi chikhalidwe cha kuderako.
Chochitika Choyamba: Zithunzi Zokhunza Kubereka
Mphindi 30
1. Kumbutsani ophunzira kuti pa nthawi yakutha msinkhu, akazi amayamba kusamba
kutanthauza kuti angathe kutenga pakati. Nthawi ya kutha msinkhu, anyamata amayamba
kupanga umuna ndipo angathe kupereka pakati kwa akazi. Kumbutsani ophunzira kuti
kusinthaku ndi kwabwinobwino mmoyo, bwinobwino ngati mmene analekera kukwawa ndi
kuyamba kuyenda mmene anali ana ang’ono. Akumbutseninso kuti kutha kutenga pakati
sikukutanthauza kuti ali okonzeka kutero mziwalo zawo, mmaganizo awo komanso m’chuma
chawo.
2. Afunseni ophunzira ngati akudziwa mmene akazi amatengera pakati, kapena mmene ana
amapangidwira.
3. Onetsani zithunzi ziwalo zoberekera za abambo ndipo fotokozerani. Mfundo zofunikira ziri
pamodzi ndi zofotokozerazi.
4. Onetsani zithunzi za ziwalo zoberekera za amayi ndipo fotokozerani. Mfundo zofunikira ziri
pamodzi ndi zofotokozerazi.
5. Onetsani zithunzi za msambo ndipo kufotokozerani. Mfundo zofunikira zili pamodzi ndi
zofotokozerazi
6. Onetsani zithunzi za “Mmene mimba imachitikira” ndipo fotokozerani za mimba. Mfundo
zofunikira zili pamodzi ndi zofotokozerazi
7. Perekani nthawi yayitali ya mafunso kuchokera kwa ophunzira.
Chochitika Chachiwiri: Chinthu China
Chatsopano Chokhunza Kubereka
Mphindi 10
1. Funsani ophunzira kukhala awiri awiri amuna okhaokha komanso akazi okhaokha ndipo
agawane zomwe aphunzira lero zokhunza msambo komanso kubereka.
2. Funsani ophunzira kugawananso ndi nzawoyo mmene uthenga watsopanowu ungapititsire
patsogolo umoyo wawo komanso tsogolo lawo.
3. Auzeni ophunzira kugawana ndemanga zawo ndi gulu lonse. Osakakamiza munthu kupereka
ndemanga yake; zikhale kudzipereka kwa munthuyo basi.
53
Kuomba Mkota
Mphindi 5
1. Thokozani ophunzira chifukwa cha kutenga mbali m’kukambirana mutu womwe kawirikawiri
umachititsa manyazi koma wofunikira kwambiri.
2. Kumbutsani ophunzira kuti ngakhale mimba ndi chinthu cha bwinobwino ndipo angakhale
othekera kutenga mimba kapena kupereka mimba, ali aang’ono kwambiri.
3. Uzani ophunzira kuti “Thupi lanu (paliponse) ndilanu: mulilemekeze, kuliteteza, komanso
kulemekeza ndi kuteteza anzanu.”
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali pa zokambiranazi.
2. Kambiranani momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
54
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTI/MITU yodzakambirana.
Ziwalo Za Abambo Zoberekera
Ziwalo Za Abambo Zoberekera
Ziwalo Zapanja Pa Thupi:
Mbolo ili ngati paipi yomwe imatha kulimba kapena kutota; sichedwa kusintha ikagundidwa. Mutu
wake ndiye womwe umasintha mwachangu ndipo umatchingidwa ndi khungu kwa amuna omwe
sanajandulidwe. Mbolo ndi yomwe imakhala ndi njira yomwe mikodzo ndi umuna umadzera.
Mbolo ndi yomwe imapereka umuna kwa mkazi nthawi yogonana.
Machende ndi kathumba komwe kamakhala m’munsi mwa mbolo ndipo mkati mwake mumakhala
timipira. Mu timipirati mumakhala umuna ndipo umatetezedwa ku kutentha kapena kuzizira
ndimachendewa.
Ziwalo za m’kati:
Machende ndiwo mibulu iwiri yonga mazira a nkhuku yopezeka kutsogolo komansopakatipa
ntchafu ndipo imakhala mkati mwa thumba lawo.tchende lirilonse limapanga ndi kusunga ukala
umene umakumana ndi dzira kuti mimba iyambe mkazi akatha msinkhu. Tchende limapanga
ukala wa ulamuliro umene umapangitsa mwamuna kukula mwa umuna (mawu a besi, ndevu)
ndinso nyele.
Pambali pa tchende pali njira zing’onozing’ono zopingizana za ukala.awa ndi malo omwe ukala
umapangidwa, kusungidwa ndiponso kutulutsidwa panthawi yogonana. Njira zaukala ndizo
ziwiri zimene ntchito yake ndi kutenga ukala kuchoka kumene umapangidwa kupita munjira ya
mkodzo ndi ukala.
Timatumba taukala tilipo tiwiri ndipo timatulutsa timadzi tomwe ndi mbali imodzi ya ukala
(semen) Ukalawu umakhala woyera ngati mkaka ndipo ndi m’mene timadzira tachimuna (umuna)
umadutsira. Ukala umathandiza kuti umuna uyende bwinobwino komanso ukhale wathanzi.
Dzira lina lotchedwa “Prostate Gland” pachingerezi limatulutsa timadzi tomwe ndi mbali imodzi
ya ukala. Pamusi paderali pali mnofu umene umatchitchiriza umuna kugwera munjira yomwe
igapangitse umunawo kutuluka (urethra) pokhapokha ndi nthawi yothira umuna. Mnofu omwewu
umateteza kuti mkodzo usamatuluke limodzi ndi umuna pokodzera. Dera la “prostate gland”
ndi dera losachedwa kuzindikira kusintha komwe kukuchitika kwa ilo ndipo ndi malo obweretsa
chisangalalo chachikulu nthawi yogonana. Chikhodzodzo ndi chiwalo chokhala ndi mphako
m’mene mkodzo umasungidwira.
55
Ziwalo za abambo zoberekera
56
Ziwalo zobelekera za munthu wamkazi
Ziwalo zowoneka za kunja:
Ziwalo zoberekera zakunja za amayi zimatchedwa bumbu. Ziwalo zimene zimapanga bumbu ndi izi
makutu akulu ndi ang’ono akumaliseche, nkongo ndi nyini. Makutu akumaliseche amatetezedwa
ndi kuvindikira khomo la nyini. Mmilomo yankati ndi yakunja imakumana pamwamba pa
malisechehe .
Mkati mwa makutu amenewa ,muli kanyama kangati chala kotchedwa nkongo kamene
kanapangidwa ndi khungu longa la mbolo ndiko kamapangitsa nyere. Nkongowu ntchito yake
ndi yokhayo yobweretsa nyere ndi kukwaniritsidwa kwa mkazi.
Nyini ndi malo omwe amuna amalowetsa mbolo yake panthawi yogonana. Ndiwo malo omwe
nsambo umatulukira ngakhalenso mwana pa nthawi yobadwa.
Ziwalo za mkati:
Mayi aliyense amabadwa ndi mazira mazana ambiri m’mimba mwake. Mazirawa ndi ang’onoang’ono
kwambiri motero kuti ndi kosatheka kuwaona ndi maso.
Njira yamazira imalumikiza kopangira mazira ndi chibelekero. Dzira likatulutsidwa kuchoka
kolipanga, limayenda mnjirayi mpaka pa malo pomwe likuane ndi umuna kapena ukala.
Chibelekero ndi malo amene dzira lomwe lakumana/lafayidwa ndi ukala limakhala litadutsa mu
njira yakeyo. Chibelekerochi chimakhala chitakonzeka bwino pozisandutsa malo a wofuwofu
mkati mwake. Ngati mtsikana wagonedwa posachedwa kapena kuti m’masiku ochepa, dzira
lisanatulutsidwe, panthawi imenelikufika mu njira mwake zimatheka kukumana ndi ukala
omwe umadikilira.nkumanowu ukachitika dzira lofayidw a ndi ukala limasunthira mchibelekero
nkumatilira m’mbali mwachibelekero. Ikatero ndiye kuti mimba yayamba. Ngati dzilaro silikumana
ndi ukala mimba siyimachitika choncho palibe kukonzekera kulikonse kumene chibelekero
chimachita kuti chitetedze dzilaro choncho limanyamulidwa pamodzi ndi chiwofuwofu chonse
cha mkati mwa chibelekero limodzi ndi magazi komanso madzi ena a mthupi. Zimenezi zimayenda
ndi kutulukira pa khomo la chibelrkero mpaka panja pa nyini. Kutuluka kwa zinthu zimenezi
kumatchedwa msambo. Msambo umatuluka pang’onopang’ono pakati pa masiku atatu ndi asanu
ndi awiri. Khomo lachibelekero ndi lomwe limakumaniza chibelekero ndi nyini.
57
Ziwalo zoberekera za Amayi
58
Mmene msambo umachitikira
59
Msambo
Msambo umachitika kamodzi pa mwezi kwa amayi ambiri, n’chifukwa chake umatchulidwa kuti
“kumwezi.” Nthawi zambiri, umatenga masiku osachepera atatu komanso osaposera asanu nd
awiri. Iwo uli chizindikiro chakuti mtsikana kapena mayi angathe kutenga mimba ngati agonana
ndi munthu wamamuna.
Chimayambitsa msambo n’chiyani? Msambo umachitika ngati mtsikana asali ndi mimba. Pamapeto
pa pa msambo uliwonse, chiberekaro chimayambanso kukonzekera kulandira kadzira komwe
kakumana ndi umuna. Ngati kadzira komwe kakumana ndi umuna sikafika muchiberekero mpaka
masabata awiri kapena atatu, chiberekero chimayamba kutulutsa magazi omwe anachikutira uku
ndiko kusamba.
Msambo umayamba mosiyanasiyana kwa anthu osiyana monga ena amatha msinkhu msanga
kuposa anzawo. Atsikana ena amayamba kusamba ali ndi zaka zisanu ndi zinayi kapena khimi,
ena sayamba kusammba mpaka zaka zingapo zitatha. Mzimayi amadziwa kuti wayamba kusamba
ngati waona magazi akutuluka kumaliseche kwake. Magaziwa samatuluka ngati madzi apa mpopi,
amatuluka pang’onopang’ono, ngati kudontha. Nthawi zambiri panthawiyi amazindikira kunyowa
kwachilendo pa panti wake chifukwa cha magazi omwe agwera pa pantipo. Ichi n’chifukkwa chake
kuli kofunika kumadziwa nthawi imene amasamba pamwezi kuti adzivaliratu zinthu zozitetezera
kuti asaonongere zovala.
Msambo ndi nthawi yomwe imayambira tsiku lomwe mayi wayamba msambo wake kukafika pa
tsiku loti msambo wina uyambikanso tsiku lotsatiralo. Izi zimachitika pafipifupi mwezi uliwonse
ndipo n’chifukwa chake amati “kumwezi”. Kusiyana kwa nthawi yomwe msambo wina wachitika
kufiki nthawi yakuti wina uchitikenso zimakhala zosiyana mwa m’zimayi aliyense. Kwa ena
pamatenga masiku 21 (kapena kucheperapo). Kwa ena, pamafika mpaka masiku 35 kuti msambo
wina uchitike. Kusakhazikika kwa masiku a msambo kumachitika kwambiri kwa atsikana omwe
angoyamba kumene kumapanga msambo. Zimatengabe ka nyengo kuti thupi lizolowere
kusinthika kwa m’thupiku. Mwachitsanzo, mtsikana atha kupanga msambo masiku ofanana kwa
miyezi iwiri kenaka mwezi wina osapanga msambo, kapena kupanga msambo wina patangopita
masiku ochepa msambo wina utangotha kumene. Nthawi ya msambo yake imakhazikika ngakhale
nthawi zina zimapitirira mpaka akakula. Nthawi zina amatha kudotha magazi kwa tsiku kapena
masiku awiri mkati mwa msambo. Pamenepa palibe chodandaulitsa. Nkhawa ndi matenda
zimatha kusokoneza nthawi ya kachitidwe ka msambo. Msambo ndi nthawi.
60
M’mene mimba imachitikira
61
mmene mimba imayambira
Kufayiridwa kwa dzira kumachitika pokha pokha ukala wakumana ndi dzira la mkazi. Miyanda
ya ukala imathiridwa mu nyini pa nthawi yogonana. Mwamuna akalowetsa mbolo yake mu
nyini amathira ukala . Ukalawu umayamba kusambira kupita m’chibelekero kudzera pa khomo
pachibelekeropo. Thupi la mayi limathandiza kuchengeta ukalawu mpaka ukafike m’njira yodutsa
mazira. Ngati dzira lokhwima (kapena mazira akucha bwino potengera mapasa) likupezeka
m’njiramu mnkumano umachitika. Ngakhale kuti mazana a ukala amathiridwa mu nyinimo,
umodzi okha wa machawi ndi omwe umapanga nkumano ndi dzira. Ukala ungathe kukumanabe
ndi dzira ungakhale utatha masiku asanu chipangireni zogonana. Ngati dzira lafayiridwa, limapita
m’chibelekero kudzera mu njira ya mazira komwe limayamba kukula mwa mwana.
Kudzalidwa kwa mwana kumachitika dzira likamamatira m’mbalimbali mwa chibelekero
cha m’zimayi. Mmenemu mumapazeka zakudya zofunikira zimene mwana wopangidwayo
amagwiritsa ntchito kufukira pokakhala mwana weniweni. M’zimayi sapanga msambo panthawi
yomwe ali ndi mimba chifukwa chibekero sichinyanyala za mkati mwake zomwe chimataya pa
msambo. Dzira lodzalidwalo limakakhala m’chibelekero ndi kumakula kwa miyezi isanu ndi inayi
khanda lisanapangidwe. Kenako limatuluka mthupi la mzimayi(m’chibelekero) mu njira yotchedwa
kubeleka.
62
Gawo 10
Thumba la katengedwe ka HIV
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Zolinga zaphunziro:
Nthawi:
Pogwiritsa ntchito zida zogwiritsa ntchito pasewero kuchokera m’thumba
la katengedwe ka HIV, ophunzira akambirana m’magulu ang’onoang’ono
ayesera kuthetsa mabodza okhudzana ndi kachilombo ka HIV ndi
kulimbikitsa mfundo zoowa zokhudzana ndi kachilombo ka HIV.
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kuzindikira mfundo zoopsa zokhudzana ndi kachilombo ka HIV kwa
achinyamata.
2. Kufotokoza njira za momwe angapewere kachilombo ka HIV.
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
Mphindi 40
99 Phunziroli lisanayambe, pezani ndi kuika “m’thumba la katengedwe”
zinthu zotsatirazi:
99 Kapu yomwera madzi; chithunzi cha mwamuna ndi mkazi atagwirana
manja; chipanda chopanda mowa; pepala la mawu olembedwa kuti
“kudziletsa”; kondomu ya mwamuna kapena chikutiro cha kondomu;
chidole; ndalama; mankhwala olerela; mankhwala a nsikidzi; mpira;
foni; diploma; mphete ya ukwati; chithunzi chosonyeza mwambo wa
chinamwali; chithunzi cha mkazi yemwe ali ndi diso lakuda.
99 Ngati chimodzi mwa zinthuzi palibe, tikhoza kungojambula.
99 Onjezeraninso thumba lina lomwe mukhalemo mfundo zabodza
zokhudzana ndi HIV. Mwachitsanzo, mu Madera ena mumakhala
bodza lapakati pa sing’anga ndi kachilombo ka HIV. Mu Madera
ena, pamakhala bodza lopanda umboni lokhudzana ndi momwe
kachilombo ka HIV kamafalikira.
99 Unikaninso zolembera zoonjezera za “zinthu zathumba la katengedwe
ka HIV ndi mgwirizano wake ndi Matenda opatsirana pogonana
ndiponso kachilombo ka HIV” zomwe ziri kumapeto kwa gawoli.
Ntchito 1: Zida zachionetsero
1. Gawani ophunzira m’magulu a ophunzira atatu kapena anayi pagulu.
63
2. Yendetsani thumba lija m’magulumu. Funsani ophunzira m’magulumu kuti atole chinthu
kuchokera m’thumbalo mosayang’anamo. Yendetsani thumbalo mpaka zinthu zonse ziri
m’thumbalo zitatha.
3. Funsani gulu lirilonse kuti likambirane za chinthu chomwe asankhacho kuti chikugwirizana
bwanji ndi kachilombo ka HIV kapena matenda opatsirana pogonana.
4. Funsani ophunzira kuti afotokoze zomwe akambirana m’magulumo ku kalasi lonse za momwe
chinthu chomwe anasankhacho chikugwirizirana ndi kachilombo ka HIV komanso matenda
opatsirana pogonana.
5. Konzani zina zilizonse zolakwika (gwiritsani ntchito notsi za “zinthu za m’thumba la katengedwe
ka HIV ndi mgwirizano wake ndi matenda opatsirana pogonana komanso HIV” zomwe zili
kumapeto kwa gawoli).
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Kumapeto kwa gawoli kuli kufotokozera za chinthu china chilichonse chomwe
chatulutsidwa kuchokera m’thumba muja mogwirizana ndi kachilombo ka HIV.
Komabe, achinyamata ali ndi luso lapadera ndipo akhoza kubweretsa mfundo zina
kuwonjezera pa zimenezi. N’koyenera kuti zilandiridwenso.
6. Awuzeni ophunzira za malo omwe angapite kuti akayezetse ndi kulangizidwa pa za matenda
opatsirana pogonana ndi kachilombo ka HIV.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Bwerezani mwachidule mfundo zofunikira zonse m’gawoli.
2. Uzani ophunzira kuti n’zosadabwitsa ndipo n’zabwinobwino kuti anthu ena amachita manyazi
komanso satakasuka ndi nkhani zokhudzana ndi HIV komanso matenda opatsirana pogonana,
koma mpofunika kupeza nzeru zolondola zokhudzana ndi nkhaniyi ngakhale njira zake
zitakhala zochititsa manyazi motani.
Phunziro Lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
64
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Zinthu za m’thumba la katengedwe ka HIV ndi mgwirizano wake
ndi Matenda opatsirana pogonana komanso kachilombo ka HIV
Kapu yomwera madzi; mpira; telefoni
•
•
Palibe kufalikira kwa kachilombo ka HIV komanso matenda opatsirana pogonana kudzera
m’kapu yomwera madzi, chotsekulira chitseko, foni, masewera ndi zina zotere. Zimenezi
zimatchedwa kukhudzana wamba. Kachilombo ka HIV ndi matenda opatsirana pogonana
safalikira kudzera mu kukumbatirana, kugwiritsa ntchito mpando umodzi ndi zina.
Zinthu zamadzi zomwe zimafalitsa matendawa ndi monga: magazi, umuna, ukazi ndi mkaka
wamawere. Malovu samafalitsa kachilombo ka HIV.
Chithunzi cha mwamuna ndi mkazi atagwirana manja
•
•
Anthu awiriwa pachithunzipo akuchepetsa kufalikira kwa kachilombo ka HIV ndi matenda
opatsirana pogonana chifukwa akugonana awiriwa basi
Kukhala ndi abwenzi angapo ogonana nawo pa nthawi imodzi zimawonjezera chiopsezo
chotengakachilombo ka HIV.
Chipanda chopanda mowa
•
•
•
•
Mowa umasokoneza kuganiza kwa munthu koyenera, kotero umatha kukupangitsa
zinthuzomwe zingakuike pachiopsezo chotenga kachilombo Ka HIV ndi matenda ena
opatsirana pogonana.
Mowa umachititsa mtsikana kukhala pachiopsezo chogwiriridwa. Ngakhale atakana kugonana
ndi munthu, mowa ungathe kumulepheretsa iye kukakamira pa chisankho chakecho.
Mwamuna amene waledzera samvera mtsikana akamukanira kugonana naye.
Anyamata ndi atsikana omwe aledzera amapanga zisankho mosaganiza zimene sangapange
ali osaledzera.
Mowa ungapangitse munthu kuyamba waiwala kaye za chidziwitso chomwe ali nacho pa za
matenda opatsirana pogonana komanso kachilombo ka HIV ndipo amatha kugwiritsa ntchito
kondomu molakwika kapena kuchita zomwe akadati sanaledzere sakadachita.
Kudziletsa
•
•
•
•
•
•
Kudziletsa ku m’chitidwe uliwonse wogonana ndi chisankho chabwino zedi kwa achinyamata.
Kudziletsa ndiye njira yokhayo yapamwamba zedi yopewera mimba, matenda opatsirana
pogonana ndi kachilombo ka HIV.
Kumawalola ophunzira kulimbikira maphunziro awo.
Achinyamata ayenera kukhala okonzeka pa za nthawi yomwe angayambe kugonana.
Achinyamata ayenera kupeza anzawo omwe angathe kuwalimbikitsa pa chisankho
chakudziletsa. Ayeneranso kudziwa zambiri zokhudzana ndi mimba ndi matenda opatsirana
pogonana ndi, kupewedwe ka mimba ndi kapewedwe ka matenda opatsirana pogonana.
Achinyamata ayenera kupeza chithandizo ngati wina akuwaumiriza kuchita nawo chiwerewere.
Kondomu ya amuna
•
Imathandiza kupewa kufalikira kwa matenda opatsirana pogonana komanso kachilombo ka
HIV pamene yagwiritsidwa ntchito moyenerera.
65
•
Makondomu ndi otetezeka.
Chidole
•
•
•
Kupatsirana kwa kachilombo ka HIV kuchokera kwa amayi kupita kwa mwana kumachitika
pamene mayi yemwe ali ndi kachilombo ka HIV apatsira mwanayo kudzera mu mkaka
wamawere, pobereka, ndi nthawi yomwe akutenga kumene mimba. Ngati mayiyo akumwa
ma ARV, pamakhala mwayi wonse woti mwanayo asapatsiridwe kachilomboko.
Njira yoyenera ya momwe mayi amene ali ndi HIV angayamwitsire mwana wake, zimadalira
chisankho cha mwini wakeyo komanso zinthu zomuzungulira iye. Kuyamwitsa mwana
mwakathithi kumafunika miyezi 6 yoyambirira kwa mayi amene ali ndi kachilomboko kupanda
apo kusinthanitsa ndi mkaka wina nthawiyi isanathe kumavomerezedwa ngati zili zotheka.
Ngati zili zotheka kusinthanitsa, amayi omwe ali ndi kachilombo ka HIV amalimbikitsidwa kuti
asamayamwitse ana awo mkaka wamawere.
Pali udindo waukulu womwe umafunika pamene wakhala bambo wa munthu ukadali
ku sukulu. Mwachitsanzo, bamboyo amakhala ndi nthawi yochepa yosewera ku bwalo la
zamasewera ndipo amafunika nthawi yambiri yogwira ntchito kuti apeze chakudya, pogona,
makhwala, zovala ndi zina zambiri zoti apereke kwa mwana ndi mayi amwanayo.
Ndalama
•
•
•
Amene alibe ndalama amatha kupanga zinthu zomwe zimawaika pachiopsezo chotenga
kachilombo ka HIV chifukwa chofuna kupeza ndalama. Mwachitsanzo, mtsikana atha kuchita
chiwerewere ndi munthu wamkulu, kapena kuchita chiwerewere mosadziteteza kapena
kusinthanitsa thupi lake ndi ndalama kapena chakudya.
Kusinthanitsa matupi ndi zinthu monga ndalama, zovala, sopo kuchitiridwa ubwino ndi zina,
kumaika atsikana pachiopsezo chifukwa choperewera mphamvu zokambapo maganizo awo
pa zakugonana modziteteza.
Ngakhale nthawi zovuta zimapangitsa anthu kupanga zisankho zomwe sakufuna, nthawi zina
anthu mwakufuna kwawo amatha kuchita m’khalidwe wogonanawo pofuna kupeza zinthu
zoti atha kukhala bwino bwino ngakhale atati alibe. Pali chiopsezo chachikulu chosinthanitsa
matupi
Njira ndi mapilitsi olerela
•
Njirazi zimathandiza kwambiri ku kapewedwe ka mimba koma sizimathandiza pa kapewedwe
ka kufalikira kwa HIV ndi matenda opatsirana pogonana.
Nkhanza
•
•
•
•
•
66
Nthawi zina achinyamata sakhala ndi mwayi wosankha kugonana kapena ayi kapenanso ngati
angagwiritse ntchito kondomu pakakhala kuti pali nkhaza zoumiriza wachinyamatayo kapena
waledzeretsedwa.
Achinyamata ayenera kumapewa kupita ku malo owopsa kapena ayenera kamakhala pagulu.
Ngati wachinyamata akuchita mantha kapena akuona kuti akukakamizidwa ndi munthu wina
ndi bwino kuwuza wamkulu wothandiza za mantha awo.
Anyamata ayenera kuganizira zochita zawo kwa atsikana komanso azimayi. Ngakhale ataona
abambo womwe amawapatsa ulemu akuchitira nkhanza mtsikana kapena mzimayi, iwo
akuyenera kukhala abambo ozindikira omwe angathe kusinthitsa m’khalidwe wa nkhanzawo.
Ngati mzimayi wagwiriridwa, ayenera kufunsa munthu wamkulu kuti apite naye kuchipatala.
Diploma
•
•
•
Aliyense atha kutenga kachilombo, ngakhale ophunzira kwambiri.
Kuphunzira kumapereka mwayi wodzakhala pabwino mtsogolo ndi ntchito zabwino.
HIV kapena mimba ndi kukhala mzibambo pamene sunakonzeke, zingathetse maloto a
maphunziro.
Mphete ya ukwati
•
•
•
•
•
Banja limamuteteza munthu ku kachilombo ka HIV ngati anthu onsewo ayezetsa, alibe
kacholomboko, ndipo akukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake.
Kwa ena, kudikira osagonana mpaka m’banja ndi mbali ya chipembedzo chawo.
Ena amaona kuti kugonana ndi kwaphindu kwambiri ngati kwasungidwira m’banja.
Patha kukhala kukambirana ngati zili zotheka kudikira mpaka mu banja- nkhaniyi ndi yofunika
kwambiri ndipo iyenera kulandiridwa ndi manja awiri.
Kwa atsikana achichepere, kulowa m’banja kukutanthauza mapeto a maphunziro awo ndi
chiyembekezo cha tsogolo labwino komanso kuwaika pachiopsezo cha HIV.
Chizindikiro cha chinamwali
•
•
•
Kwa zinamwali zomwe mumakhala mdulidwe, kachilombo ka HIV kangafalikire kuchokera kwa
yemwe ali ndi kachilomboko kupita kwa amne alibe ngati agwiritsa ntchito chida chimodzi
komanso chosawilitsidwa mokwanira.
Mduludwe wa amuna ngati utachitidwa molongosoka ndi motsata mwambo, kungathandize
kuchepetsa kufalikira kwa matenda a edzi.
Miyambo yachinamwali yomwe imalimbikitsa achinyamata kugonana ndi akuluakulu kapena
anyamata anzawo kapena kumwa mankhwala olimbikitsa kugonana angalimbikitse kufalikira
kwa kachilombo ka HIV/EDZI chifukwa chowalimbikitsa achinyamata kuyamba m’chitidwe
wogonana asanankhime.
67
Gawo 11
Kupanga zisankho zabwino
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira ayamba kudzikhulupirira okha pa maluso otha kupanga
zisankho zoyenera za m’moyo wawo, pamene akukumbutsidwa za
zisankho zina zomwe anapanga kale. Kudzera mu luso lachibadwa lotha
kupanga chisankho apanga ntchito yomwe iwunikire za zotsatira za
bwino komanso zoipa zomwe zimadza chifukwa cha zisankho zomwe
amapanga.
Zolinga zaphunziroli: Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kuzindikira kuti timapanga zisankho m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.
2. kudziwa kuti chisankho chirichonse chomwe chimapangidwa chiri
ndi zotsatira zake, zabwino kapena zoipa.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 bbolodi/choko kapena tchati/pentopeni
99 Werengani nkhani ya Beatrice ndi Oto mu ntchito 2 ndipo mudziwe
njira zingapo zopangira zisankho zomwe akukumana nazo.
Ntchito 1: Ndapangako Chisankho lero?
Mphindi 10
1. Funsani ophunzira kuti aganizire za tsiku la lero, kuchokera pa nthawi yomwe adzuka mpaka
panopa. Afunseni kuti aganizire zisankho zomwe apangapo.
2. Afunseni ophunzira kuti anene zisankho zimenezi. Tengani ndi kukambirana chisankho
chimodzi potengera yankho lomwe lakondedwa ndi aliyense. Mwachitsanzo, ndidya chiyani,
ndivala chiyani, ndiyankhule ndi ndani, ndidzere njira iti popita ku sukulu ndi zina zambiri.
3. Fotokozani kuti tsiku lirilonse pamakhala nthawi zosiyanasiyana zomwe timapanga zisankho
za zinthu zomwe tikuyenera kupanga.
4. Funsani ophunzira za chisankho chomwe akambirana m’mwambamu. Mwachitsanzo, njira
yoyenera kudzera popita ku sukulu. Funsani ophunzira anene mmene njira zomwe anatsata
popanga chisankho chawo. Zitsanzo za mayankho awo zingakhale: njira yomwe ndi yofulumira
ndi iti? Njira yomwe mnzanmga amafuna kudzera? Ndi njira yomwe ndidzera nthawi zonse?
68
Ngati ndimafuna kudzera kaye kumsika ndi zina zotero.
5. Fotokozani kuti ena amapanga chisankho kutengera pa zomwe angokhumba (ndikungomva
ngati ndiyende choncho kapena poti ndi mmene ndimayendera) pamene ena amapanga
zisankho kutengera pa zomwe aganiza (ndinadziwa kuti ndachedwa ndipo inali njira yachangu;
ndimafuna kuti ndiyiime kaye kumsika ndiye njira yake ndi yomweyo). Funsani ophunzira kuti
akambe maganizo pa njira ziwiri zopangira zisankhozi – kupanga zisankho pogwiritsa ntchito
mutu wathu kapena pogwiritsa ntchito mtima wathu.
6. Fotokozani kuti nthawi zina zilibe ntchito kuti wagwiritsa ntchito mtima kapena mutu wanumwachitsanzo, kuti tidya chiyani ngati chakudya cha mmawa koma nthawi zina ndi zofunika
monga ngati kuti mukwere galimoto limodzi ndi munthu wina kapena ngati mukuyenera
kulandira zinthu zabwino kuchokera kwa m’zibambo kapena kupita ku chisangalalo ndi
munthu wina komanso ngati n’koyenera kugonana ndi munthu wina wake ndi zina zotero.
7. Pamene chisankho chili chovuta kupanga pamafunika kuika mtima ndi maganizo ako onse
kuti upange chisankho cholondola.
Ntchito 2: Zisankho ndi zotsatira zake
Mphindi 30
1. Fotokozani kuti Ntchito yotsatira ndi ya masewera otchedwa “nthawi yopanga chisankho”
ndipo nd mwayi kwa ophunzira otha kuphunzira kutha kupanga zisankho zam’moyo pogwiritsa
ntchito mtima komanso maganizo awo. Fotokozani kuti muwerenga nkhani yokhudzana ndi
Beatrice ndi Oto.
2. Fotokozani kuti nthawi iliyonse yomwe mwasiya nkhaniyi ndi kuomba manja kawiri (PHWA,
PHWA) zikutanthauza kuti Beatrice ndi Oto akuyenera kuima ndi kupanga chisankho.
Ophunzira akambirana ndi kupanga chisankho m’malo mwa Beatrice ndi Oto.
3. Werengani: “mzibambo wina wachinyamata, dzina lake Oto, ayimitsa galimoto yake kuti
ayankhule ndi mtsikana wa sukulu dzina lake Beatrice, ndipo pamapeto pake amufunsa ngati
akufuna kuti amutenge pagalomoto”.
4. IMANI: Ombani m’manja kawiri (PHWA, PHWA) ndipo funsani ophunzira:
•
•
•
•
•
Ndi chisankho chanji chomwe Oto wapanga?
Ndi zotsatira zanji zabwino zomwe zingabwere ngati Beatrice atavomereza kukwera
galimotoyi?
Ndi zoopsa zanji zomwe zingadze ngati Beatrice atavomera kukwera galimotoyi?
Mukuganiza mtima mwake akumva chiyani?
Nanga mukuganiza kuti maganizo ake akumuuza kuti chiyani?
5. Werengani: “mtsikana uja avomera kukwera galimoto ndipo mzibambo uja amuuza mtsikanayu
69
kuti aime kaye pamowa kuti amugulireko mowa asafike kaye ku nyumba kuchokera ku sukulu.”
6. IMANI: Ombani mmanja kawiri (PHWA, PHWA) ndipo kambiranani ndi ophunzira:
•
•
•
•
•
•
Ndi zabwino zanji zomwe mtsikanayu angapeze atavomera kuti ayime kaye pamowapa
kuti amweko?
Ndi zovuta zanji zomwe zingadze ngati atavomera?
Ngati atagwiritsa ntchito zokhumba zake, mukuganiza kuti angatani?
Ngati ataganizira za kuipa ndi ubwino wa chisankhochi mukuganiza angati chiyani?
Nanga Oto? Ndi zisankho zanji zomwe akuyenera kupanga? Ndi zotsatira zanji zabwino/
zoipa zomwe zingadze chifukwa cha zisankho zomwe angapangezo?
Kodi nanga bwanji Oto atazindikira kuti walakwitsa kumukweza Beatrice galimotoyi ndi
kumuyitanira ku mowa? N’chifukwa chiyani angamve choncho? Nanga akuyenera kuti
atani tsopano?
7. Werengani: “mtsikana wa sukulu uja auza mzibambo kuti alola kupita kumowako ngati
akulonjeza kuti akangomwa botolo limodzi lokha kenaka ndikumapita ku nyumba. Mzibamboyo
avomera. Mu bar muja agula mowa umodzi wina aliyense kenaka iye adziyitanitsira wina wambiri
mpaka aledzera. Mtsikanayo ayesera kuthawa koma amugwira dzanja kumuletsa kuti asatuluke.
Kenaka mtsikanayu pamapeto pake akwanitsa kuthawa ndi kutuluka panja koma akaona kuti
kunja kwada ndipo ali pamalo posatetezeka. Tsopano akufunitsitsa kumapita kunyumba.”
8. IMANI: Ombani mmanja kawiri (PHWA, PHWA) ndipo afunseni ophunzira :
•
•
•
•
•
•
•
Kodi ndi nthawi ya chisankho yanji yomwe mtsikanayu wakumana nayo?
Ndi zina mwa zotsatira zabwino/zoipa zanji za zisankho zimenezi?
Kodi mtsikanayu apange chiyani tsopano?
Kodi inu mukadatani?
Mukuganiza n’chifukwa chiyani Oto anali wabwino poyamba paja kenako ndikusintha?
Kukadakhala kotheka kubwezeretsa nthawi m’mbuyo kwa Oto ndi zisankho ziti zomwe
anayenera kuzisintha kuti zisafike pomwe zafikapa?
Kodi Oto angadzatani mtsogolo muno kuti zisadzamucitikirenso?
9. Funsani ophunzira:
•
•
•
•
•
70
Ndi nthawi ziti zachisankho mu kaseweroka?
Ndi zisankho zanji zomwe Beatrice anapanga ndipo zotsatira za zisankho zakezo zinali
zotani?
Mukuganiza n’chifukwa chiyani anapanga zisankho zotero? Mukuganiza kuti anapanga
zisankho zimenezi moganiza ndi mutuwake kapena anangotsatira zomwe mtima wake
unkakhumba?
Ndi zisankho zotani zomwe Oto anaganiza, nanga zotsatira zake zinali zotani?
N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti Oto anapanga zisankho zimenezi? Kodi nanu
mukadapanga zisankho zotero? Kodi Oto anapanga zisankho moganiza bwino bwino
kapena anangotsatira zokhumba za mtima mwake?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Funsani ophunzira kugawana zomwe aphunzira kuchokera ku Ntchito ya m’gawoli.
Unikaninso kuti kupanga chisankho sikudalira zikhumbokhumbo zokha komanso kuganiza.
Zikuphatikizapo kiringalira za zotsatira zabwino/zoipa zomwe zingadze malingana ndi
chisankho chathu. Zikutanthauza kuganiza za zotsatira zomwe sungathe kuzilamulira
(mwachitsanzo, kumwa moledzera kwambiri kapena ayi.)
2. Funsani ophunzira za momwe akagwiritsire ntchito m’moyo wawo zomwe aphunzira m’gawoli.
3. Funsani ophunzira aliyense kudzipereka kuti adziomba kaye mmanja asanapange ( PHWA,
PHWA) ndi kulingalira kaye za zotsatira zoipa kapena zabwino zomwe zingathe kubwera pa
nthawi iliyonse yomwe akupanga chisankho m’moyo wawo.
Phunziro Lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana
71
Gawo 12
Kodi ndichite chiyani ndi zilakolakozi?
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira akambirane za ubale umene ulipo kapena kusowa kwa ubale
pakati pa chikondi ndi kugonana. Ophunzira anene zinthu zimene
munthu angachite kuti amuonetsera wina kuti akumukonda posachita
naye zogonana.
Zolingaza
maphunziro:
Potsiriza pa chigawochi ophunzira ayenera kuchita izi:
1. Kukambirana kusiyana kwa kugonana ndi chikondi.
2. Apeze njira zomwe zingaonetse chikondi posachita zogonana.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunkira:
99 Mumvetsetse nkhani ya Martina ndi Moffat, mu ntchito 2.
99 Ngati ophunzira amatha kuwerenga bwinobwino, alembe nkhani za
Tim/Mary; Martina/Moffat; ndi James/Gertrude pa bolodi. Mbali ina
ya bolodi alembe ziganizo izi:
• Awa awiri amkondana ndipo amachita zogonana.
• Awa awiri amachita zogonana koma sakondana.
• Awa awiri amkondana koma samachita zogonana.
Ntchito 1: Chikondi kapena kugonana
Mphindi 15
1. Werengani nkhani zotsatirazi kwa ophunzira kapena zilembeni pa bolodi ngati ophunzira
amatha kuwerenga bwinobwino:
•
•
•
72
Anzake a Tim amamuseka chifukwa sanayambe wachitako zogonana. Mary anatengeka
ndipo akufuna kuti ayesere ngati angathe kukwanitsa kuvina bwino pochita zogonana.
Tim wamuona Mary akupita kunyumba pochokera ku sukulu ndipo wamufunsa kuti
agonane naye. Iye wavomera.
Martina ndi Moffat amakondana kwambiri ndipo agwirizana kuti adikira kudzachita
zogonana akadzalowa m’mbanja. Amapeza njira zambirizowonetsera kuti amakondana
posachita zogonana.
James ndi Gertrude amakondana koma sangakwanitse kumanga banja. Akufuna
kumasangalala pa moyo wawo wokhuza kugonana tsono agwirizana kugwiritsa ntchito
kondomu nthawi zonse pamene akugonana
2. Mukatha kuwerenga nkhani, werengani ziganizo zotsatirazi kapena mulembe pa pepala
kapena pa bolodi ngati ophunzira amatha kuwerenga bwinobwino. Afunseni ophunzira
alumikize nkhani iliyonse ndi ziganizo zotsatirazi:
•
•
•
Awa awiri amakondana ndipo amagonana modziteteza.
Awa awiri amachita zogonana koma sakondana.
Awa awiri amakondana koma samachita zogonana.
3. Tsopano funsani ophunzira mafunso otsatirawa:
•
•
•
•
Nzotheka kuchita kugonana popanda chikondi?
Nzotheka kukhala pa chikondi koma osachita zogonana?
Kodi pali kusiyana kotani pakati pa chikondi ndi kugonana?
Kodi James ndi Getrude amaonetsera bwanji chikondi chawo kwa wina ndi mzake?
Ntchito 2: Ndondomeko yayitali
Mphindi 25
1. Agaweni ophunzira mu magulu a atsikana paokha ndiponso anyamata paokha.
2. Werengani: “Martina ndi Moffat amakondana koma sachita zogonana. Iwo amati anapeza
njira zimene zimaonetsera chikondi pa wina ndi nzake. Monganso Martina ndi Moffat, tsiku lina
mukhonza kudzakhala ndi chilakolako chofuna kumuonetsera munthu wina chikondi chanu mu
njira yina osati yogonana.”
3. Funsani gulu lirilonse litulutse ndondomeko ya zinthu zimene zingaonetsere munthu wina
kuti mumamukonda popanda kugonana naye. Gulu lirilonse likhale pa mpikisano woti lione
kuti gulu limene lipange ndondomeko yayitali pakati pa anyamata kapena atsikana. Zina mwa
zitsanzo ndi izi:
•
•
•
•
•
•
Kumpatsa wokondedwa wako switi yomaliza.
Kunena kuti “Ndimakukonda”
Kumutonthoza pamene wakhumudwa.
Kumuyamikira
Kuwalembera ndakatulo kapena nyimbo.
Wosamachita za mseri.
4. Bwezerani anyamata ndi atsikani pamodzi ndipo afunseni kuti agawane ndondomeko zomwe
anapanga, azinena chinthu chimodzi chimodzi pa ndondomeko zawo mosinthana mnyamata
ndi mtsikana mpaka atamaliza zonse.
5. Funsani mfunso wokambirana awa:
•
Kodi ndi zinthu ziti zimene zikufanana pakati pa anyamata ndi atsikana?
73
•
•
•
•
Kodi ndi zinthu ziti zimene zikusiyana pakati pa anyamata ndi atsikana?
Kodi ndi mfundo iti imene atsikana ayikonda kwambiri?
Kodi ndi mfundo iti imene anyamata ayikonda kwambiri?
Mungamve bwanji munthu wina atakuchitirani zoterezi?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Nenani izi: “Pamene mwangotha msinkhu mumakhala ndi zilakolako zochuluka pa munthu
wina. Anthu amati ukamamva chonchi ndiye kuti uyenera kuyamba kugonana ndi munthuyo kuti
umuwonetse chkondi. Ngati munthu wina atakuuza kuti ugonane naye kuti utsimikizire chikondi
chako ndiye kuti munthu ameneyo wasokonekera maganizo pa nkhani yosiyanitsa pakati pa
kugonana ndi chikondi. Kumbukirani Moffat ndi Martha amene ali pa chikondi koma samagonana
pofuna kuonetsera chikondi chawo. Ndipo Tim ndi Mary awonetsa kuti kugonana sikutanthauza
chikondi popeza amagonana koma sanali pa chikondi.”
2. Pakutha tsiku la lero mudziwa kuti pali njira zambiri zimene mungaonetsere chikondi pa
munthu wina popanda kugonana naye. Mafuno abwino pa maganizo anu abwino.
Phunziro Lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
74
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 13
Ndine wokonzeka kuyamba zogonana?
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Pochita sewero ndi zokambirana, ophunzira amaphunzira kusiya
kulingalira za kuchita kapena kusachita zogonana, zimene zimathandiza
kuchepetsa zotsatira zimene zingakhale nthawi yayitali chifukwa cha
zilakolako za kanthawi yochepa.
Zolingaza
maphunziro:
Potsiriza pa gawoli ophunzira achita:
1. Amvetsetsa zifukwa zimene achinyamata amachitira chiwerewere.
2. Amvetsetsa zotsatira zochita chiwerewere.
Nthawi:
Mphindi 55
Zipangizo
zofunkira:
99 Ziduswa za mapepala zoti ophunzira agwiritse ntchito mu ntchito 1
chigawo chachiwri. Ngati palibe ziduswa za mapepala ophunzira athe
kukumbukira mafunsi awo.
99 Werengani gawoli ndipo mumvetsetse zinthu zopambana pa
mafunso amene ali mu ntchito 1,mugawo 2 ndi mafunso amene ali
mu ntchito 2, mugawo 4.
99 Musanayambe chigawochi, funsani wophunzira wa mkazi kapena
wamwamuna ngati angakhale wokondweretsedwa kuchita sewero
lomwe anthu awiri okondana akusinkhasinkha zochita kapena
kusachita zogonana. Ngati palibe amene akufuna kuchita izi, kapena
mukuganiza kuti izi ndi zochititsa manyazi kwambiri kwa ophunzira,
funsani achikulire awiri kuti achite seweroli.
Ntchito 1: Kodi ndilingalire
chiyani ndisanachite Zogonana?
Mphindi 15
1. Anthu awiri omwe apange sewero achokepo kukakonzekera magawo a sewero. Zinthu
zimenene akufunika kukambirana zikhale mayina awo a pa sewero, nthawi imene
anadziwanirana, anakumana bwanji, kumene anakumana, amamva bwanji pa wina ndi
mnzake ndiponso zimene akuganiza pa zakuchita zogonana.
75
2. Pamene awiririwa akukonzekera sewero, ena onse akhale awiriawiri m’magulu a atsikana
kapena anyamata okhaokha ndipo alingalire kuti iwo ndi wachinyamata, amene akuganiza
zochita zogonana ndi munthu wina. Ndi mafunso ati omwe angawathandize kupanga
chisankho chabwino? Mwachitsanzo, ndi chifukwa chiyani ndikufuna kupanga zogonana
ndi munthuyu? Ndi mafunso ati amene angawathandize kulingalira za zotsatira za chisankho
chawo? Mwachitsanzo,’’ungatani mtsikanayo atatenga mimba? Gulu lirilonse lirembe mafunso
oti afunse anthu amene achita sewero panthawi imene abwelere m,malo mwao.
•
Musamalire kuti musawafunse anthu awiriwa mafunso wowulura mayankho amene
mukufuna kumva. Mwachitsanzo:
MUSAFUNSE KUTI: simukuganiza kuti ndi zolakwika kuchita zogonana musanalowe
m’banja?
MUFUNSE KUTI: mumaganiza motani pa nkhani yochita zogonana musanalowe
m’banja?
•
Yesetsani kufunsa mafunso ogwirizana ndi mafunso amene mwangofunsa. Mwachitsanzo
“Queres ter um filho com essa pessoa?”
YANKHO: “AI”
“ndiye mukuchitapo chiyani kuti mupewe kutenga mimba ngati mukuchita zogonana?”
Ntchito 2: Tidzichita kapena tisamachite?
Mphindi 20
1. Itanani awiri omwe amachita sewero kuti abwelere m’malo mwao. Akumbutseni kuti ali
panthawi yofunika kupanga chisankho chofunikira. (m’manja) ndipo mulingalire zotsatira
zina zilizonse zimene zingadze chifukwa cha chisankho chimene apanga. Adziwitseni kuti
ophunzira anzawo awathandiza kupanga chisankho chosankha kuchita kapena kusachita
zogonana powafunsa mafunso. Ophunzira anzao awathandiza kuchita chisankho moganiza
osati monga m’mene akumvera.
2. Funsani awiri aja kuti anene mayina awo. Akhale mumaudindo awo apasewero pamene gulu
liwafunse mafunso
3. Udzani ophunzira kuti afunse mafunso okhuza atsikana kapena anyamata ndi cholinga choti
apange chisankho limodzi.
4. Ngati gululi lamalidza kufunsa mafunso, wonjezerani mafunso awa amene sanafunsidwepo:
•
•
•
•
76
Ndi chifukwa chiyani ukuganiza zochita zogonana ndi munthuyu?
Ngati umalingalira zochita zogonana ngati njira yotsimikiza chikondi chako, unayamba
waganizirapo njira zina zimene zingaonetse chikondi popanda kugonana?
Unayamba wakambirana ndi munthuyu zokhudzana ndi kugonana?
Ukumva kukamizidwa ndi munthu wina kuti ukachite zogonana?
•
•
•
•
•
Ndinu oledzera kapena mwagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo? Ngati muli
woledzera mukadafunabe kugonana ngakhale mudakati simudaledzere?
Mupitiliza kukhala limodzi ngati anthu omwe ali pa chibwenzi kapena mukwatilana?
Ngati simufuna kukhala ndi mwana, mungatani popewa kutenga mimba?
Kodi moyo wanu ungasinthe bwanji mutakhala ndi mwana panopa? Mungadzapitiridze
sukulu?
Mungachite chiyani kuti mupewe kutenga kachilombo ka edzi kapena matenda
opatsirana pogonana? Mudzakhala otetezedwa bwanji?
Ntchito 3: kupanga chisankho choganiza
Mphindi 15
1. Pamene awiriwa amaliza kuyankha mafunso onse, achokepo kwa mphindi zisanu kuti
akakambirane:
•
•
•
•
Atamva zonse zimene zanenedwa kodi akanasankha kuchita kapena kusachita
chiwerewere?
Kodi ndi zotsira zanji zoyipa kapena zabwino zimene zingadze chifukwa cha
chisankhochi?
Ndi mafunso ati amene anathandizira kwambiri kupanga chisankho?
Kodi uku ndi “kulingalira” kapena “kulakalaka” kapena zones?
2. Pamene awiriwa achokapo ophunzira akambirane mafunso onsewa ndipo aponye mavoti
yosankha ngati akufuna kuti awiriwa achite zogonana kapena ayi.
3. Awiriwa abwera ndipo anena chisankho chawo ndi zifukwa zake. Ndipo gulu liwauza m’mene
anavotera.
Kuomba mkota
Mphindi zisanu
1. Kodi ndi zifukwa ziti zomwe mwamva zimene zingalimbikitse kwambiri kuti munthu achite
zogonana?
2. Kodi ndi zifukwa ziti zomwe mwamva zimene zingalimbikitse munthu kuti asachite zogonana?
3. Kodi mukuganiza kuti achinyamata amadzipatsa nthawi (m’manja) yodzifunsa mafunso
oterewa asanachite zogonana?
4. Kodi kukambirana uku kuthandiza bwanji chisankho chanu?
5. Thokozani awiri aja chifukwa cha sewero lao.
77
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
78
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 14
Kukana kuchita zogonana
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira akambirane zotsatira zoyipa zomwe zimadza chifukwa
chochita zogonana pamene uli msinkhu waung’ono.
Zolinga
za maphunziro:
Potsiliza pa gawo ili ophunzira athe kuchita izi:
1. Kupanga mfundo zowathandiza kukana kuchita zogonana.
2. Awonetse maluso ponena “toto”
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 Pezani ma chati awiri (kapena jambulani zigawo ziwiri pabolodi) gawo
limodzi mulembe “zabwino” ndipo linalo mulembe “zabwino.”
Ntchito 1: Ubwino ndi Kuipa kwa kudziletsa
Mphindi 10
1. Funsani ophunzira kuti aganizire za phunziro lomwe langothali ndi zonse zomwe zingadze
chifukwa cholola kugonana. Auzeni kuti lero aphunzira mmene angaphunzirire kunena kuti
ayi kapena kudziletsa kuchita m’chitidwe wogonana mpakana pamene ali okonzeka kulandira
china chirichonse chomwe chingadze. Akumbutseni kuti kudziletsa kumatanthauza kusachita
m’chitidwe wogonana. Akumbutseninso kuti kugonana kumatanthauza pamene mwamuna
alowetsa mbolo yake kwa mkazi.
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
N’zofunika kukumbukira kuti anyamata atha kukakamizidwanso kuchita zogonana
ngakhale pa nthawi yomwe sakufuna. Anyamata akhoza kuchita manyazi kunena
zimenezi ndipo mungawathandize kumasuka kunena zokumtima kwawo.
Akumbutseni kuti kukhulupirira kuti “mwamuna weni weni amachita zogonana” ndi
njira ina yokhalira “m’bokosi”. Auzeni kuti mwamuna weniweni amadikira.
2. Funsani ophunzira kuti alingalire za zinthu zabwino zokhudzana ndi kudziletsa. Lembani pa
bolodi pansi pa mawu oti “ubwino”. Akamaliza ophunzira onani ndi kuonjezera zina mwa
zotsatirazi ngati sizinatchulidwe:
79
•
•
•
•
•
•
•
•
Titha kudikikira osogonana mu ubwezi okondana wina ndi mnzake komanso ngati tili
okhulupilirana
Ngati tidikira kufikira tili okonzeka, kugonana kwathu koyamba kungakhale kwabwino
chifukwa tidzakhala tili okonzeka.
Tidzakhala mu chiopsezo chochepa chongogwiritsidwa ntchito kapena kuchitidwa
nkhanza.
Kudzakhala kochepa kupezeka tikudandaula kuti tagonana ndi munthu oti samatikonda.
Kudziletsa ndi njira yokhayo ya pamwamba yodzitetezera ku mimba, matenda
opatsirana pogonana, kuphatikizapo. Makondomu amathandiza ngati atagwiritsidwa
bwino ntchito nthawi ina iliyonse yomwe tikugonana. Nthawi zina amtha kuphulika
ndipo palibe njira iliyonse yogwiritsa ntchito mankhwala olelera yomwe iri yodalilika
kotheratu. Ngati tidziletsa, sitidzada nkhawa za mavuto oterewa.
Ngati tigwiritsa pa mfundo yogonana pokhapokha titalowa m’banja, tidzakhala
osangalala kuti tinasunga mfundo zathu..
Ngati anzathu kapena makolo athu amavomeleza mfundo yakugonana pokhapokha
titalowa m’banja, adzatiganizira ife kukhala anthu abwino.
Ngati tikhala odziletsa, tidzakhala ndi nthawi komanso mphamvu zokwanira
pamaphunziro athu ndi maluso athu.
3. Tsopano funsani ophunzira kuti alingalire za zotsatira zoyipa zobwera chifukwa cha kudziletsa.
Lembani mayankho awo pansi pa mawu oti”kuyipa” pabolodi kapena papepala. Ena mwa
mayankho omwe angapereke ophunzira ndi awa:
•
•
•
•
•
•
•
Tidzamanidwa chisangalalo chomwe chimabwera chifukwa cha kugonana.
Tikhoza kumva kukhala okhumudwa komanso otsalira zitapezeka kuti anzathu onse
akupanga koma ife ayi.
Tikhoza kuchita mantha kuti chibwenzi chathu chitha ngati titakana
Sitikufuna kukhumudwitsa zokhumba za abwenzi athu.
Anzathu atha kutinyoza.
Anyamata amaona ngati atsikana omwe amakana kugonana ndi odzimva kotero
amawakakamiza kugona nawo.
Tithe kuziona ngati sitinakule ngati sitikuchita m’chitidwe ogonana.
4. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali pa zokambiranazi ndi ndandanda omwe
atulutsawo. Auzeni kuti akhala akugwiritsa ntchito ndandanda wa mfundozi mu zochitika
zomwe zikubwerazi.
Ntchito 2: kugwiritsa ntchito
mawu oti “ayi” ku kugonana
Mphindi 30
1. Akumbutseni ophunzira za njira yolumikizana ndi anzathu ya kudzikhulupirira.
•
80
“Ndikumva …” apa ophunzira anene zomwe akumva mu mtima mwawo
•
•
•
“Pamene…” apa wophunzira amanena chomwe mnzawoyo wachita chomwe
chawapangitsa kuti amve choncho mtima mwawo. Tizindikire kuti apa cholinga
sikumunena mzathuyo koma kunena mmene ife tikumvera.
“chifukwa…” wophunzira amafotokoza chifukwa chomwe zomwe zachitikazo
zawapangitsa kuti amve mmene akumvereramo.
“ ndipo ndikufuna….” Ndi chiyani chomwe akufuna kuti akhalenso bwino?
2. Kodi kuyankhula modzikhulupiriraku kungagwiritsidwe bwanji ntchito ponena kuti “ayi” ku
kugonana? Auzeni ophunzira za chitsanzo ichi:
•
•
•
•
Ndimamva kusasangalala
…pamene iwe ukuti sindimakukonda chifukwa choti sindikufuna kugonana nawe
…chifukwa ine ndimakukonda
…ndipo ndikufuna kuti mwalo mwake tidzingocheza ndi kukumbatirana.
•
•
•
•
zimandikwiyitsa
…pamene sukumva kuti ndikuti “ayi”
…chifukwa ukudziwa kuti ndimakhulupirira kuti kugonana ndi kwa m’banja
…ndipo ndikumapita kunyumba.
3. Auzeni kuti tsopano tigwiritsa ntchito njira yathu ya kuyankhula mochangamuka n’cholinga
chofuna kugonjetsa amene angatiumirize kugonana pamene ife tisakufuna.
4. Agaweni kuti akhale awiri awiri. Mmodzi mwa ophunzira awiriwo ndi amene adzinena
kuti “ayi”. Agwiritsa ntchito njira ya kuyankhula mochangamuka pofuna kunena kuti “ayi”.
Akhoza kugwiritsa ntchito ndandanda wa “zabwino zonenera kuti “ayi” ku kugonana pofuna
kuthandizika pa mfundo zanu.
5. Winayo ndi amene adzifunsira ndipo akhoza kugwiritsa ntchito ndandanda wa”kuipa
konenera kuti “ayi” pofuna kunena mfundo zakezo. Akhoza kugwiritsa ntchito njira ina iliyonse
yomukopera mzawoyo.
6. Zitsanzo za kuyesezera kwawoko zingakhale zotsatirazi:
•
•
•
•
•
Mtsikana akufuna kugonana koma mnyamata sakufuna.
Mnyamata akufuna koma mtsikana sakufuna.
Anthu osiyana zaka; mwachitsanzo mzibambo wachikulire akufuna kugonana ndi
mtsikana wachichepere.
Achinyamata awiri omwe ali m’chikondi.
Mzimayi apereka ndalama kwa mnyamata kuti agone naye.
Ngati wotsogolera, muyenera kuganiziranso zitsanzo zina zomwe ophunzirawa angakumane
nazo m’madera mwawomo.
7. Atayesezera kuchita zitsanzo zingapo, afunsa ophunzirawo kuti asinthane mbali. Ofunsira
akhale ofunsiridwa ndipo ofunsiridwa atenge mbali ya ofunsira.
81
8. Abweretseni ophunzirawa pamodzi ndipo funsani ena kuti awonetsenso zomwe amachita
pamene amakambirana.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Akamaliza ophunzirawo kupanga ziwonetserozo athokozeni ophunzirawo chifukwa chotenga
mbali ndipo kenaka funsani gululo mafunso otsatirawa:
•
•
•
Nd njira ziti zomwe zinawathandiza kuti aime pa chisankho chawo cha kudziletsa?
Ndi njira ziti zomwe ofunsira anagwiritsa ntchito ndi zinali zokomedwetsa?
Ndi njira ziti zabwino zomwe zinathandiza kugonjetsera mayeserowo?
2. Malizani powauza ophunzira kuti tsopano apeza luso lotha kunena kuti “Ayi” ku mfundo zofuna
kuti ife tigonjetsere mayeserowo akugonana komano mfundonso zochokera kwa winayo
nthawi zina zimakhala zamphamvu. Njira yomwe angakhalirebe olimba ku mfundo zokopa
choncho ndi kukhala othandizana wina ndi mnzake ku chisankho chathu chosalola kugonana
mpaka m’banja.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira potenga mbali pa zokambiranazi.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
82
NTHAWI;
MALO;komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 15
Sindimafuna kugonana
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira aphunzire za njira zosiyanasiyana za mphamvu zomwe
zingagwiritsidwe ntchito pofuna kuwumiriza ophunzira kugonana
asakufuna, kaya atavomera kapena asanavomere. Adziwe kuti kugonana
komwe kwachitidwa mwa kusafuna kwawo si vuto lawo ndipo adziwe
komwe angakapeze chithandizo.
Zolinga zophunziro:
Pakutha paphunziroli, ophunzira athe:
1. Kudziwa kuti kugonana komwe kumachitika mokakamizidwa kudzera
m’maganizo kapena kugwiritsa ntchito mphamvu ndi kugonana
kosayenera.
2. Kudziwa malamulo a m’dziko lawo okhudza za nthawi yoyenera
yomwe munthu angavomere kugonana.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunikira:
99 Mudziwiretu malo ndi anthu omwe ophunzira omwe achitiridwa
nkhaza zokhudzana ndi kugonana angapite kukapeza chithandizo.
Funsani sukulu yanu zomwe zilipo zoti zingathandize pankhaniyi.
99 Unikaninso nkhani ya “Mmene Tingachitire Ndi Achinyamata Omwe
Achitiridwa Nkhanza Zokhudza Kugonana” yomwe ili kumapeto kwa
gawoli.
99 Unikaninso chaka chovomerezeka cha dziko lanu. Apa tikutanthauza
chaka chomwe wophunzira angathe kuviomera payekha kuti
agonane ndi munthu kapena asagonane naye kapena kuchita chinthu
chilichonse choopsa (onani ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA
kumapeto kwa Ntchito 2).
Ntchito 1: kodi ali ndi ulamuliro ndi ndani?
Mphindi 25
1. Lembani mawu oti “ulamuliro” pa bolodi.
2. Funsani ophunzira tanthauzo la mawu oti ulamuliro. Funsani ophunzira zitsanzo za anthu
omwe ali ndi ulamuliro. N’chifukwa chiyani umulamuliro uli wofunikira? Kodi ulamuliro
ungagwiritsidwe bwanji ntchito?
83
3. Uzani ophunzira kuti ayimirire.
4. Konzani sikelo ya ulamuliro pansi pa kalasi lanu kapena pakhoma ndipo mulembepo 1
kumayambiriro kwa sikeloyo, 5 pakati pa sikeloyo ndi 10 kumapeto kwa sikeloyo.
5. Werengani nkhani zotsatirazi mwapang’onopang’ono. Funsani ophunzira kuti anene mmene
nkhani iliyonse yawerengedwayo kuti munthu aliyense yemwe anali m’nkhaniyo anali ndi
mphamvu zochuluka bwanji malingana ndi sikelo yomwe akonza ija. (1 kutanthauza kuti
panalibe ulamuliro ndi 10 kutanthauza kuti panali ulamuliro wambiri).
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Ngati palibe nthawi yokwanira kugwiritsa ntchito nkhani zonsezo mukhoza
kungogwiritsa ntchito nkhani imodzi yomwe nkhaza zakuthupi zagwiritsidwa ntchito
(Martha, Sara) ndi ina yomwe kunyengerela kwagwiritsidwa ntchito (Lucy, Peter).
Mwachitsanzo, mu nkhani (a), pa sikelo kuyambira 1 mpaka 10 kuwonetsera kusiyana kwa
ulamuliro; kodi Martha ali ndi ulamuliro wochuluka bwanji? Afunseni ophunzira kuti akaime
pamene pakusonyeza mlingo wa ulamuliro womwe Martha ali nawo pasikelopo. Kenaka funsani
ophunzira kuti aime pa sikelo kuti asonyeze mlingo wa ulamuliro womwe wophunzira wamkulu
uja ali nawo. Funsani opphunzira kuti ndi ndani ali ndi ulamuliro wochuluka: Martha kapena
wophunzira wamkuluyo? Afunseni kuti afotokozere yankho lawo.
Tsatani njira yotsatirayi pa kankhani kalikonse.
Nkhani zonse:
a. Martha amachokera ku sukulu kupita ku nyumba kudzera njira yachidule yomwe
inali mkati mwa minda ya chimanga chitalichitali. Pamene anafika pamalo poti
panali chimanga chambiri zedi komanso chachitali, mnyamata wamkulu komanso
wamphamvu wakusulu kwawo anatulukira ndi kumugwira Martha kumulowetsa
m’chimnga muja. Mnyamatayu anamuuza Martha kuti asakuwe. Iye ananena kuti
Martha ankachita matama kuti sanagonepo ndi mwamuna chibadwire ndiye
akafuna kuti amukhaulitse. Mnyamatayo anamugwiririra Martha.
b. Lucy ali ndi zaka 14 ndipo ali ang’ono ake anayi. Bamboo ake sali pantchito ndipo
mayi ake ndi woyembekezera. Iye amawathandiza mayi ake popita kumsika
kukagulitsa kapena kukagula zinthu. Panjira akumana ndi kufunsiridwa ndi
njonda ina yomwe ili ndi malo omwera mowa. Njondayi ndi yachikulire komanso
imadwaladwala. Amayi ndi azakhali ake amuuza kuti ndi chinthu cha mtengo
wapatali kufunsiridwa ndi munthu ngati ameneyu ndipo amuuza Lucy kuti
avomere. Lucy akana chifukwa bamboyo ndi wamkulu komanso sakumufuna.
Bambo ake ndi amalume ake amuumiriza kuti apite kwa njondayo ndipo asiye
kuchita matama. Lucy apita kwa njondayo ndipo kumeneko amupatsa ndalama
84
ndi mowa zoti atengere bambo ndi amalume ake popita kunyumba. Iye avomera
ndipo mwakachetechete alira pamene akukhalira pamalo amodzi ndi njondayi.
c. Amayi ake a Peter ali ndi mzawo woti mwamuna wake anamwalira ndipo
wakhala ali ndi chidwi ku nkhani ya sukulu ya Peter. Pa nthawi ina, pamene
makalo a Peter analephera kumulipirira sukulu, mayiyu anamuthandiza pomuuza
kuti adzikamulimira kumunda wake. Peter anavomera. Poyamba zonse zinali
bwino bwino kufikira panthawi yomwe mayiyu anayamba kumufunsa mafunso
okhudzana ndi zibwenzi ndi zina zomwe amakonda. Ulendo winan anayamba
kumagwiragwira ndipo mmene anadandaula anamuuza kuti ngati amafuna
kukhala mwamuna weni weni weni anayenera kumapanga zimenezi kawiri
kawiri. Anamulonjezanso kumulipirira fizi ya teremu yotsatirayo. Peter sakufuna
kumagona ndi mayiyu komanso akufuna kupita ku sukulu. Tsopano wayamba
kumagona ndi mayiyu kawiri kawiri koma sizikumusangalatsa.
Aphunzitsi a Sara anamupempha kuti awanyamulire mabuku kupititsa ku nyumba
kwawo tsiku lina ataweruka. Atafika anapeza kuti ali wokha m’nyumbamo.
Anamufunsira. Sara anakana ndipo anawauza kuti ndi zosayenera chifukwa iwo ndi
aphunzitsi ake komanso munthu wamkulu. Aphunzitsiwo anamukoka ndikuyamba
kumugwiragwira uku akumukokera kuchipinda kwawo. Sara anayamba kukuwa
ndipo anamusiya. Iye anathawa.
6. Funsani ophunzira, ndi zifukwa ziti zomwe zinapangitsa kuti anthu a m’nkhaniyi akhale ndi
ulamuliro? Zina mwa zitsanzozo ndi:
•
•
•
•
•
•
Akulu komanso amphamvu
Wina amene umamukhulupirira ngati mnzako, wachibale kapena mphunzitsi
Ali ndi ndalama
Mphunzitsi ndi munthu yemwe amakhala ndi ulamuliro
Mzimayi wamasiye uja amapereka fizi ndipo anali ndi ulamuliro pa tsogolo la Peter.
Amuna nthawi zambiri amakhalandi mphamvu za ku thupi, pa ndalama, ndi pa
chikhalidwe. Abambo nthawi zambiri amatenga maudindo a pamwambakusiyana
ndi amayi: mwachitsanzo, ufumu, m’boma, ku usilikali, ku mpingo ndi ma bizinezi.
Mukumbukurani za mabokosi a m’gawo 3? Timayembekezera amuna kutenga maudindo
a pamwamba pamene atsikana ndi amayi amaponderezedwa kuti atenge maudindowa.
85
Ntchito 2: kupereka chilolezo,
kunyengereredwa ndi kugonana mosafuna
Mphindi 15
1. Nenani “m’nkhani iliyonseyi ophunzira analibe ulamuliro- munthu winayo anali ndi ulamuliro”.
Funsani “kodi wophunzira anapereka chilolezo pa zomwe zinamuchitikira mu nkhaniyi?” Tikati
“kupereka chilolezo” tikutanthauza “wophunzirayo anavomera pa chochitikacho?” Funsani:
•
•
•
•
Kodi Martha anavomera kugonana ndi wophunzira wamkulu uja?
Kodi Peter anavomera kugonana ndi amnzawo a amayi ake aja?
Kodi Sara anavomera kugwiridwa ndi aphunzitsi ake kapena kugonana nawo?
Kodi Lucy anavomera kuti agonane ndi mwini wake wa malo omwera mowa uja?
2. Martha ndi Sara sanavomereze. Wophunzira ndi mphunzitsi uja anagwiritsa ntchito mphamvu
kuti agone nawo ndi kuwagwiragwira.
3. Nenani: “zikuoneka ngati Peter ndi Lucy anavomera kuti agonane ndi anthu amene agonana
nawowo kupanda apo sitikuwaona atakana. Koma kodi Lucy ndi Peter anasangalala nazo?
Chifukwa chiyani sanangalale kapena anasangalala?
•
•
•
Ayi. Lucy analira pamene njonda ija anagona naye.
Ayi. Peter sanasangalale nazo za kugonana ndi amayi aja.
Ayi. Onse anakana kwa nthawi yayitali mpaka pamapeto pake mpamene anagonja.
4. Funsani ophunzira , “kodi n’chufukwa chiyani Peter ndi Lucy anapangabe chiwerewerechi
ngakhale sankafuna kuvomera? Ophunzira afotokoze kuti:
•
•
Lucy chifukwa choti makolo ake anamukakamiza.
Peter chifukwa ankafuna ndalama zopitira ku sukulu.
5. Fotokozani kuti zonse zomwe zinachitikira Sara, Martha, Lucy ndi Peter ndi kugonana
mwakusafuna kwa mwini wake kutanthauza kuti onsewa sanafune kugonana ndi anthu
amene anagonana nawowo.
•
•
•
•
•
86
Sara ndi Martha anachita kukakamizidwa mwamphamvu za kuthupi kuti agonedwe
kapena kusisitidwa.
Lucy ndi Peter sanavomere koma analibe mwayi wokana.
Achinyamata amene amagonana ndi anthu mwakusafuna kwawo amakhala
atawumirizidwa kapena kunyengeredwa ndi anthuwo, kotero amakhala alibenso mwayi
woti angakane.
Palibe wachinyamata aliyense yemwe wachita chiwerewere mwakusafuna kwake
ayenera kunenedwa kapena kuimbidwa mlandu.
Zomwe zinachitikira Martha, Sara, Peter ndi Lucysi vuto lawo.
6. Mu dziko lathu lino ana osakwana zaka (onani pa ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA)
savomerezedwa mwamalamulo kuvomereza zakugonana ndi munthu aliyense. Izi
zikutanthauza kuti kugonana ndi aliyense yemwe sanafike msinkhu umenewu ndi mlandu.
Dziko lathu limazindikira kuti akulu akulu ali ndi ulamuliro komanso mphamvu zambiri koposa
ana kotero sakuyenera kugwiritsa ntchito mphamvu powumiriza achichepere kuti apange
nawo zogonana.
ZOYENERA KUDZIWA WOTSOGOLERA:
Ku Malawi, msinkhu wovomerezeka ndi 13. Ku Mozambique ndi 19. Ku Botswana,
msinkhu wake ndi 16. Izi zikutanthauza kuti ana omwe sanafike zaka zimenezi
sakuyenera kuvomera pawokha kuchita zogonana ndipo ngati munthu wamkulu
achita nawo zadama ndi mlandu wogwiririra mwana ndipo akuyenera kumangidwa.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. RUnikaninso zomwe ophunzira omwe agwiriridwa angachite kuti apeze chithandizo.
2. Kumbutsaninso ophunzira kuti si vuto lawo pamene apezeka atagonana ndi munthu
mwakusafuna kwawo.
3. Uzani ophunzira kuti Gawo 20 “kugwiritsa Ntchito kulumikizana Popewa Zoopsa” aphunzira za
mmene angadzitetezere okha.
Phunziro lotsatira
1. Athokozeni ophunzira potenga mbali pa zokambiranazi.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO;komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
87
Mfundo zofunikira pamene mukuchita
ndi ana omwe anagwiriridwapo ndi
omwe anakakamizidwa kuchita zogonana
Ndi zotheka kuti ophunzira ena omwe atenga nawo mbali mu angathe kukamizidwa kuchita
zogonana kapena kugwiriridwa. Ena akhonza kuchitilidwa nkhaza zokhuza kugonana koma iwo
osazindikira kuti ndi nkhanza. Chifukwa choti nkhanza zokhuza kugonana kapena kugwiririra
ndi zochuluka mumadera ambiri, phunzirori lingapangitse ophunzira ena kukumbukira zomwe
zinawachitila zomwe zingabweretse kuwawidwa mtima. Mmumsimu muli njira zomwe aphunzitsi
angagwiritse ntchito kuwatonthoza ophunzira omwe angakmbikire zomwe zidawachitikila.
Kuonjezera pa njira zimenezi aphunzitsi ayenera kupeza zinthu zina zomwe angagwiritse ntchito
potonthoza omwe asweka mitima, monga kupeza anthu omwe angamawalangize, anamwino,
atsogoleri achipembedzo kapena mafumu makamakanso omwe anaphunzitsidwa momwe
angathandizire anthu omwe achitiridwa nkhanza zogonana kapena kugwiriridwa.
Njira zolimbikitsa:
1. Mukhale okonzeka nthawi zones kumuthandiza ophunzira yemwe wagwiriridwa kapena
wachitilidwa nkhanza zogonana.
2. Mtengereni ophunzirayo pa malo otetezeka kunja kwa kalasi, kutali ndi anzake. Onenetsetsani
kuti malowo ndi otetezeka komanso kwa ophunzirayo.
3. Mufunseni ophunzirayo chomwe akufuna kuchita pa nthawi imeneyo, mwachitsanzo
kupita kunyumba, kukhala mkalasi momo pamene akuphunzitsa phunzirori koma
osatenga nawo mbali, kukhala panja osatenga nawo mbali pa phunzirori kapena
kukhala malo ena apasukulu pomwepo kuyankhula ndi mulangizi kapena munthu wina
amene angathe kuthandiza nthawi yomweyo kapena tsiku lina ndi zina).
4. Musaweruze.Muthandizeni ndi kumufotokozera ophunzirayo mosayang’ana mmene
akumvera, zikhulupiliro zake kapena maganizo ake.
5. Musamuuze zinthu zambiri mbiri ophunzirayo,musamufunse mafunso ambiri kpaena
kumupatsa malangizo ambirimbiri. Musaganize kuti ophunzirayo ndi okonzeka kulandira
zones zomwe mungamupatse.
6. Mvetserani zomwe ophunzirayo akunena. Ntchito yanu ndikumumvetsetsa ndi
kumuthandiza. Musamuwuze ophunzirayo momwe akumvera kapena momwe
akuyenera kumvera. Muuzeni kuti sizolakwika kumva momwe akumveramo.
7. Khalani omasuka kuti muthe kumuthandiza opunzirayo. Aphunzitsi akhale okonzeka kuyitana
aphunzitsi ena, muwawuze ophunzira kuti apumulire kaye kwa nthawi yochulukirapo komanso
mukhale okonzeka kuyitana aphunzitsi ena ngati ophunzirayo angafune kuti aphunzitsiwo
asakhalepo.
88
8. Mumutsatile ophunzirayo. Izi zimathandiza kuti ophunzirayo awone kuti mumamukonda
komanso ndinu okhuzidwa ndi vuto lake ndipo mukufuna akhale bwino msanga.
9. Mukhale ndi mulangizi kapena munthu yemwe anaphunzitsidwa bwino kuti ayankhule ndi
naye ophunzirayo za momwe akumvera.
10.Ngati ophunzira mbiri akhuzidwa , zikutanthauza kuti ophunzirawo siwokonzeka kuphunzira
phunziroli chotero muyimitse ndipo muzapitilize tsiku lina kapena mulidumphe kumene.
Zomwe sizimabweretsa chitonthozo
1.
2.
3.
4.
5.
6.
7.
8.
9.
Musamusokoneze, kumukalipila kapena kumuchititsa manyazi ophunzirayo.
Musamuwonetse kuti iye ndi olakwa Musamufunse mafunso ambirimbiri.
Musamuweruze ophunzirayo
Musangomusiya.
Musachepetse mmene akumvera.
Musamupangitse ophunzirayo kumva kuopsezedwa
Musamupangitse ophunzirayo kuti ayiware kapena chotse maganizo omwe ali nawowo
Musamuwuze momwe akuyenera kumvera.
Musakambirane zomwe zikumuchitikirazo ndi anthu ophunzira ena.
89
Gawo 16
Kuyankhula ndi akulu akulu zokhuza kugonana
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira afotokoze makhalidwe a anthu akulu akulu omwe angathe
kuwakhulupirirandi kukamba nawo nkhani zokhuza kugonanandipo
ayesere angayambire kukambirana nawo nkhani ngati zovuta ngati
zimenezi.
Zolinga Zaphunziro: Pomaliza phunziroli, ophunzira adziwe momwe:
1. Angadziwire munthu wamkulu yemwe angathe kukambirana naye
nkhani zokhuza kutha msinkhu, kukula ndi kugonana
2. Kupeza njira za momwe angayankhulirane ndi akulu akulu nkhani
zogonana.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 •Konzetserani bolodi kapena pepala lomwe mukugwiritsa ntchito
ndi “njira zomwe tingagwiritse ntchito pofuna kuyankhula ndi akulu
akulu nkhani zogonana” zomwe zikupezeka mu ncthito 2.
Ntchito yoyamba: Ndi wachikulire wake
uti yemwe ndingayankhule naye?
Mphindi 15
1. Awuzeni ophunzira kuti muli ndi anzanu awiri omwe akufuna thandizo la momwe angapezere
munthu woti ayankhule naye. Afotokozereni nkhani iyi pogwiritsa ntchito mayina omwe ali
mdera lanu.
•
•
90
Mzawo wa abambo ake a Chimwemwe anamuuza chimwemwe kuti wayamba kuoneka
bwino ndipo akufuna apite naye kokasangala. Iye sakufuna kuwachitira mwano
abambowa, ndiye anavomera mwaulemu. Bamboyo anamufotokozera kuti akambirana
nawo bamboo ake koma bamboo akewo sanamuuze china chiri chonse chokhuza ndi
bambowa. Iye ali ndi nkhawa chifukwa bambowa samadziwa bwino bwino komanso
sakudziwa kuti bamboo akuyembekezera chani kuchokera kwa iyeyo. Tsiku lija lafika
ndipo sakudziwa kuti atani.
Tsiku lina Zikani anali ndi maloto abwino kwambiri okhuza mzimayi wokongola yemwe
amamukonda Zikani. Iye anamva bwino kwambiri kenako anadzuka ndi kupeza kuti
malo omwe anagona anyowa komanso pali zonanda ngati mamina. Chinachitika ndi
chani? Anakhuzidwa mu mtima mwake chifukwa cha malotowa naganiza kuti Mulungu
wamulanga ndi nthenda yoopsa. Samadziwa kuti atani.
2. Afunseni ophunzira kuti akanakhala abwenzi a Chimwemwe ndi Zikania akanawauza kuti
amuuze ndani zokhuza ndi mavuto awowo? Ophunzirawa sakuyenera kutchula dzina
la munthu koma kutchula udindo wa munthuyo monga: adzakhali, amalume, mzanga
wapamtima,mchimwene wanga wamkulu, azaumoyo, aphunzitsi, alangizi akusukulu, abusa,
amayi ogwira nthcito kumsika ndi ena otero. Nanga akulu akulu omwe munawatchula mu
gawo 6 aja? Lembani onse omwe awatchule.
3. Onani mndanda wa anthu omwe ophunzira anawatchula kuti ndi omwe angamuuze
Chimwemwe ndi Zikana kuti akakambe nawo zokhuza mavuto awo.
•
•
Ndi chani chomwe chakupangitsani kuganiza kuti munthu yemwe mwamutchulayi
mungathe kukamba naye nkhani zogonana?
Ndi makhalidwe ati omwe ali nawo omwe angakupangitseni kuona kuti ndi anthu
oyenera kukamba nawo
Cholinga chake ndichofuna kuwathandiza ophunzira kutchula makhalidwe omwe amabwera
mumagaizo awo akamaganiza za anthu omwe awatchulawo.
4. Kumbukirani kuti ophunzira akhonza kukhala ndi maganizo omwewo koma angathe kugwiritsa
ntchito mawu ena ndipo izi ndi zabwino ndithu. Asiyeni makhalidwewa momwe ophunzirawa
atchulira.
Munthu wamkulu okhulupirika amakhala…
•
•
•
•
•
Amatenga mavuto ngati ake: Iye amayetsetsa kuti akhuzidwe ngati momwe
mwanayo wakhuzidwira Wawulemu: Iye amamuthandiza ophunzirayo
molemekeza zisankho zake, zofuna zake, ufulu wake komanso ulemu wake.
Wosaweruza: Iye amapereka thandizo la mtundu wina uli wonse mopanda
kuweruza, kuonetsa kusagwirizana nazo kapena mopanda kukwiya kapena
kukalipa.
Wachinsinsi: Iye amasunga chinsinsi cha zonse zomwe zakambidwa pokhapokha
itakhala nkhani yokhuza nkhanza, kufuna kudzichita chiwembu kapena kuchitira
ena chiwembu.
Oteteza: Iye sachita choyipa china chiri chonse. Samapereka malangizo otsutsana
ndi zomwe akufuna ophunzirayo.
Osamala:Iye amaonetsa kumvetsetsa, kuthandiza komanso kulimbikitsa ophunzira.
91
5. Awuzenu ophunzira kuti awonenso bwino bwino makhalidwe omwe atchulidwa ndipo
muwafunse mafunso awa?
•
•
•
Kodi munthu angakhale ndi makhalidwe onsewa?
Ngati ayi, alipo makhalidwe ena omwe akuwawona kuti ndi ofunikira kwambiri kuposa
ena
Afunseni ayerekeze makhalidwe a munthu wamkulu yemwe angamukhulupilire ndi
omwe iwo anatchula kuti ndi makhalidwe amunthu wamkulu yemwe angayankhule
naye. Alipo mayina ena omwe angawachotse pa mndanda wa anthu anatchula uja?
Alipo ena omwe akufuna kuonjezera?
Ntchito ya chiwiri: Momwe mungayambire
kukambirana nkhani zokhuza kugonana
Mphindi 25
1. Afunseni ophunzira ngati akuganiza kuti zikhonza kukhala zovuta kapena zophweka kuti
Zikani ndi Chimwemwe akambirane akulu akulu omwe amawakhulupilira zokhuza mavuto
awo? Pa yankho lomwe apereka penne zifukwa zake?
2. Awuzeni ophunzira kuti ndizotheka kuti angathe kumangika, kuchita chilendo kapena
kuchita mantha kukambirana nkhani zogonana ndi akulu akulu. Afunseni ophunzira ngati
ali ndi amaganizo a momwe Zikani ndi Chimwemwe angayambitsere nkhani zawo ndi
akulu akulu. Lembani mayankho omwe ophunzira apereke. “ Werengani mndandanda wa
“Momwe mungayambire kukambirana nkhani zokhuza kugonana ndi akulu akulu”, mwa
pang’onopang’ono komanso momveka bwino mukupereka zitsanzo ndi kuona zomwe
zikugwirizana ndi zomwe ophunzira ananena.
“Momwe mungayambire kukambirana nkhani zokhuza kugonana ndi akulu
akulu”
a. Njira yoyankhula mwa chindunji
“Tingayankhulane? Ndiri ndi funso lokhuza zomwe taphunzira ku suluku lero mu
phunziro la maluso amoyo
b. Njira yozungulira
“Ndinamvera pologalamu yina yake pa wayilesi yokhuza tsikana omwe anali ndi
ana koma ali ang’ong’ono. Mukuganiza kuti ana ngakhale makolo abwino?
c. Njira yofunsa mokayilira
“Ndi zotheka kuti munthu angakhale ndi mimba atagonana kamodzi ndi
mwamuna?”
92
d. Njira yoyamba ndi kunena kuti “ndinamva kuti”
“Ndinamva kuti ukakana kugonana ndi munthu yemwe umamukonda, akhonza
kukusiya. Nanga ungatani kuti ukane kugonana komanso usamukhumudwitse
munthuyo?”
3. Afunseni ophunzira kuti akhale awiri awiri, atsikana okhaokha ndi anyamata okhaokha . Mu gulu
lirilonse wina akhale wamkulu wina wachinyamata yemwe akufunsa thandizo pa vuto lomwe
ali nalo ndipo achite izi mosinthana. Yemwe ali wachinyamata angathe kukamba nkhani ina ili
yonse yomwe akufuna kapena ngathe kugwiritsa ntchito nkhani ya Zikani ndi Chimwemwe.
Nkhani zake zikhale zokhuza kutha msinkhu kapena kugonana. Ayesere pogwiritsa ntchito
njira zomwe zalembedwa mpaka atamaliza zonse.
4. Yemwe akutenga mbali ya wamkulu wopereka malangizo awonenso makhalidwe omwe
munthu wankulu wodalirika akuyenera kukhala nawo ndipo ayesere kuwawonetsera.
5. Awuzeni ophunzira kuti abwerere mmalo awo ndipo afunse mafunso awa:
•
•
•
•
Mumamva bwanji momwe munal wamkulu wopereka malangizo? Zinali zophweka?
Afunseni ophunzira kuti afotokoze momwe anamvera? Ndi makhalidwe ati amunthu
wamkulu omwe munawakumbikira?
Ndi makhalidwe ati amunthu wamkulu omwe nail ovuta kuwakumbukira
Mumamva bwanji kukhala wachinyamata yemwe anapita kukafunsa thandizo kwa
munthu wamkulu pa nkhani zokhuza kugonana? Munamva bwanji?
Pali njira yoyambitsira kuyankhula yomwe anayiwona kuti inali yophweka?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Nenani mwachidule momwe ophunzira anamvera momwe amatenga mbali ya wachinyamata
yemwe amakafunsa thandizo kwa munthu wankulu: kumangika, kuchita mantha ndi zina.
Athokozeni ophunzira chifukwa cholora kukambira nkhani zovutazi.
2. Akumbutseni ophunzira momwe amamvera mmene amatenga mbali yawamkulu wopereka
malangizo ndipo ayerekeze ndi momwe amamvera momwe anali wachinyamata: kumangika
chifukwa alibe mayankho olondora, kumangika ndi zina.
3. Akumbutseni za khalidwe lotenga mavuto ngati ako lomwe liri pamndandanda wa makhaldwe
amunthu wamkulu yemwe tingathe kumudalira. Kutenga mavuto ngati ako zikutanthauza
kuti kumva ngati momwe winayo akumvera ndikuziyerekeza ngati ndi iweyo. Nthawi yina
akadzafuna kuyankhula ndi munthu wamkulu zokhuza kugonana, azakumbukire kuti munthu
wamkuluyo azakhala womangika, komanso wamantha monga iwo analiri ndipo akhonza
kugwiritsa ntchito njira zomwe aphunzira kuti ayambitse zokambiranazo.
93
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
94
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 17
Kugonana ndi abambo akulu akulu
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira akambirane zotsatira zogonana mtsikana ndi abambo akulu
ndi kukambirana njira za momwe angachepetsere kapena kuthetsera
vutoli.
Zolinga za phunziro: Pa mapeto pa phunziro ili , ophunzira akhonze:
1. Kufotokoza zomwe zimawachititsa atsikana kugonana ndi abambo
akulu akulu.
2. Kutchula zomwe zimawapangitsa atsiakana kugonana ndi abambo
akulu akulu I.
3. Kupeza njira zochepetsera chiopsezo chomwe chimakhalapo
chifukwa chogonana ndi abambo akulu akulu.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Nkhani ya maria ndi yina ya mafunso a nkhani ya Josofini mu ntchito 1.
99 Gawo ili likhonza kukhala lovuta.Mukuyenera kuwereng abwino
nkhani yo khuza Mphamvu ndi kukakamiza mu gawo 15 “Sindimafuna
kugonana”.
99 Mukuyenera kudziwa zaka za munthu yemwe amatengedwa kuti ndi
wamkulu Mmalawi. Izi zizakuthandizani mu khwerero la chiwiri mu
gawo lomaliza. (onani zoyenera kudziwa wophunzitsa kumapeto kwa
phunziroli).
Ntchito yoyamba: Wina amanena kuti “inde” wina “ayi”
Mphindi 30
1. Kambiranani za chithunzichi powafunsa ophunzira mafunso awa…
•
•
•
•
•
Chikuchitika ndi chani mu chithunzichi?
Izi zimachitika mdera lanu
Izi zimachitika chifukwa chani?
Atsikana amapeza phindu lanji akamachita zoterezi
Abambo amapeza phindu lanji kamachita zoterezi
95
2. Agaweni ophunzira mumagulu awiri ang’onoang’ono. Awuzeni kuti akamba nkhani zokhuza
atsikana apasukulupo omwe akuwaziwa.
3. Awuzeni kuti nkhani zawozo zikhale zatsatane tsatane, azikambe mwamphamvu, mosangalatsa
komanso zoti ena ngathe kuyankhulapo monga momwe agogo awo amanenera nthano.
4. Funsani gulu lina kuti liganize za mzawo wotchedwa maria , yemwe avomere kuchita chibwenzi
ndi abambo akulu. Akamakonzekera nkhani ya Maria yovomera kupanga chibwenzi ndi
abambo, gulu lawo akambirane nkhani mafunso awa:
•
•
•
•
•
•
•
•
Maria ndi wotani?
Banja lakwawo ndi lotani?
Kodi amachita bwino ku sukulu?
Kodi zotsatira zabwino zovomera kukhala pa chibwenzi ndi abambo akulu ndi zotani
kwa Maria?
Nanga zotsatira zoyipa kwa Maria ndi zotani? Zoopsa zake ndi zotani?
Ali ndi mphamvu mu chibwenzichi ndani? Maria anali ndi mwayi wosankha chani?
Maria angachepetse bwanji chiopsezo chake mmene wavomera kukhala pa chibwenzi
ndi abambo akulu?
Maria angakane bwanji zogonana kapena kukamira kuti agwiritse ntchito kondomu?
5. Awuzeni agulu linalo kuti anena nkhani ya mzawo wa pasukulupo, Josofini, yemwe akane
kukhala pa chibwenzi ndi abambo akulu. Akamakonzekera nkhani ya Maria yovomera
kupanga chibwenzi ndi abambo, gulu lawo akambirane nkhani mafunso awa:
•
•
•
•
•
•
•
•
•
•
Josephine ndi wotani?
Banja lake ndi lotani?
Kodi amachita bwino kusukulu?
Chinamuchititsa Josofini kukana kukhala pa chibwenzi ndi abambo akulu ndi chani
Anali ndi mphamvu ndani pa nkhani imeneyi? Josofini anali ndi mwayi wosankha chani?
Kodi zotsatira zabwino za Josofini ndi chani?
Kodi zilipo zotsatira zoyipa kwa Josofini chifukwa chokana?
Kodi Josofini angatani kuti asakumane ndi zotsatira zoyipa zomwe zingabwere chifukwa
chowakana abambowa
Kodi Josofini angatani kuti achepetsebe chiopsezo chake?
Awuzeni magulu awiriwa kuti azafotokoza nkhani za zawozo mu gawo linalo, awonetsetse
kuti ayankha mafunso onse omwe afunsidwa. Ngati sakufuna kunena ngati nkhani
cahbe angathe kupanga sewero.
6. Apatseni nthawi magulu awiriwa kuti akonzekere.
96
Ntchito ya chiwiri: Tsogolo la
Maria ndi Josofini ndi lotani
Mphindi 10
1. Magulu onse akumane malo amodzi ndipo gulu lirilonse linene nthano yawo; oyamba Maria
kenako Josofini.
2. Afunseni ophunzira:
•
•
•
•
Mungamuthandize bwanji Maria yemwe wavomera kukhala pachibwenzi ndi abambo akulu?
Mungamuthandize bwanji Maria kuti akane kukhala pa chibwenzi ndi abambowa?
Mungamuthandize bwanji Josofini kukana kukhala pa chibwenzi ndi abambo akulu?
Mungamuthandize bwanji Josofini kukana kukhala pa chibwenzi ndi abambo akulu.
3. Afunseni ophunzira kuti aganizire kuti zotsatira za zisankho za atsikanawa ndi zotani?
•
•
Chomwe chimutsane Maria ndi chani? Maria akhala ali pati pakamatha zaka zisanu?
Akuchita chani?
Chomwe chimutsatire Josofini ndi chani? Josofini akhala ali pati pakamatha zaka zisanu?
Akuchita chani?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Mu phunziri ili taphunzira zifukwa zomwe zimawapangitsa atsikana kuvomera kukhala pa
chibwenzi ndi abambo akulu (Funsani zitsanzo) zotsatila zake (zoipa ndi zabwino) zakukhala pa
chibwenzi ndi abambo akulu akulu (funsani zitsanzo), ndipomaliza, mmene tingachepetsere
chiopsezo chokhala pa chibwenzi ndi abambo akulu (Funsani zitsanzo).
2. Awuzeni ophunzira kuti pambalipokhala kugonana koopsa, kugonana ndi akulu akulu ndi
kuswa malamulo adziko luno. Akumbutseni ophunzira kuti mdziko lathu lino, malamulo
amanena kuti, mwana wosakwana zaka 13 (wonani mumsimu) sangathe kukana kapena
kuvomera kugonana ndi mwamuna. Ngati mwana yemwe ali pa chinthunzipa ndi wosakwana
zaka 13, ndiye kuti bamboyi akuswa lamulo akamagonana naye.
ZOYENERA KUDZIWA OTSOGOLERA:
Malingana ndi malamulo adziko lino, munthu yemwe sanakwane zaka 13
amatengedwa kuti ndi mwana ndipo sangathe kupanga chiganizo china chili chonse
pa yekha. Zomwe zikutanthauza kuti aliyense wa zaka zosaposa 13 sangathe kupanga
ganizo linalilonse lokhuza kugonana. Wina aliyense wamkulu yemwe angagonane
ndi mwa wosakwa zaka 13 akupalamula mulandu wogwiririra ndi akuyenereka
kulangidwa monga mwa lamulo.
97
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
98
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
99
Gawo 18
Zomwe ndimakhulupirira, Ndalama
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Kupyolera mukukambirana ndi zochitika zokhuza mtengo wa ndalama,
ophunzira afotokoze zikhulupiliro zawo ndipo awone ngati njira
zawo zopezera ndalama ndi momwe amagwiritsira ntchito ndalama
zikugwirizana ndi zomwe amazikhulupirila.
Zolinga zaphinziro:
Pamapeto a phunziroli ophunzira aphunzire kuchita izi:
1. Kudziwa zomwe iwo amazikhulupilira.
2. Afufuze bwino bwino chidwi chomwe amayika pa zinthu ndi zomwe
amachita kuti apeze zinthuzo.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Bolodi/choko kapena pepala ndi cholembera papela(pentopeni)
99 Pepala ndi pensulo (mungathenso kugwiritsa ntchito timitengo ndi
kulemba pansi).
Ntchito yoyamba: Kodi ndimakhulupilira chani?
Mphindi 20
1. Afunseni ophunzira kuti mawu akuti zikhulupiliro amatanthauza chani? Funsani wina aliyense
mkalasimo amene ali ndi choti anene mukutchula mobwereza mawu awa:
•
•
Ndi mfundo ziti, zikhulupiliro, masomphenya kapena mfundo zomwe umazitsatila?
Zimatithandiza kupanga chisankho cha zomwe ndingachite kapena ayi? Tinaphunzira
kwa makolo athu, mdera lomwe timakhala, ku mtundu wathu, ku mpingo wathu,
chifukwa ndife akazi kapena amuna, komwe timakhala ndi zina.
2. Perekani zitsanzo za zikhulupiro ndi makhalidwe omwe amafanana nazo:
•
•
•
•
•
100
Chilungamo: Kunena zoona nthawi zonse
Banja: Kusamala makolo anga kapena kukwatiwa
Chipembezo: Kupemphera nthawi zonse
Kumvera: kukhala bwenzi labwino
Chuma: kukhala ndi ndalama zambiri
•
•
Thanzi labwino: Kusamala thupi langaMaphunziro: Kukhonza bwino,kupitiliza
maphunziro
Miyambo ya chikhalidwe: Kulemekeza akulu, kupita kuchinamwali
3. Afunseni ophunzira kuti akahale awiriawiri ndipo akawuzane zomwe amakhulupilirat.
ZOYENERA KUDZIWA OTSOGOLERA:
Ndikofunika kuti ophunzira asamve ngati zikhulupililo zake zikuweruzidwa. Cholinga
cha phunziroli sikuweruza zikhulupiliro za ophunzira koma kuwathandiza ophunzira
kuti aganize kuti ziphunziro zawo ndi zotani.
4. Pakatha mphindi zisanu, ophunzira abwerere mmalo awo ndipo muwafunse kuti anene
zikhulupiliro zawo. Mungathe kuzilemba pa bolodi kapena papepala ndipo muzichonga
zomwe zabwerezedwa. Muwafunse kuti:
•
•
Pali zikhulupiliro zina zomwe ndi zofanana kwa ophunzira onse zomwe sizinatchulidwe
kwambiri?
Kodi zinali zophweka kapena zovuta kukambira zikhulupiliro zawo?
Ntchito 2: Mtengo wa ndalama
Mphindi 20
1. Akumbutseni ophunzira za zikhulupiliro zawo ndikuwakumbutsa kuti zomwe amakhulupilira
zimakhuza ziganizo zomwe amapanga . Awuzeni ophunzira kuti pakhala nthawi yowona
momwe zikhulupiliro zawo zingakhuzire ziganizo zomwe amapanga pofuna kupeza kapena
kugwirisa ntchito ndalama.
2. Afunseni ophunzira onse kuti ajambule mtengo ( papela kapena pansi) afotokozereni kuti
mtengo wina uli wonse ukuyenera kukhala ndi masamba akulu akulu pakati pa 8 ndi 10
ndi mitsitsi ikulu ikulu ya pakati pa 5 ndi 8. Thunthu la mtengo likhonda kukhala laling’ono.
Afotokozereni kuti masamba matengo akuyimira mmwe amagwiritsira ntchito ndalama
zawo. Afunseni ophunzira kuti alembe pa tsamba lilonse zinthu zomwe amagula akakhala
ndi ndalama. Chinthu chili chonse chilembedwe pa tsamba lakelake. Mitsitsi ya mtengowo
ikuyimira njira zopezera ndalama . Afunseni ophunzira kuti alembe pa mitsitsi mmene
amapezera ndalama ndi komwe amakapeza ndalama.
3. Afunse ophunzira mafunso awa:
•
•
•
Zomwe aphunzira pojambula mtengo
Zilipo njira zomwe mungachepetsere kuononga ndalama kapena kusintha kuti
muzigwiritsa bwino ntchito ndalama zanu?
Ndi zinthu ziti zomwe mwalemba pa masamba zomwe mumazifunadi
101
•
•
Nanga ndi ziti zomwe simumazifuna koma mumangogula
Mumangogula chifukwa chani? Ayikeni mayankho awo mumagulu, mwachitsanzo
“chifukwa znanga li nazo” zimandipangitsa kuti ndioneke kuti ndine wapamwamba” ndi
zina zotero.
4. Akumbutseni ophunzira za zikhulupiliro zawo zimene analemba . Afunseni mafunso awa:
•
•
•
Kodi zifukwa zomwe zimawapangitsa kugula zinthu izi zimaonetsera azomwe
amakhulupilira
Zikhulupiliro zake ndi ziti?
Koma amatsutsana ndi kulimbana ndi zikhulupiliro zawo?
5. Afunseni ophunzira kuti awone njira zomwe amapezera ndalama. Afunseni mafunso awa?
•
•
•
•
•
•
•
Kodi njira zomwe ampaezera ndalama zikuonetsa zomwe amakhulupilira?
Kodi zilipo njira zina zopezera ndalama zomwe simungazichite? Njira zake ndi ziti?
Nanga ndi chifukwa chain simungazigwiritse ntchito?
Chimachitika ndi chain munthu akakhala ndi zikhulupiliro ziwiri zomwe zikuoneka
ngati zikutsutsana? Mwachitsanzo mtsikana wina makhulupilira kuti akhale ndi zovala
zatsopano komanso kukhala moyo wathanzi ndi wautali. Kodi akhale pa chibwenzi ndi
abambo akulu akulu kuti azimupatsa ndalama koma akhale pa chiopsezo chotenga
kachirombo ka HIV? Kodi angatani kuti akwaniritse zikhulupililo zake zonsezi
Kodi ndi chifukwa chani nthawi zina sitimatsatila zomwe timakhulupilira?
Kodi anzathu apatipangitsa bwanji kuti tisinthe kapena kuyiwara zikhulupiliro zathu?
Kodi tingatani kuti tisunge zomwe timakhulupilira?
Kodi ngati abwenzi tingathandizane bwanji kusunga zikhulupiliro zathu?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Athokozeni ophunzira potenga nawo mbali komanso chifukwa cha zomwe aphunzira?
2. Alimbikitseni ophunzira kuti azikambirana ndi abale awo zokhuzana ndi zomwe amakhulupilira.
3. Akumbutseni ophunzira za mbali yofunikira kwambiri yomwe angachite pothandizana wina
ndi mzake kuti asunge zikhulupiliro zawo.
102
Phunziro Lotsatira?
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
103
Gawo 19
Kugonana ndi bwenzi lako lokha
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira aone mwakuya ngati ziri zotheka kwa mtsikana wa zaka
14 kulonjeza kuti azigonana ndi munthu mmodzi yekha ndi zotsatila
zakusasunga lonjezoli.
Zolinga Zaphunziro: Pamapeto paphunziroli ophunzira aphunzira:
1. Awuzeni kuopsa kokhala ndi mabwenzi ogonana nawo ambiri.
2. Pezani njira zomwe munthu angazigwiritse ntchito kuti akhale ndi
bwenzi logonana nalo limodzi.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Jambulani bokosi pansi (kapena yikani pepala pansi) kutsogolo kwa
kalasi lofanana mulitali ndi muli fupi.
Ntchito yoyamba: Ndikulonjeza koma nanga…?
Mphindi 40
1. Funsani mnyamata mmodzi ndi mtsikana mmodzi kuti abwere kutsogole .
2. Awuzeni ophunzira kuti anzawo omwe abwera kutsogolowo ali ndi zaka 14 aliyense: Maria
ndi bwenzi lake Kwame. Iwo ali pa chibwenzi ndipo agwirizana kuti azigonana. Akunena kuti
sazigonana ndi munthu winanso.
3. Afunseni achinyamata omwe ali kutsogolowa kuti ayime pa pepala lomwe lili kutsogolo lija
ndipo awuzeni ophunzira kuti pepalali likuyimira kama wa Maria ndi Kwame.
4. Afunseni ophunzira kuti akambirane:
•
•
Kodi chcingamuthandize Maria ndi Kwame kuti asunge lonjezo lawo ndi chani?
Nanga chomwe chingapangitse kuti kukhale kovuta kukwanitsa ndi chani?
5. Awuzeni ophunzira kuti aganize kuti Maria ndi Kwame asunga lonjezo lawo. Afunseni mafunso
awa:
•
104
Ndi anthu angati omwe ali pa kama? (Yankho: awiri
•
•
•
•
•
•
Kodi izi zingabweretse chani pa moyo wawo?
Chinamuthandiza Maria ndi Kwame kuti asunge lonjezo lawo ndi chani?
Kodi chiopsezo chawo ku HIV ndi matenda ena opatsirana pogonana ndi chani
Nanga anthuwa ali pa chiopsezo chanji?
Kodi ndi zoona kuganiza kuti anthu awiri azaka 14 angathe osakhala ndi mabwenzi ena
ogonana nawo
Kodi angatani kuti asagonanenso ndi munthu wina
6. Kodi Maria ndi Kwame sangathe kusunga lonjezo lawo angachite chani? Tsopano muwawuze ana
suluku kuti Maria ndi Kwame amagonananso ndi anthu ena. Ophunzira asankhe Maria kapena
Kwame ndipo osankhidwayo apite akasankhe munthu wina ndipo abwere naye pa kama paja.
Funsani mafunso awa:
•
•
•
•
•
•
•
Ndi anthu ngati omwe ali pa kama?
Ndi zikukwa ziti zomwe zingamupangitse Kwame kapena Maria kugonana ndi munthu
wina?
Kodi chiopsezo chawo ku HIV kapena matenda opatsirana pogonana ndi chotani
tsopano?
Zotsatila za khalidwe ili ndi zotani? What are the consequences of this behavior?
Ngati Maria ndi Kwame anagwirizana kuti sazagonana ndi munthu wina, kodi yemwe
akugonana ndi munthu winayo ndi wokhulupilika?
Kodi yemwe akugonana ndi munthu winayo angabweretse mavuto anji kwa mzakeyo?
Nanga iwo angatani?
7. Awuzeni ophunzira kuti aganizire kuti Maria ndi Kwame onse akugonana ndi munthu wina.
Maria kapena Kwame apite akasankhe munthu wina bwere naye pa kama paja. Funsani
mafunso awa:
•
•
•
•
•
•
•
•
Ndi anthu angati omwe ali pa kama paj atsopano
Kodi ndi chifukwa chani Maria ndi Kwame akugonana ndi anthu ena
Kodi zotsatila za khalidwe limenli ndi zotani kwaonse awiri?
Nanga chiopsezo chawo ku HIV ndi Matenda opatsirana pogonana ndi chotani?
Kodi Maria ndi Kwame ndi okhulupilirika kwa wina ndi mzake?
Kodi Maria ndi Kwame ali ndi udindo wanji kwa wina ndi mzake?
Nanga ali ndi udindo wanji kwa anthu ena omwe akugonana nawowo?
Nanga angachite chani?
8. Tsopano afunseni ophunzirawo kuti aganizire kuti anthu ena omwe amagonana ndi Maria ndi
Kwame alinso ndi anthu ena ogonana nawo. Afunseni kuti awiri ena anayitanidwa aja akatenge
anzawo ena. Funsani mafunso awa:
•
Ndi anthu angati omwe ali pakama ndi Maria ndi Kwame (yankho: 6)
9. Ophunzira aganizenso kuti anthu ena omwe ali pakama paja alinso ndi anthu ena ogonana
nawo. Afunseni kuti nawonso akatenge anzawo ogonana nawo ndi kubwera nawo pa kama
paja.
105
10.Afunseninso ena kuti abwere pakama paja kufikira anthu onse mkalasimo atabwera pakama
paja. Izi zikhonza kukhala zosangalatsa kwa ophunzira chifukwa azikanganirana malo papepala
paja. Akankhana kankhana afunseni mafunso awa:
•
Ndi anthu angati omwe ali pa bedi la kWame ndi Maria tsopano?
11.Muwawuze ophunzirawo kuti modzi wa iwo ali ndi kachilombo ka HIV komanso wina ali
ndi matenda opatsirana kudzera pogonana. Koma munthu yemwe ali ndi matendawa
sangadziwike pakungomuona momwe akuonekera. Funsani mafunso awa:
•
•
•
•
Chiopsezo cha HIV ndi matenda opatsirana kudzera pogonana ndi chotani
Kodi ophunzirawa anali okhulupirika ngati analonjezana ndi bwenzi lawo kuti
sazagonana ndi wina?
Kodi ophunzirawa ali ndi udindo wanji kwa wina ndi mzake?
Nanga achite chani tsopano?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Afunseni ophunzira kuti afotokoze chomwe aphunzira mu phunzirori chomwe chiri
chothandiza kwa iwowo.
2. Akumbutseni ophunzira za gawo la kupanga chisankho pamene anapanga sewero lowomba
mmanja kawiri nthawi ina ili yonse yomwe panali ganizo labwino. Ophunzira aganizire bwino
za ganizo lina lirilonse lokhuza kukhala ndi bwenzi limodzi kapena ambiri ogonana nawo. Vuto
lokhala ndi abwenzi ambiri ogonana nawo ndi lotani?
3. Awuzeni ophunzira kuti ngakhale zingakhale zosangalatsa kukhala ndi zibwenzi zambiri
zogona nazo, zotsatira zake ndi zoipa kwambiri.
4. Akumbutseni ophunzira za phunziro lomwe anaphunzira njira zina zoonetsera chikondi kwa
wina ndi mzako pambali pakugonana. Ophunzira anene njira zina zomwe Maria ndi Kwame
akanachita kuti awonetse chikondi kwa wina ndi mzake.
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
106
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 20
Zotsatira za kumwa mowa
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira awunikire momwe mowa ungawalepheretsere kukwaniritsa
masomphenya awo ndipo aganizire za mfundo zomwe zingawathandize
kuti asamamwe mowa mwa uchidakwa.
Zolinga za phunziro: Pamapeto pa phunziroli ophunzira aphunzira izi:
1. Kufotokoza malamulo okhuza mowa kwa anthu amsinkhu wawo.
2. Ndi chifukwa chain anthu achinyamata ena amamwa mowa.
3. Kufotokoza zotsatila za kumwa mowa.
4. Kupeza njira zothanziza kuti asamamwe mowa kapena asamamwe
mwa uchidakwa.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Kuwunika malamulo okhuza kumwa mowa ndi zaka zoyenera kumwa
mowa ndi chilango chimene chimaperekedwa kwa achinyamata,
eni ake malo ogulitsa ndi kumwera mowa ndi ena otero akalakwira
malamulowa.
Ntchito 1: Owa ndi masomphenya athu
Mphindi 10
1. Afunseni ophunzira kuti anene kuti ndi chani chomwe chimabwera mumaganizo awo akamva
mawu akuti mowa. Lembani pa bolodi zonsezi.
2. Jambulani chithunzi cha ophunzira , mbali inayi lembaniko mawu akuti masompohenya.
3. Fotokozani kuti munthu ukamwama mowa, umachita zinthu zomwe ulu bwino bwino
sungachite. Munthu samaganiza bwino akamwa mowa. Afunseni ophunzira kuti ndi zinthu
ziti zimene anthu amachita akamwa mowa zomwe sangachite akakhala kuti ali bwino bwino.
Funsani kuti apereke zitsanzo. Afunseni kuti zimenezi zingawalepheretse bwanji kukwanilitsa
masomphenya awo. Ngati kuli kotheka patseni chitsanzo chogonana mosadziteteza.
Kugonana kosadziteteza kukhonza kuwalepheretsa kukwaniritsa masomphenya awo chifukwa
kungapangitse kuti atenge mowa yosayembekezera komanso kachilombo ka HIV ndi zina.
107
4. Pa chitsanzo china chirichonse chomwe ophunzira apereka, afunseni kuti zingalepheretse
bwanji kukwaniritsa masomphenya. Ophunzira onse akanena awuzeni kuti alembe
cholepheretsa pakati pa chojambula chija ndi komwe kunalembedwa masomphenya kuja.
5. Onse akamaliza kujambula chorepheretsachi afunseni ophunzira awerenge kuti zolepheretsa
zilipo zingati ndipo muwawuze kuti mowa umalepheretsa kukwaniritsa masomphenya athu.
Malingana ndi zomwe zajambulidwa afunseni ophunzira kuti anene kuti ndi chifukwa chani
achinyamata amamwa mowa ngakhale amadziwa kuti mowa umalepheretsa kukwaniritsa
masomphenya awo.
ZOYENERA KUDZIWA OTSOGOLERA:
Muphunziro iri mukhonza kukambamo za mankhwala ena ozunguza bongo.
Ntchito yachiwiri: Kuganiza musanachite
Mphindi 30
Fotokozani kwa ophunzira kuti mbali ya chiwiri ya phunziroli iyankha funso lakuti ‘chifukwa chani’
pogwiritsa ntchito nthano.
Werengani nthano ya Lute
Lute anayamba kumwa mowa (vinyo) wokoma kukhala zochitika zosiyana siyana
monga ngati pa mwambo wa sadaka.Akulu amakhala pakhomo, kugawana chakudya
ndi zakumwa, achinyamata amakakhla kwa okha ku mdima kumamvetsera nyimbo
ndikumwa mowa.Nthawi zambiri kukhala sadaka kumakhalanso mowa. Poyamba Lute
amakana kumwa mowa koma mazimzkake amamuseka kuti ndi mwana. Iye amafuna
nayenso akhale nawo mugulu lija komanso kuti akhale wamkulu ndipo achinyamata
onse omwe amawasirira amamwa mowa. Izi zinamupangitsa kuti nayenso ayambe.
Poyamba amasangalala ndi momwe amamvera akamwa, kutentha, kutchuka komanso
kufuna zogonana-koma kenako anaymaba kumva kuwawa mmimba ndi mutu. Lute
anapanga chisankho kuti sadzamwanso. Koama kuli sadaka ina, mnyamata wina
yemwe amamukonda-Mapi- anamupatsa mowa ndipo anamupangitsa iye kumva kuti
ndiofunikira kwambiri. Ndiye lute anavomera. Iye ndi Mapi anamwa mowa wawo ndi
kukhala paokha kumakamwa ndi kukamba nkhani zawo. Lute sakanatha kudziwa kuti
anamwa mowa wochuluka bwanji komanso zomwe zinachitika koma akuganiza kuti
Iye ndi Mapi anagonana-ngakhale amaganiza kuti anakana.
1. Kodi ndi zovuta ziti zomwe zingakhale zotsatila za khalidwe la Lute lakumwa mowa? Zina mwa
zovutazo zikhonza kukhala monga: kudwala mmimba/mutu, matenda opatsirana pogonana,
kugwiriridwa, kutenga mamba/ matenda opatsirana pogonana kapena HIV, kudzichotsera
ulemu wake ndi zina zotero.
108
2. Ndi chifukwa chani Lute anaganiza zomwa mowa? Zifukwa zina zitha kukhala monga: chifukwa
chofuna kukhala ngati anzake, samafuna kunyozeka, amafuna kuti mzake mapi amukonde ndi
zina zotero.
3. Tsopano poti tadziwa zina mwa zifukwa zomwe zinamupangitsa Lute kumwa mowa tiyene
tibwerere mmbuyo timuthandize Lute kuonanso ubwino ndi kuona kwa ganizo lina lirilonse
lomwe anapanga.
4. Akumbutseni ophunzira za nkhani yakupanga chisankho pamene mumawafunsa ophunzira
kuomba mmanja kawiri nthawi yomwe pakufunika kupanga chisankho. Afunseni ophunzira
za zisankho zomwe Lute mayenera kuchita. (Mwachitsanzo kumwa mowa atasekedwa ndi
anzake,asamwenso mowa chifukwa choti unamudwalitsa, kumwa mzake Mapi atamufunsa
kuti atero, kuchokapo onse limodzi ndi Mapi ndi zina zotero).
5. Tiyeni timuthandize Lute poyerekeza kuti tabweza nthawi mmbuyo ndipo zomwe zinachitikazo
sizinachitike. Tiyang’ana ganizo lina lilinse (ndi kuomba mmanja kawiri) ndikuganizira za
ubwino ndi kuipa kwa chisankho china chili chonse chimene anapanga.
6. Kuyang’ana za chisankho china chiri chonse, kodi angachite bwanji kuti apewe chiopsezo
chomwe angakhale nacho chifukwa cha kumwa mowa pa zifukwa zimene anapereka?
Mwa chitsanzo:
Ndi chifukwa chani anamwa? Samafuna kusekedwa
Ombani m’manja kawiri
Chomwe akanachita mmalo momwa mowa
Kumvera nyimbo ndi achinyamata ena koma akhlale ndi mzake wina yemwe samamwa ndipo
alonjezane kuti alimbikitsana kuti asamwe mowa.
Anamwa chifukwa chani Samafuna kunyozedwa .
Ombani mmanja kawiri
Kupeza njira mmalo mwakumwa
Gwiritsani ntchito kuyankhula mozidalira Sizimandisangalatsa mukamandi nyoza chifukwa
ndimmamva ngati sine mmodzi wa inu ndikufuna kuti musiye zimenezi.”
Ndi chifikwa chani anamwa? Amafuna kumusangalatsa Mapi
Ombani kawiri
Kusankha njira yina mmalo mwakumwa
Amuyitane Mapi kuti akacheze naye pamodzi ndi mzake Mary mmalo mwakumwa.
109
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Ombani mkota mofotokozanso kuti zotsatila za kumwa mowa zingalepheretse kukwaniritsa
masomphenya.Afunseni ophunzira kuti kuti apereke zitsanzo. Mwachitsanzo; Ngati lute ali ndi
mamba sangathe kupitiliza maphunziro ake.
2. Akumbutseni ophunzira kuti aliyense ali di chifukwa chimene amamwera mowa . Awuzeni
ophunzira kuti aganizire paokha za Lute ndi zifukwa zomwe anamwera mowa (samafuna
kunyozedwa, amafuna kuti amzake asamusale, amafuna Mapi kuti amukonde).
3. Onaninso za malamulo okhuza kumwa mowa.
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
110
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 21
Kugwiritsa ntchito kuyankhula ngati njira yodzitetezera
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira aphunzire njira zosiyana siyana zoyankhulirana kuti ziathandize
kuziteteza.
Zolinga zaphunziro:
Pamapeto pa phunziroli ophunzira aphunzire:
1. Kufotokoza njira zisanu za momwe tingagwiritsire kuyankhulana kuti
titetezeke.
2. Kuwiritsa ntchito njira zoyankhuliraan kuti achipetse chiopsezo
chawo chogwiriridwa.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Kudziwa bwino za njira zoyankhulirana ndi zitsanzo zomwe zili mu
ntchito 1.
Ntchito 1 kuyankhula! Kukambirana! Kuthawa!
Mphindi 40
1. Awuzeni ophunzira kuti aphunzira njira yomwe ingawathandize kuthana ndi zovuta zomwe
angakumanae nazo.
2. Fotokozani njira zisanu zoyankhulirana pogwiritsa ntchito zitsanzo zili musizi. Chitsanzo: “Popita
kunyumba mnyamata akumukakamiza khrise kuti agonane naye Mtsikanayo sakufuna chifukwa
ndi namwari.”
111
Momwe mungachitile
Chitsanzo
Kukhala ozodalira
Gwiritsani ntchito izi kuti
kufotokoza momwe mukumvera:
Ndikumva ngati
Ukama
Chifukwa…
Ndipo ndikufuna
Ndimamva kukamizidwa
ukamandiuza kuti ndigonane
nawe chifukwa ndilamulo la
kutchalitchi kwa kuti ndizisunge
mpakana ndizalowe mbanja
nndiye ndikukupempha kuti
usiye kundivutitsa.
Kanani
Yankhulani molimba mtima
Gwiritsani ntchito ayi ngati
yankho lanu.
Ayi. Ndikutanthauza ayi
Ndakana sindikufuna kugonana
nawe
Imitsani zokambirana kufikira
nthawi yina mutaganiza bwino .
Sindingakupatseni yankho
lero chifukwa ndikufuna
ndikayankhule kaye ndi abusa
nga kuti nditani. Ndikawafunsa
lamulungu likubwerari
Pemphani
Pangani chiganizo chomwe
nonse mungagwirizane nacho.
Sindingagonane nawe koma
utha kupita nane kutchalitchi ndi
anthu akathu.
Thawani/pewani
Chokani pamalo pomwe
mukuwona kuti mungathe
kuchitidwa chipongwe.
Njira yoyankhulirana
Dikilani
Ngati mnyamata akumuopseza
khrise azingopita osamuyankha
kapena abwerere kusukulu
akawawuze aphunzitsi kuti
amuthandize.
ZOYENERA KUDZIWA OTSOGOLERA:
Afotokozereni kuti njira zonse zoyankhulirana ndi zothandiza nthawi ina ili yonse.
Musawone ngati mwalakwitsa mukapanda kunyengerera kapena kukambirana.
Mukawona kuti ndinu wosatetezeka thawani kapena chokanipo pamalopo.
3. Zitsanzo zina za momwe mungayankhulilane ziri kumapeteku.
4. Agaweni ophunzira mumagulu okwana asanu. Mugulu lirilonse mukhale anyamata ndi atsikana.
5. Lipatseni gulu lirilonse chimodzi mwa zochitika zokhuza njira zoyankhulirana zomwe ziri
kummapeto kwa phunzirori.
6. Gulu lirilonse likonzekere kupanga sewero lowonetsa njira yoyankhulirana yomwe
yaperekedwa ku gululo ndi momwe njirayo ingawathandizire pankhani yomwe awerenge.
112
7. Apatseni nthawi ophunzira yokonzekera sewero lawo.
8. Awuzeni onse kuti akhalenso pamodzi. Afunseni onse kuti awonetse njira zoyankhulirana
zosiyanasiyana kufikira njira zonse zoyankhulirana zitawonetsedwa
9. Onse akamaliza kuwonetsa sewero lawo, afunseni:
•
•
•
•
•
Ndi zovuta ziti zomwe anakumana nazo mmene amapanga masewerowa?
Ndi njira yiti yoyankhulirana yomwe inali yophweka. Ndi chifukwa chani?
Ndi jira iyi yoyankhulirana yomwe ikumakuwonekera yophweka? Chifukwa chani?
Ndi njira ziti zoyankhulirana zomwe ziri zothandiza mukakhala pa chiopsezo?
Ndi njira ziti zoyankhulirana zomwe ziri zosathandiza mukakhala pa chiopsezo?
10.Afunseni kuti anyamata angatani ataona mnyamata mzawo akuchita zoyipa kapena
kukakamiza mtsikana kuti agonane naye?
11.Ophunzira angatani kuti azithandizana?
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Awuzeni ophunzira kuti pogwiritsa ntchito njira zoyankhuliranazi, angathe kupeza njira
zothanirana ndi chiopsezo chomwe akumana nacho.
2. Tsindikani kuti nthawi yina iriyonse yomwe ophunzira awona kuti ali pa chiopsezo achite
chotheka kuchokapo ndi kukapeza thandizo.
3. Malizani ndi kuwawuza ophunzira kuti akuyenera kukhala othandizana. Akhonza kuyesera
zomwe aphunzira poonetsetsa kuti akuyendera limodzi kuti athe kutetezana.
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
113
Zitsanzo za ntchito 1
a. Marita amapita kunyumba kuchokera kusukulu ndipo anadutsa njira yachidule yodutsa
mumunda momwe munali chimanga chitali chitali. Pamene amadutsa pomwe panali
chimanga chambiri komanso chitali chitali, mnyamata wina wamkulu wa kusukulu kwawo
anamudumphira Marita. Anamuuza kutiasakuwe.Mnyamatayo anamuua Marita kuti
amayerekedwa chifukwa ndi namwari ndiye akufuna amuonetse kuti sangakane amuna. Kodi
Marita anene kuti chani nanga achite chani kuti kuti aziteteze? Njira yoyankhulirana-kuthawa/
kupewa.
b. Bambo wanyumba yoyandikana ndi ya kwa Esime anamuza kuti akufuna kuti Esime apite
kunyumba kwake akamuthandize ntchito zapakhomo. Bamboyo anamuuza Esime kuti kuti
poti iye ndi mzawo wa bamboo ake, azimutenga ngati wachibale ndipo azimuyitana kuti
amalume. Esime samawakonda malumewa chifukwa samamasuka komanso amakhala ndi
mantha akakhala pafupi. Amzake ena anamunong’oneza kuti amalumewa mawagwiragwira.
Kodi Esime anganene chani kwa amalumewa. Njira yoyankhulirana-kudikira.
c. Mayi ake a Peturo anali ndi anzawo omwe amuna awo anamwarira ndipo amakonda kukhala
ndi chidwi ndi maphunziro a Peturo. Makolo a Peturo atalephera kumulipilira sukulu, Mayiyu
anadzipereka kuti amulipirira akalora kumuthandiza ntchito zapakhomo. Peturo anavomera.
Zonse zinayamba bwino koma kenako anayamba kmufunsa mafunso achinsinsi okhuza
bwenzi lake komanso zomwe amakonda. Tsiku lina atapita kunyumba kwawo anayamba
kumugwiragwira. Kodi Peturo awawuze chani amayiwa amasiyewa Njira yoyankhulirana
-Kuwadandaulira–
d. Tsku lina taweruka aphunzitsi ake a Sara anamuuza kuti akawasiyire mabuku awo kunyumba
kwawo. Atafika kunyumba napeza kuti analimo yekha mnyumbamo. Anamufunsira ndipo
anamuuza kuti alowe m’nyumba. Sara awawuze kuti chain aphunzitsiwa? Njira yoyankhuliranakukana.
e. Madalitso amakonda sukulu koma amakhala ndi nthawi yochepa yowerenga chifukwa ali
ndi abale ake ena ng’ono ang’ono okwana asanu. Akamamaliza ntchito zapakhomo madzulu
amakhala atatopa ndipo skhala ndi nthawi yolemba ntchito yomwe aphunzitsi anamupatsa
kusukulu. Lero iye anali osangala pamene aphunzitsi anamutchula mkalasi ya masamu chifukwa
maona ngati akudziwa yankho lake. Koma malakwitsa. Aphunzitsi anamuseka ndi kunena kuti
aliyense akudziwa kuti akazi sakhonza masamu . Anamuuza Madalitso kuti akungotaya nthawi
yake kumapita kusukulu, kuli bwino angopeza mwamuna kuti amukwatire. Kodi amzake
aMadalitso komanso Paul awauze chain aphnzitsiwa? Njira yoyankhulirana –Kuzidalira.
114
Njira zina zoyankhulirana o
Chitsanzo: “Aphunzitsi amuna amene amatchuka ndi kupanga zibwenzi ndi atsikana ang’ono
ang’ono amuuza mtsikana wa folomu 4 kuti akawasiyire mabukhu kunyumba kwawo’
Njira yoyankhurilana
Mungayankhule bwanji
Chitsanzo
Kukhala ozidalira
Gwiritsani ntchito izi
kufotokoza maganizo anu :
Ndikumva ngati…
Mukamandi…
Chifukwa …
Ndipo ndikufuna …
Ndimamva kumasuka
mukamandiperekeza
kunyumba chifukwa
ndinu aphunzitsi anga
ndipo sizoyenera kuti
ndipite kunyumba kwanu
ndipo ndikupempha
musazanduuzenso zimenezi.
Kukana
Nenani molimba mtima .
Kanani kotheratu.
Ndakana! Ndakana ndithu
Ndakana sindipita nanu
kunyumba
Kuchedwa/kudikira
Musafulumire kuyankha
kufikira mutaganiza bwino
kapena kuchoka malo
osatetezeka.
Zikomo pondipempha kuti
ndikuperekezeni aphunzitsi.
Koma ndikawafunse kaye
makolo anga. Ndikawuza
ndipo ndizakuwuzani mawa
Kukambirana
Pangani chiganizo chimene
nonse mugwirizane nacho.
Sindingakuperekezeni
chifukwa makolo anga
sangandilore, komandikhonza
kukuperekezani mpaka
pamete pathera malo asukuyi.
Kuthawa/kupewa
Chokani pamalo pamene
mukuona kuti chitetezo
cahnu ndi chochepa kapena
mukhonza kuchitidwa
chipongwe.
Musayankhe muzingopita.
Kapena yendani nawo
aphunzitsi koma mukafika
pakhomo pa nyumba yawo
thawani.
115
Chitsanzo: “Abambo akulu agalimoto yawo anamuuza mtsikana wa sitandadi 5 kuti akakwera
mgalimoto yawo amugulira mowa komanso amupatsa ndalama.
Njira yoyankhurilana
116
Mungayankhule bwanji
Chitsanzo
Kukhala ozidalira
Gwiritsani ntchito izi
kufotokoza maganizo anu :
Ndikumva ngati…
Mukamandi…
Chifukwa …
Ndipo ndikufuna …
Sindingavomere kukwera
galimoto yanu chifukwa
sindikukudziwani ndipo
musadzandiuzenso kuti
ndikwere galimoto yanu.
Kukana
Nenani molimba mtima .
Kanani kotheratu.
Ndakana
Sindikufuna
Ndakana sindikwera o.
Kuchedwa/kudikira
Musafulumire kuyankha
kufikira mutaganiza bwino
kapena kuchoka malo
osatetezeka.
Zikomo pondipempha kuti
ndikwere nawo galimoto yanu
koma ndikawapemphe kaye
makolo anga.
Kukambirana
Pangani chiganizo chimene
nonse mugwirizane nacho.
Izi ndi zovuta chotero
kukambirana sikungathandize.
Kunama kungathe kuthandiza
di cholinga choti uchokepo.
Chokani ndikukawuza munthu
yemwe mukumudalira.
Kuthawa/kupewa
Chokani pamalo pamene
mukuona kuti chitetezo
cahnu ndi chochepa kapena
mukhonza kuchitidwa
chipongwe.
Musayankhe, thawanirani ku
malo komwe mungakhale
otetezeka.
Gawo 22
Kulemekeza kale lathu, kusunga tsogolo lathu
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira awonenso bwino za chikhalidwe chawo ndi momwe
chikuwirizirana ndi chiopsezo.
Zolinga za phunziroli: Pamapeto pa phunziroli, ophunzira aphunzira
1. Zikhalidwe zomwe zimalimbikitsa kuti amunthu akhale ozilemekeza,
olemekeza thupi lake komanso la anthu ena
2. Zikhalidwe zomwe zili zoyipa komanso zingathe kuyika munthu pa
chiopsezo.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
Palibe
Ntchito 1: Chikhalidwe chathu chimatiuza kuti
Mphindi 25
1. Yambani ndi kuwafunsa ophunzira mafunso awa Ndizinthu ziti zomwe zili mu chikhalidwe chathu?
•
•
•
•
Kuti zikhalidwe zimenezi ndi zothandiza? (mwachitsanzo, khalidwe loyang’anira abale
ena ndi ana amasiye)
Zikhalidwe zina ndi zoipa l? (Mwachitsanzo abambo akulu akulu kumagona ndi atsikana
ng’onong’ono ndi cholinga chowakhwimitsa.)
Pali zikhalidwe zina zomwe ndi zoipa komanso zabwino? (Mwachitsanzo, amayi kukana
kugonana ngati njira yorela zimathandiza mayi komanso mwana uja kukula bwino.
Koma ngati bamboo asakudziletsa, thanzi la mayi, bamboo ndi banja lonse likhonza
kukhuzidwa ngati bamboyo akuchita zachiwerewere mosadziteteza, kugwiritsa ntchito
ndalama zomwe banja lija likanagwiritsa ntchito ndi kutenga kachilombo ka HIV
Kodi zikhalidwe zimasintha kapena zimakhala chimodzi modzi? Zikhalidwe zina zinali
zothandiza kale kale koma pano zinthu zinasintha chotero ndipofunika kusintha kapena
kuthetsa zikhalidwe zoterezi. Mwachitsanzo kuwaphunzitsa atsikana kugonana ndi
amuna kulu akulu akatha msinkhu zinali zothandiza kwa atsikana akakwatiwa kale kalero
ndipo kunalibe HIV. Masiku ano atsikana amapita kusukulu, ndikukwatiwa akamaliza
sukulu komanso ali pa chiopsezo chotenga kachilombo ka HIV ngati angachite zomwe
anaphunzitsidwa ku chinamwali.
117
2. Awuzeni ophunzira kuti zikhalidwe zikusintha mu madera osiyanasiyana. Izi ndi zabwino
chifukwa malo omwe tikukhala nawonso akusintha choteo ndikofunika kusintha kuti miyoyo
yathu nayo isinthe.
3. Awuzeni ophunzira kuti ndikofunika kuganiza bwino za momwe tingasungire ndi kulimbikitsa
zinthu zomwe ziri zabwino zokhuza chikhalidwe chathu ndi kusintha kapena kusiya zomwe
ziri zoyipa.
4. Agaweni ophunzira mumagulu, anyamata amsinkhu umodzi akhale gulu limodzi
chimodzimodzinso atsikana. Funsani gulu lilonse kuti lilembe malangizo omwe amalandira
kuchokera kwa akulu akulu okhuza kukula ndi nkhani zogonana komanso zokhuza kukhala
mwamuna kapena mkaziweniweni.
5. Gulu lilonse lisankhe langizo limodzi kapena awiri ndipo alembe ubwino walangizo limeneli
kmanso kuipa kwake.
Ntchito 2: Zikhalidwe zomwe ndingasunge…
zikhalidwe zomwe sindingazisunge
Mphindi 19
1. Ngati ziri zovomerezeka awuzeni ophunzira abwerere mmumalo awo ndipo kambiranani za
malangizo kapena miyambo yomwe analemba ija . Ngati ziri zosaloledwa kuti onse akhale
pamodzi, aphunzitsi amuna akhale ndi anyamta paokha ndipo aphunzitsi akazi akhalenso ndi
atsikana paokha.
2. Mu gulu lirilonse kambiranani ubwino ndi kuyipa kwa malangizo omwe analembedwa.
Awuzeni ophunzira kuti akuyenera kuvotera khalidwe lina lirilonse ndipo mavoti atsikana ndi
anyamata awerengeredwa ndi kulembedwa. Pa langizo kapena mwambo uli wonse funsani
mafunso awa:
•
•
•
•
Ndi angati omwe akuganiza kuti mwambo kapena langizoli likhale choncho?
Ndi angati akuganiza kuti mwambowu kapena langizoli lisiyidwe?
Ndi angati akuganiza kuti lisinthidwe?
Ngati mukufuna kusintha mwambo, mukufuna usinthe bwanji?
3. Kwa ophunzira omwe anamva kuti miyambo yina ikuyenera kuthetsedwa kapena kusinthidwa,
akuganiza kuti iwoiwo ngati ophunzira angachitepo chani kuti izi zitheke?
4. Alangizeni ophunzira kuti kuti akambirane ndi abwenzi awo, abale kapena oyandikana nawo
nyumba zokhuza mwambo kapena langizo lomwe akufuna lithetsedwe kapena lisinthidwe
pofunsa mafunso awa.
118
5. Mukufuna mutasintha, nanga tingasinthe bwanji. Ophunzira akuyenera kudziwa kuti kukamba
za miyambo monga yachinamwari kukhonza kukhala kovutilapo chotero adziwe kuti anthu
ena sangafune kukambirana za nkhani imeneyi. Omwe sakufunawo asawakakamize.
ZOYENERA KUDZIWA OTSOGORELA:
Kukamba zokhuza chinamwari kuknza kukhala kovutilapo chotero aphunzitsi awone
ngati kuli koyenera kuti ophunzira akambe nkhani ngati imeneyi.
Kuomba mkota
Mphindi imodzi
1. Ayamikireni ophunzira chifukwa cholora kukambirana nkhani zimenezi.
2. Akumbutseni ophunzira kuti zikhalidwe zikusintha ndi kuti ngakhale tikufuna kusataya
chikhalidwe chathu tiganizenso za tsogolo lathu.
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
119
Gawo 23
Kodi Ndiri pa chiopsezo?
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Ophunzira afufuze za zinthu zomwe anyamata ndi atsikana amachitira
limodzi ndipo alembe kuopsa kwa chili chonse.
Zolinga za phunziro: Pomaliza phunziroli ophunzira aphunzira.
1. Makhalidwe omwe amapangitsa munthu kukhala pa chiopsezo
chotenga HIV.
2. Kupeza njira zochepetsera chiopsezo.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Mu ntchito yoyamba mukuyenera kukhala ndi zitsanzo za zochitika
zomwe ziri zofunika kwa anyamata ndi atsikana ndipo gwiritsani ntchito
chiyankhulidwe chawo. Ganizilani za maphunziro ena ambuyomu
kuti atahandize ophunzira kupeza zitsanzo . Mwachitsanzo, ngati
mukukamba za mowa, tchulani zitsanzo zomwe ophunzira anapereka
monga kukamwa mowa ku mtsinje ndi anzanga. Zinthu zomwe
ophunzira amachita ngati mbali imodzi ya chisangalalo.
Ntchito yoyamba: Izi ndi zosangalatsa komanso zoopsa
Mphindi 40
1. Agaweni ophunzira anyamata ndi atsikana paokha.
2. Funsani gulu lirilonse kuti aganize za machitachita osiyanasiyana kuphatikizapo okhuza
zogonana omwe anyamata ndi atsikana angachite kuti asangalale. Awuzeni kuti aganizire
zinthu zonse zomwe akambirana mumaphunziro ammbuyomu. Apatseni zitsanzo monga
zingapo, monga Kusewera mpira kapena masewera ena ali wonse.
•
•
•
•
•
•
•
120
Kupita kunyumba ndi abwenzi
Kupsopsonana
Kugwiranagwirana malo obisika
Kugonana kugwiritsa ntchito kondomu
Kugonana osagwiritsa ntchito kondomu
Kumvera nyimbo
Kuyankhula ndi abwenzi
•
•
•
•
•
Kupita kuchinamwali limodzi
Kusasa fumbi (kapena miyambo yina yomwe yakambidwa mu phunziro 21
Kukmwa mowa ndi kpita ku malo omwera mowa Kukagula zinthu kumsika
Kugonana ndi abambo
Kupita ku mzikiti/tchalitchi
3. Ophunzira azitchula zomwe alemba ndipo inu muzilembe pa bolodi. Mukalemba zonse pa
bolodi , perekani chochitika chimodzi kwa ophunzira aliyense. Onjezerani machitachita ena
kuti ophuzira aliyense atenge chimodzi.
4. Lembani mzere pansi. Lembani ‘chiopsezo chachikulu’ mbali ina, kapena ikani chizindikiro
chosenya chiopsezo ku HIV. Pakati pa mzere lembani ‘chiopsezo pang’ono’ kapena ikani
chizindikiro chosonyeza chiopsezo pang’ono ku HIV ndipo kumapeto amzere lembani ‘palibe
chiopsezo’ kapena ikani chizindikiro chosonyeza kuti palibe chiopsezo ku HIV.
5. Awuzeni ophunzira kuti aganizire chochitika chomwe apatsidwa ndipo azifunse mafunso awa:
•
•
Machitachita amenewa ali ndi chiopsezo chachikulu, chaching’ono kapena alibe
chiopsezo chotenga HIV?
Ndichifukwa chani ndikuganiza choncho?
6. OPhunzira onse ayime pamzere malo omwe akusonyeza chiopsezo chochitika chomwe
apatsidwa.
7. Kenako afunseni ophunzira kuti ndi chifukwa chani ayima pamene ayimapo.
ZOYENERA KUDZIWA OTSOGOLERA:
Awuzeni ophunzira onse kuti sakufotokoza kapena sakuyikira kumbuyo zomwe iwo
amachita. MMalo ofunsa kuti ‘ndi chifukwa chani umachita zimenezi,’ funsani kuti
‘mukuganiza kuti ana asukulu amachita izi chifukwa chani’
8. Afunseni ophunzira ena kuti anene ngati akugwirizana nazo kapena ayi komanso anene
zifukwa chake. Onetsetsani kuti zokambiranazi ndi zosangalatsa. Onetsetsani kuti zomwe
akukambirana ndi zoona. Mungathe kuonjezerapo mfundo zina zomwe ophunzira
sanazitchule. Onetsetsani kuti pali kugwirizana pakati pa machitachitawa ndi chiopsezo ku
HIV. Mwachitsanzo:
•
•
Kumwa mowa sukungafalitse kachilombo ka HIV koma mutha kufunsa ‘mukuganiza kuti
chimachitika ndi chani anyamata ndi atsikana akamwa mowa limodzi?’ Zimakhala zovuta
kapena zophweka kukana kugonana? Mwamuna yemwe waledzera komanso anagulira
mowa mtsikana angakwiye ngati mtsikanayo angakane zogonana? Chingachitike ndi
chani?
Ngati chochitikacho chiri chofunika ndalama, afunseni ophunzira kuti ‘mwana wa sukulu
ndalamazo amazitenga kuti?’
121
•
Machitachita ena akhonza kukhala ongobisalilako koma cholinga chake chiri choti
achinyamata akagonane. Mwachitsanzo, atsikana khonza kunena kuti ‘akupita kuchigayo
kukagayitsa’ ngati njira yozembera kuti akakumane ndi anyamata kuti akagonane.
Zikhonza kukhala bwino ngati muli ndi zitsanzo zambiri zaterezi.
9. Mutatha kukambirana kwa nthawi yayitali omwe akuona kuti anayima polakwika asunthe.
Koma ngati anayima malo abwino asasunthe koma akhale pansi pa mzerepo.
10.Pitilizani kufikira aliyense atakhala pa mzere. Onjezerani machitachita ena ofunikira makamaka
okhuzana ndi kugonana omwe sanawaganizire.
11.Afunseni ophunzira:
•
•
•
•
Ndi machitachita ati omwe angabweretse chiopsezo chachikulu?
Ndi machitachita ati omwe angabweretse chiopsezo chochepa
Ndimachitachita ati omwe akuoneka achiopsezo chochepa kapena opanda chiopsezo
koma angakhale ndi chiopsezo chochuluka? monga kumwa mowa.
Ndi machitachita ati omwe alibe chiopsezo? Ndi machitachitati omwe munthu
angasangalare nawo omwe sangamuyike pa chiopsezo chotenga kachirombo ka HIV.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Awuzeni ophunzira kuti ndikofunika kuti anyamata ndi atsikana akhale ndi zinthu zomwe
angapange limodzi mosangalala komanso ndi kupewa HIV.
2. Afunseni ophunzira kuti angachite chani kuti athandizane wina ndi mzake kucita machitachita
osangalatsa omwe alibe chiopsezo ku HIV?
3. Afunseni ophunzira zomwe aphunzira kuchokera ku phunziro ili ndi zomwe ali okonzeka
kukthandizana wina ndi mzake
Phunziro lotsatira
1. Thokozani ophunzira chifukwa chotenga mbali pa phunziroli.
2. Kambiranani za momwe phunziro lotsatira lidzayendere:
•
•
•
122
NTHAWI;
MALO; komanso
MUTU/MITU yodzakambirana.
Gawo 24
Kukonza za tsogolo langa
Gawoli mwachidule
Kufotokozera
za gawo:
Kutengera pa zomwe ophunzira aphunzira mumaphunziro amubukhulu,
ophunzira apange mapulani atsogolo lawo Pomaliza phunziro ili
ophunzira aphunzira:
Zolinga za phunziro: Pomaliza phunziro ili ophunzira aphunzira:
1. Kufotokoza ndi kugwiritsa ntchito njira yophweka yopangira mapulani
amoyo wawo.
2. Kutchula masomphenya awo.
Nthawi:
Mphindi 45
Zipangizo
zofunukira:
99 Bolodi/choko/pepala laikulu lolembapo/pentopeni Ophunzira
aliyense akhale ndi pepala ndi cholembera.
99 Ganizilani kuti ndi nthawi yayitali bwanji imene yapitapo kuchokera
pamene munaphunzitsa phunziro lachiwiri kudzafika pano. Mukhonza
kulumpha funso loyamba, ndikufikira funso lachiwiri ngati papita
nthawi yayitali kwambiri Ntchito 1, khwerero 7,ikukhuza kufunsa
ophunzira zokhuza kukhala ndi masomphenya. Aphunzitsi angathe
kulemba mafunsowa pa bolodi musanayambe kuphunzitsa.
Ntchito 1: Ndondomeko zomwe
ndingatsate pokhazikitsa masomphenya anga
Mphindi 40
1. Akumbutseni ophunzira kuti mmene amayamba maphunziro a GGI anaphunzira mmene
angakhazikitsire masomphenya amoyo wawo.
2. Afunseni ophunzira kuti aganize za masomphenya omwe akufuna kuwakwaniritsa. Akhonza
kukhala masomphenya omwe anali nawo mu phunziro lachiwiri kapena osiyana omwe
awaganizira momwe amaphunzira maphunziro a GGI.
3. Mpatseni ophunzira alayense pepala. Afunseni ophunzira kuti alembe kapena kujambula
masomphenya awo kudzanja lamanja la pepala lomwe munawapatsa lija. Kumamzere
alembeko dzina lake kapena ajambule chithunzi chake.
4. PAwuzenii kuti tsopano wina aliyense ali ndi masomphenya ake, ndi nthawi yoti tikambirane
123
zina ndi zina zokhuza masomphenyawa ndi momwe tingawakwaniritsire. Awuzeni ophunzira
awone ngati pali nyanja pakati pa iwowo ndi masomphenya awo. Angafune chain kuti mange
mulatho pakati pa iwowo ndi masomphenya awowo. Aloleri kuti aganize mwakuya. Lembani
m,ayankho pa bolodi.
5. Ayamikireni ophunzira chifukwa chakuganiza mwakuya ndipo muwafunse ajambule miyala
itatu ikulu ikulu pakati pa iwowo ndi masomphenya awo.
6. Pogwiritsa ntchito zomwe ophunzira apeza ataganiza mwakuya zija, athandizeni ophunzira
kukonzekera masomphenya awo.
• Mwala woyamba: Chifukwa chani masomphenyawa ali osangalatsa kwa ine?
Ndizovuta kuti ukwaniritse masomphenya ako ngati usakusangalala nawo. Afunseni kuti
chikuwapangitsa kuti akhale ndi masomphenya amenewa ndi chani ndipo mulembe
yankholo mu mwala woyamba omwe uli pakati pa iwowo ndi masomphenya awo.
• Mwala wachiwiri: Ndani kapena ndi zinthu ziti zomwe zingawathandize uti
akwaniritse masomphenya awo? Zikhonza kukhala zophweka kuwoloka mulatho ndi
thandizo lochokera kwa abwenzi, munthu payekha, gulu kapena mabungwe. Amenewa
ndi ndani? Afunseni ophunzira kuti munthu/anthu amenewa angakhale ndani, lembani
kapena jambulani chithunzi chawo pa mwala wachiwiri omwe uli pakati pa ophunzira
ndi masomphenya awo.
• Mwala wa chitatu ndi makhwerero ati omwe ndikuyenera kukwera kuti ndikwaniritse
masomphenya anga? Zikhonza kukhala zophweka kukwaniritsa masomphenya
ako ngati uli ndi njira kapena makhwerero okwaniritsira masomphenyawo. Afunseni
ophunzira kuti alembe makhwerero amenewa pa mwal awachitatu uja omwe uli pakati
pa iwowo ndi masomphenya awo.
• Miyala yina : Pali miyala ina , yomwe yapezedwa nthawi yomwe amaganiza mwakuya
yomwenso iri yofunika kwa wina liyense payekha payekha. Awuzeni ophunzira kuti
awonjezere miyala ina yomwe angakwerepo kuti akafikire masomhenya awo. Pangani
magulu ang’ono ang’ono a anthu atatu kapena anayi ndipo muwawuze ophunzira kuti
afotokoze mapulani awo mosinthana ndi magulu ena.
7. Pangani magulu ang’ono ang’ono a anthu atatu kapena anayi ndipo muwawuze ophunzira
kuti afotokoze mapulani awo mosinthana ndi magulu ena.
Kuomba mkota
Mphindi 5
1. Muwapatse opunzira zinthu zomwe zingawathandize kukwaniritsa masomphenya awo
makamaka masomphenya okhuza kumaliza maphunziro kapena kubwerera ku sukulu.
2. Athokozeni ophunzira chifukwa chotenga nawo mbali mumaphunzilo amaluso la moyo a GGI.
124
125
Dzina
Wotsogolera:
M/F
zaka
Gired
mudzie:
1 2 3 4 5 6 7 8 9 10 11 12 13 14 15 16 17 18 19 20 21 22 23 24
Maphunziro
onse omwe
mwaphunzira
Kabweredwe (chonde ikani ‘x’ pofuna kuonetsa kuti munthu wabwera)
sukulu:
Mafomu owunikira za kabweredwe a GG
Fomu yoyamba. Kabweredwe ka ophunzira ku maphunziro a maluso a umoyo m’sukulu

Similar documents

tiyeni atsikana!

tiyeni atsikana! Kodi pali malamulo kwa achinyamata omwe ali achichepere? Malamulo ake ndi oto chani? • Palibe chilango china chilli chonse kwa mnyamata kapena mtsikana amene ali wamng’ono akapezeka ndi mowa kapen...

More information

baibulo - Akamaihd.net

baibulo - Akamaihd.net Imalimbikitsa anthu ndi uthenga wabwino wakuti Ufumu wa Mulungu posachedwapa uchotsa zoipa zonse n’kusintha dziko lapansili kukhala paradaiso. Imalimbikitsa anthu kukhulupirira Yesu Khristu yemwe a...

More information